Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndingachite Chiyani Ngati Makolo Anga Akufuna Kuthetsa Banja Lawo?

Kodi Ndingachite Chiyani Ngati Makolo Anga Akufuna Kuthetsa Banja Lawo?

Zimene mungachite

 Fotokozani za kukhosi kwanu. Uzani makolo anu kuti zochita zawozo zikukukhumudwitsani komanso kukusokonezani maganizo. Mwina iwo angakuuzeni zimene zikuchitika ndipo nkhawa yanu ingachepe.

 Komabe, ngati makolo anuwo sakukuthandizani, mungauze munthu wina wamkulu amene mumamukhulupirira.—Miyambo 17:17.

 Komanso Atate wanu wakumwamba, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” ndi wokonzeka kumvetsera mavuto anu. (Salimo 65:2) Muuzeni nkhawa zanu zonse “pakuti amakuderani nkhawa.”—1 Petulo 5:7.

Zimene simuyenera kuchita

Kupirira mavuto amene mumakumana nawo makolo anu akathetsa banja lawo kuli ngati kupirira ndi ululu mukathyoka mkono. Mumamva kupweteka kwambiri komabe pakapita nthawi mumachira

 Musawasungire chakukhosi. Daniel, yemwe makolo ake anathetsa banja lawo iye ali ndi zaka 7 zokha, anati: “Zimene makolo anga anachitazo zinasonyeza kuti anali odzikonda. Sanaganizire n’komwe za ana awofe ndiponso kuti zitikhudza bwanji.”

 Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chikanachitikira Daniel ngati akanapitirizabe kukhala wokwiya komanso kusungira chakukhosi makolo akewo?—Kuti mudziwe: Werengani Miyambo 29:22.

 N’chifukwa chiyani Daniel akanachita bwino kungokhululukira makolo akewo ngakhale kuti anamukhumudwitsa kwambiri?—Kuti mudziwe: Werengani Aefeso 4:31, 32.

 Pewani makhalidwe amene angakubweretsereni mavuto. Mnyamata wina dzina lake Denny anati: “Makolo anga atathetsa ukwati wawo, ndinavutika kwambiri maganizo ndipo sindinkasangalala. Kenako zinthu zinayamba kundivuta kwambiri kusukulu moti chaka china ndinalephera mayeso. Patapita nthawi . . . ndinakhala mwana wovuta kwambiri m’kalasi monse, moti ndinkangokhalira kukangana ndiponso kumenyana ndi ana a sukulu anzanga.”

 Kodi mukuganiza kuti pali chilichonse chaphindu chimene Denny ankapeza povutitsa m’kalasi ndiponso kumenyana ndi anzake?

 Kodi mfundo yopezeka pa Agalatiya 6:7 ingathandize bwanji anthu ngati Denny kuti apewe makhalidwe amene angawabweretsere mavuto?

 N’zoona kuti pangatenge nthawi yaitali kuti muiwale mavuto amene mungakumane nawo chifukwa cha kutha kwa banja la makolo anu. Komabe n’kupita kwa nthawi, mungakwanitse kupirira mavuto amenewa ndipo mungayambe kuona kuti zinthu zayambanso kukuyenderani bwino pa moyo wanu.