Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Palibe Vuto Ngati Nditadzilemba Pathupi Langa?

Kodi Palibe Vuto Ngati Nditadzilemba Pathupi Langa?

 Kodi n’chiyani chingachititse kuti anthu azikopeka nanu?

Mnyamata wina dzina lake Ryan anati: “Zojambulajambula za pathupi zimakhala zokongola kwambiri moti anthu amene amachita zimenezi ndimawatayira kamtengo.”

Anthu amadzilemba pathupi pa zifukwa zosiyanasiyana, ndipo ena angaone kuti akuchita zimenezi pa zifukwa zabwino. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Jillian anati: “Kusukulu kwathu kunali mtsikana winawake yemwe mayi ake anamwalira. Mtsikanayo atakula, analemba dzina la mayi akewo kumbuyo kwa khosi lake. Nanenso ndimaona kuti zingakhale zosangalatsa kwambiri nditadzilemba zinthu ngati zimenezi.”

Kaya munthu akufuna kudzilemba chifukwa chiyani, aliyense ayenera kuiganizira bwinobwino nkhaniyi chifukwa akangokulemba, zimakhala zovuta kufufuta. Ndiye kodi muyenera kudzifunsa mafunso ati musanachite zimenezi? Nanga kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingakuthandizeni kuti musankhe bwino?

 Kodi muyenera kudzifunsa mafunso ati?

Kodi kudzilemba pathupi kumakhala ndi mavuto otani? Webusaiti ya chipatala china chotchedwa Mayo, inanena kuti: “Malo amene palembedwawo pamakhala timabala ndipo zimenezi zingachititse kuti munthu adwale matenda a pakhungu komanso matenda ena. Nthawi zina m’mbali mwa malo amene alembedwa mumatuluka tizilonda komanso malo omwe alembedwawo amatha kutupa.” Webusaitiyi inanenanso kuti: “Ngati anthu amene akujambula khunguwo atalemba anthu angapo pogwiritsa ntchito chipangizo chimodzi, anthuwo akhoza kutenga matenda opatsirana kudzera m’magazi.”

Kodi anthu angamaganize kuti ndine munthu wotani? Muyenera kudziwa kuti anthu angadziwe kuti ndinu munthu wotani poona mmene mukuonekera. Angadziwe ngati muli munthu wachibwana kapena ayi komanso ngati muli wokhulupirika kapena tambwali. Mtsikana wina dzina lake Samantha anati: “Ndikaona munthu amene anadzilemba pathupi lake, ndimayamba kuganiza kuti munthuyo ndi chidakwa kapena wolowerera.”

Mtsikana wina wa zaka 18, dzina lake Melanie, anati: “Ineyo ndimaona kuti kudzilemba pakhungu kumapangitsa kuti usamaoneke bwino. Anthu amene amachita zimenezi amakhala ngati akudzibisa kuti athu ena asadziwe mmene amaonekera.”

Kodi chinthu chimene atandijambulecho sindidzatopa nacho? N’kupita kwa nthawi, munthu amakula ndipo nthawi zina amanenepa. Zimenezi zingachititse kuti zimene anajambulitsa pakhungu lake zisiye kuoneka bwino. Mnyamata wina dzina lake Joseph anati: “Ndinaonapo munthu wina amene anajambulitsa pakhungu lake zaka zambiri m’mbuyomo, koma sizinkaoneka bwino mpang’ono pomwe.”

Mtsikana winanso wa zaka 21, dzina lake Allen, anati: “N’kupita kwa nthawi, zinthu zimene munajambulitsa pakhungu lanu zimafwifwa. Chinthu chimene unkachiona kuti n’chokongola kwambiri zaka zapitazo chimayamba kukunyansa.”

Zimene Allen ananenazi n’zoona. Zimene munthu angajambulitse pakhungu lake sizimasintha. Zimene zimachitika ndi zoti munthu ukamakula umasiya kukonda zinthu zimene zinkakusangalatsa poyamba. Koma pa nkhani ya zodzilembalemba pakhunguyi, zimakunyansa koma zili pakhungu lako lomwelo. Mtsikana winanso dzina lake Teresa anati: “Ndimaona kuti si bwino kuchita zinthu zomwe ungadzanong’oneze nazo bondo mtsogolo, n’chifukwa chake sindimafuna kujambulitsa zinazake pakhungu langa.”

 Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni pa nkhani imeneyi?

Munthu wozindikira amayamba waganiza kaye asanasankhe zochita. (Miyambo 21:5; Aheberi 5:14) Taonani mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zomwe zingatithandize kudziwa chochita pa nkhani yojambulitsa zinthu pakhungu.

  • Akolose 3:20: “Ananu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye.”

    Kodi makolo anu angasangalale atadziwa kuti mwalephera kumvera zimene anakuuzani pa nkhani imeneyi?

  • 1 Petulo 3:3, 4: “Ndipo kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwakunja, monga kumanga tsitsi, kuvala zodzikongoletsera zagolide, kapena kuvala malaya ovala pamwamba. Koma kukhale kwa munthu wobisika wamumtima, atavala zovala zosawonongeka, ndizo mzimu wabata ndi wofatsa.”

    Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti tiyenera kukongoletsa “munthu wobisika wamumtima”?

  • 1 Timoteyo 2:9: “Akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu ndi mwanzeru.”

    Kodi chofunika kwambiri n’chiyani pakati pa kukhala ndi khalidwe labwino komanso kukongola?

  • Aroma 12:1: “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza.”

    Kodi Mulungu angamve bwanji ngati mutadzijambula pathupi lanu?

Anthu ena ataganizira mfundo zimene takambiranazi, anaona kuti si bwino kuti ajambulitse zinthu pakhungu lawo. Iwo amaona kuti ndi bwino kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kutsatira zimene amakhulupirira. Teresa amene tamutchula kale uja anati: “Ndikuona kuti ngati munthu ali ndi mawu enaake amene amamusangalatsa kwambiri, angachite bwino kumangogwiritsa ntchito mawuwo. Komanso ngati pali munthu amene umamukonda kwambiri, ndi bwino kungomuuza kuti umamukonda m’malo molemba dzina lake pakhungu lako.”