Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 2: Kukonzekera Kubatizidwa

Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 2: Kukonzekera Kubatizidwa

 Ngati mukutsatira mfundo za m’Baibulo komanso mukuyesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu, muyenera kuti mukuganiza zobatizidwa. Koma kodi mungadziwe bwanji ngati mwakonzeka kuchita zimenezi? a

Zimene zili m’nkhaniyi

 Kodi ndiyenera kudziwa zochuluka bwanji?

 Ngati mukukonzekera kubatizidwa simuyenera kuloweza pamtima zinthu zambiri ngati mmene mungachitire pokonzekera mayeso akusukulu. Koma muyenera kugwiritsa ntchito mphamvu zanu za kuganiza kuti mudzitsimikizire zoti Baibulo limaphunzitsa mfundo zoona. (Aroma 12:1) Mwachitsanzo:

 Kodi ndiyenera kuchita zotani?

 Simuyenera kukhala munthu wangwiro kuti mubatizidwe. Komabe, muyenera kusonyeza kuti mumafunitsitsa ‘kupatuka pa zinthu zoipa ndi kuchita zabwino.’ (Salimo 34:14) Mwachitsanzo:

  •   Kodi mumatsatira mfundo za Yehova pa moyo wanu?

     Baibulo limati: “Khalani ndi chikumbumtima chabwino.”—1 Petulo 3:16.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimasonyeza bwanji kuti ndaphunzitsa “mphamvu zanga za kuzindikira kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera”?’ (Aheberi 5:14) ‘Kodi pali nthawi zina pamene ndakana kuchita zinthu zoipa zimene anzanga ankafuna? Kodi ndimasankha kucheza ndi anthu amene amandilimbikitsa kuchita zabwino?’—Miyambo 13:20.

     Kodi mukufuna thandizo? Onani nkhani yakuti “Kodi Ndingaphunzitse Bwanji Chikumbumtima Changa?

  •   Kodi mumazindikira kuti muyenera kuyankha mlandu pa zimene mumachita?

     Baibulo limati: “Aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.”—Aroma 14:12.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndine woona mtima podzifufuza komanso pochita zinthu ndi anthu ena?’ (Aheberi 13:18) ‘Kodi ndimavomereza ndikalakwitsa zinthu kapena ndimakonda kuzibisa, apo ayi kuloza chala anthu ena?’—Miyambo 28:13.

     Kodi mukufuna thandizo? Onani nkhani yakuti “Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?

  •   Kodi muli pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

     Baibulo limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikuchita zotani kuti ndilimbitse ubwenzi wanga ndi Yehova?’ Mwachitsanzo, ‘Kodi ndimawerenga Baibulo pafupipafupi?’ (Salimo 1:1, 2) ‘Kodi ndimakonda kupemphera?’ (1 Atesalonika 5:17) ‘Nanga kodi ndimanena zinthu zimene zili mumtima mwanga ndikamapemphera? Kodi anzanga ndi amene ndi anzakenso a Yehova?’—Salimo 15:1, 4.

     Kodi mukufuna thandizo? Onani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 2: Zimene Mungachite Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikusangalatsani.

 ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI: Kuti mukonzekere kubatizidwa, werengani chaputala 37 m’buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri. Makamaka, onani zimene mungalembe patsamba 308 ndi 309.

a Werengani nkhani yakuti “Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 1,” yomwe ikufotokoza tanthauzo ndiponso kufunika kwa kudzipereka kwa Mulungu komanso kubatizidwa.