Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndiyenera Kuchita Chiyani Ndikabatizidwa?—Mbali Yoyamba: Pitirizani Kuchita Zinthu Zofunika

Kodi Ndiyenera Kuchita Chiyani Ndikabatizidwa?—Mbali Yoyamba: Pitirizani Kuchita Zinthu Zofunika

 Zinthu zamtengo wapatali monga nyumba kapena galimoto, zimafunika kuzisamalira bwino. Zimenezi ndi zofanananso ndi ubwenzi wathu ndi Mulungu. Kodi mungatani kuti ubwenzi wanu ndi Mulungu ukhalebe wolimba pambuyo poti mwabatizidwa?

Zimene zili munkhaniyi

 Pitirizani kuphunzira Mawu a Mulungu

 Lemba logwirizana ndi mfundoyi: ‘Pitirizani kubala zipatso m’ntchito iliyonse yabwino, ndi kuwonjezera kumudziwa Mulungu molondola.’—Akolose 1:10.

 Zomwe tikuphunzirapo: Pambuyo poti mwabatizidwa, muyenera kupitiriza kuwerenga Baibulo ndi kuganizira mozama zomwe mwawerenga.—Salimo 25:4; 119:97.

 Zomwe zingachitike: Nthawi zina mungagwe ulesi kuti muwerenge Baibulo. Mwinanso mukhoza kunena kuti “ine zowerengazi n’kumanzere.”

 Zomwe mungachite: Muziphunzira mozama nkhani za m’Baibulo zomwe zimakuchititsani chidwi. Muyenera kukonza pulogalamu yophunzirira yomwe simungavutike kuitsatira. Mukakhala ndi khama, mudzayamba kusangalala ndi kuwerenga Mawu a Mulungu ndipo chikondi chanu pa Yehova chidzakula. Kukhala ndi pulogalamu yophunzirira, kudzakuthandizani kuti mupindule komanso mudzakhala osangalala.—Salimo 16:11.

 Zimene zingakuthandizeni: Kuti muzipindula mokwanira mukafuna kuphunzira, muzipeza malo aphee, opanda zosokoneza zilizonse.

 Zinthu zina zomwe zingakuthandizeni

 Pitirizani kupemphera kwa Yehova

 Lemba logwirizana ndi mfundoyi: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.

 Zomwe tikuphunzirapo: Muzilankhulana ndi Mulungu. Mukamawerenga Mawu ake, mumakhala kuti mukumumvetsera. Ndipo inunso mukamapemphera, mumakhala kuti mukumuuza maganizo anu. Dziwani kuti mukamapemphera, mumakhala ndi mwayi wopempha zomwe mukufuna kapenanso wothokoza chifukwa cha madalitso amene wakupatsani.

 Zomwe zingachitike: Nthawi zina mungaone kuti mapemphero anu akumangokhala obwerezabwereza. Mwinanso mungayambe kukayikira ngati Yehova amamvetseradi mapemphero anu.—Salimo 10:1.

 Zomwe mungachite: Tsiku lililonse muziganira zomwe munganene popemphera. Ngati simungapeze mpata wopereka pemphero lotalikirapo, ganizirani nthawi ina tsikulo lisanathe kuti mupempherere nkhaniyo. Kuwonjezera pa kupempherera zinthu zomwe ndi zofunika kwa inu, muzipemphereranso zomwe ena akufunikira.—Afilipi 2:4.

 Zimene zingakuthandizeni: Mukaona kuti mapemphero anu akungomveka obwerezabwereza, mungapemphere n’kumuuza Yehova zimenezo. Iye amafuna kuti muzimuuza chilichonse, kuphatikizapo mmene mukumvera ndi mapemphero omwe mumapereka.—1 Yohane 5:14.

 Zinthu zina zomwe zingakuthandizeni

Pitirizani kuuza anthu ena zomwe mumakhulupirira

 Lemba logwirizana ndi mfundoyi: “Uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa. . . . Chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.”—1 Timoteyo 4:16.

  Zomwe tikuphunzirapo: Mukamauza ena zomwe mumakhulupirira, chikhulupiriro chanu chimalimba. Ndipo ubwino wake ndi wakuti mukatero mumakhala ndi chiyembekezo chodzapulumuka komanso mumathandiza anthu okumverani kuti nawonso adzapulumuke.

 Zomwe zingachitike: Nthawi zina mungamangike kuuza ena zomwe mumakhulupirira. Mwina mungamachite mantha kulalikira makamaka mukakhala kusukulu.

 Zomwe mungachite: Musamalephere kuchita zinazake chifukwa cha mantha. Mtumwi Paulo analemba kuti “Ndikachita motsutsana ndi kufuna kwanga, sindingachitire mwina, ndinebe woyang’anira mogwirizana ndi udindo umene unaikidwa m’manja mwanga.”—1 Akorinto 9:16, 17.

 Zimene zingakuthandizeni: Mupemphe makolo anu kuti akuloleni kupeza Mkhristu wina, amene ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yolalikira, kuti azikuthandizani.—Miyambo 27:17.

 Zinthu zina zomwe zingakuthandizeni

Pitirizani kupezeka pamisonkhano yachikhristu

 Lemba logwirizana ndi mfundoyi: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.”—Aheberi 10:24, 25.

  Zomwe tikuphunzirapo: Timapita kumisonkhano ndi cholinga choti tikalambire Yehova. Koma pali zinthu zinanso ziwiri zomwe timapindula tikapita kumisonkhano. Choyamba, timakalimbikitsidwa ndi Akhristu anzathu. Ndipo chachiwiri, ifenso timakhala ndi mwayi wolimbikitsa ena chifukwa chopezekapo komanso tikakhala ndi zochita kapena kupereka ndemanga.—Aroma 1:11, 12.

 Zomwe zingachitike: Nthawi zina ukakhala pamisonkhano ukhoza kuphonya mfundo zofunika chifukwa choganizira zinthu zina. Mwinanso ungapezeke kuti sukumapezekapezeka pamisonkhano chifukwa chotanganidwa ndi zochita za kusukulu kapena zinthu zina.

 Zomwe Mungachite: Popanda kunyalanyaza zochita za kusukulu, muziyesetsa kupezeka pamisonkhano nthawi zonse ndipo muzikhala ndi cholinga choti muzipindula mokwanira. Muziyesetsa kuimika dzanja kuti mupereke ndemanga. Misonkhano ikatha, muziyesetsa kuyamikirako winawake chifukwa cha ndemanga yomwe anapereka kapena chifukwa cha mmene wakambira nkhani yake.

 Zimene zingakuthandizeni: Muzikonzekera musanapite kumisonkhano. Pangani dawunilodi apu ya JW Library® ndipo muzitsegula pa “Meetings” kuti mudziwe nkhani zomwe zikakambidwe pamisonkhano.

 Zinthu zina zomwe zingakuthandizeni