Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndisiye Sukulu?

Kodi Ndisiye Sukulu?

 “Ndimadana ndi sukulu.” Ngati mumamva chonchi, mwina mungafune kuisiya. Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zimene zingakuthandizeni pa nkhaniyi.

 Chifukwa chake anthu ena amasiya sukulu

 Zifukwa zimene aphunzitsi amapereka ndi izi:

  •   Kusakhoza bwino. ‘Ndimangolephera kusukulu.’

  •   Mphwayi. ‘Ndikuona kuti zimene ndikuphunzira n’zosathandiza.

  •   Umphawi. Ndimafunika kugwira ntchito kuti ndizithandiza banja lathu.

 Ganizirani zotsatirapo zake

 Baibulo limati: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ngati mukuganiza zosiya sukulu, muyenera kuganizira zotsatirapo zake.

 Dzifunseni kuti:

  •   ‘Ndikasiya sukulu, kodi ndidzatha kupeza ntchito mosavuta m’tsogolo?’

     “Uziganizira za kupeza ntchito komanso mwina kusamalira banja lako m’tsogolo. Kodi udzachita bwanji zimenezi ngati mabwana ambiri amafuna kulemba ntchito anthu amene amaliza sukulu?​—Julia.

  •   ‘Ndikasiya sukulu, kodi ndidzatha kuthana ndi mavuto amene ndingadzakumane nawo m’tsogolo?’

     “Sukulu imathandiza munthu kukonzekera zimene angadzakumane nazo pa moyo. Zinthu zimene ungadzakumane nazo zidzakhala zofanana ndi zimene unakumana nazo kusukulu, kaya ndi anthu amene ungadzakumane nawo, mayesero kapena ntchito imene uzidzagwira.”​—Daniel.

  •   ‘Ndikasiya sukulu, kodi ndidzakhala ndi maluso amene ndingadzafunike m’tsogolo?’

     “Panopa ungaganize kuti maphunziro akusukulu ndi osathandiza koma ukadzakhala ndi zaka 23 ndipo ukupanga bajeti, udzaganiza kuti, ‘Ndinkachita bwino kukonda masamu.’”​—Anna.

 Zimene zingathandize

  •   Pemphani ena akuthandizeni. Baibulo limati: “Pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.” (Miyambo 11:14) Ngati simukukhoza bwino kusukulu, mupemphe makolo, aphunzitsi, alangizi akusukulu kapena wachikulire wina wodalirika kuti azikuthandizani.

     “Uziuzako aphunzitsi ako ngati zikukuvuta. Nthawi zina, ungaganize kuti vuto ndi aphunzitsi, koma nthawi zambiri ukapempha kuti azikuthandiza umayamba kuchita bwino.”​—Edward.

  •   Ganizirani phindu lake. Baibulo limati: “Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake.” (Mlaliki 7:8) Mukamaliza sukulu, mudzakhala mutaphunzira zambiri monga makhalidwe abwino komanso maluso, osati maphunziro anu okha.

     “Mwina sudzafunika kulemba nkhani kapena kukonzekera mayeso ukadzakula. Koma mmene umachitira zinthu ukapanikizika kusukulu zimakuthandiza kukonzekera mavuto amene udzakumane nawo ukadzamaliza sukulu.”​—Vera.

    Kusiya sukulu kuli ngati kutsika boti lisanafike padoko. Mukhoza kudandaula kuti mwatsika mofulumira.

  •   Ganizirani zina zimene mungachite. Baibulo limati “Wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miyambo 21:5) Musafulumire kuganiza kuti kusiya sukulu ndi chinthu chokhacho chimene mungachite. Mwina mungamalize sukulu kunyumba pogwiritsa ntchito intaneti kapena njira ina.

     “Kusukulu umaphunzira kugwira ntchito mwakhama, kuthetsa mavuto komanso kugwirizana ndi anthu ena. Zinthuzi zidzakuthandizani moyo wanu wonse. Ndi bwino kuyesetsa kumaliza sukulu.”​—Benjamin.

 Mfundo yofunika kwambiri: Mukamaliza sukulu mudzakhala wokonzeka kusamalira maudindo amene munthu wamkulu amakhala nawo.