Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 3: Zimene Mungachite Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikuthandizani Kwambiri

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 3: Zimene Mungachite Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikuthandizani Kwambiri

 Mukatsegula Baibulo mudzaona kuti lili ndi mawu ambirimbiri. Zimenezitu zisamakuchititseni mantha n’kumaopa kuliwerenga. M’malomwake, muziliona ngati tebulo lomwe lili ndi zakudya zambirimbiri zomwe simungakwanitse kudya zonse pa nthawi imodzi koma mungasankhe kudya zokhazo zomwe mungazikwanitse pa nthawiyo.

 Kuti Baibulo lizikuthandizani kwambiri mukamaliwerenga, muziika maganizo anu onse pa zomwe mukuwerengazo. Nkhaniyi, ikuthandizani kuti muzichita zimenezi.

Nkhaniyi ikufotokoza

 Chifukwa chake muyenera kuika maganizo anu onse pa zomwe mukuwerenga m’Baibulo

 Mukamawerenga Baibulo mwakhama nthawi zonse, m’pamene mumapindula kwambiri. Taganizirani chitsanzo chotsatirachi: Mukaika masamba a tiyi m’madzi otentha kwa nthawi yochepa, kakomedwe kake kangakhale kosiyana ngati mutadikira kaye kuti masambawo akhaleko kwa kanthawi m’madzi otenthawo chifukwa tiyi wake angakhale wokoma kwambiri.

 N’chimodzimodzinso ndi kuwerenga Baibulo. M’malo mongowerenga mofulumira n’cholinga choti mumalize, muzipeza nthawi yoganizira zomwe mukuwerengazo. Zimenezi ndi zomwe munthu amene analemba Salimo 119 ankachita. Iye ananena kuti: “Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.”​—Salimo 119:97.

 N’zoona kuti simuchita kufunika tsiku lonse lathunthu kuti muzingowerenga komanso kuganizira za Baibulo basi. Koma mfundo ndi yakuti munthu amene analemba salimoyu ankapeza nthawi yoganizira Mawu a Mulungu. Zimenezi zinamuthandiza kuti azisankha zochita mwanzeru.​—Salimo 119:98-100.

 “Mayi anga anandiuza kuti, ‘Umakhala ndi masiku 7 pa mlungu ndipo pa masiku amenewa umakhala ndi zinthu zako zambiri zoti uchite. Kodi sungapezeko nthawi yoti uzimupatsa Yehova? Zimenezitu ndi zabwino.’”​—Melanie.

 Kuganizira mfundo za m’Baibulo kudzakuthandizani kuti muzisankha zinthu mwanzeru. Mwachitsanzo, mukamasankha anthu oti muzicheza nawo kapena mukamayesedwa kuti muchite zinthu zoipa.

 Zomwe mungachite kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo

  •   Muzikhala ndi cholinga. Mtsikana wina dzina lake Julia, ananena kuti: “Mumafunika kukonza ndandanda yowerengera Baibulo, kudziwa zomwe mukufuna kuwerenga, nthawi yoti muwerengere komanso malo amene mukufuna kuwerengera.”

  •   Muzipeza malo opanda zosokoneza. Mtsikana wina dzina lake Gianna, ananena kuti: “Muzipeza malo opanda phokoso komanso muziuza anthu a m’banja lanu za ndandanda yanu yowerengera Baibulo kuti asamakusokonezeni pamene mukuwerenga.”

     Ngati mukugwiritsa ntchito foni kapena chipangizo china, muzitchera kuti pasamabwere mauthenga omwe angakusokonezeni. Mukhozanso kumawerenga Baibulo lopulinta. Kafukufuku amasonyeza kuti kuwerenga buku lochita kupulinta kumathandiza kuti uzimva mosavuta zimene ukuwerengazo. Koma zimakhala zovuta kuti maganizo ako azikhala pa zimene ukuwerengazo ngati ukugwiritsa ntchito chipangizo chamakono.

     “Ndimaona kuti kuwerengera pafoni kumakhala kosokoneza. Foni yanga imabweretsa mauthenga kapena batire limatha moto kapenanso intaneti imavuta. Pamene kugwiritsa ntchito buku lopulinta kulibe mavuto amenewa koma ndimangofunika kuti pamalo omwe ndikuwerengerapo paziwala mokwanira.”​—Elena.

  •   Muziyamba ndi pemphero. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa, kukumbukira komanso kuti mfundo zimene mukufuna kuwerenga m’Baibulo zikuthandizeni pa moyo wanu.​—Yakobo 1:5.

     Kuti muzichita zinthu zogwirizana ndi pemphero lanu, muzifufuza mozama zomwe mukuwerengazo. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Ngati mukugwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Library kapena mukuwerenga Baibulo la pa intaneti, mungadine pavesilo kuti mupeze mfundo zina zowonjezera komanso nkhani zokhudza vesilo.

  •   Muzidzifunsa mafunso. Mwachitsanzo: ‘Kodi ndikuphunzira chiyani zokhudza Yehova pa nkhani imene ndikuwerengayi? Kodi nkhaniyi ikusonyeza khalidwe liti la Yehova limene ndingatsanzire?’ (Aefeso 5:1) ‘Kodi ndi zinthu ziti zimene ndikuphunzira munkhaniyi zimene ndingazigwiritse ntchito pa moyo wanga?’ (Salimo 119:105) ‘Kodi zimene ndikuwerengazi ndingazigwiritse ntchito pothandiza ena m’njira ziti?’​—Aroma 1:11.

     Muzidzifunsanso kuti: ‘Kodi zimene ndawerengazi zikugwirizana bwanji ndi mfundo yaikulu ya m’Baibulo?’ Funso limeneli ndi lofunika kwambiri. N’chifukwa chiyani? N’chifukwa chakuti zonse zimene timawerenga m’Baibulo kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso n’zogwirizana mwa njira inayake ndi mfundo yaikulu ya m’Baibulo, yofotokoza zimene Yehova adzachite pofuna kuyeretsa dzina lake pogwiritsa ntchito Ufumu wakumwamba komanso kutsimikizira kuti iyeyo ndi woyenera kulamulira komanso amalamulira m’njira yabwino kwambiri.