Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kukhala Moyo Wachiphamaso?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kukhala Moyo Wachiphamaso?

 Nthawi zina, atumiki ena a Yehova amaganiza kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo n’kutaya nthawi komanso n’kotopetsa. (Salimo 73:2, 3) Mwina angayambe kuyeserera kuchita makhalidwe osemphana ndi malamulo a Yehova ndipo kenako angayambe kuchita zinthu zoipa mobisa.

 Nkhaniyi yalembedwa n’cholinga chothandiza anthu amene ayamba kuchita zimenezi koma akufunitsitsa kusiya kukhala moyo wachiphamaso.

Munkhaniyi muli izi:

 Kodi moyo wachiphamaso n’chiyani?

 Kukhala moyo wachiphamaso ndi pamene uli ndi anzako omwe samvera Yehova ndipo ukuchita nawo zinthu zimene ukudziwa kuti n’zoipa, kwinaku ukuchita zinthu mokhulupirika ndi anzako akumpingo, n’kumachita zinthu zosonyeza ngati kuti ukufuna kutumikira Yehova. Zimakhala kuti ukubisa umunthu wako n’kumachita zinthu ziwiri zosiyana.

 “Ukamakhala moyo wachiphamaso zimakhala kuti ukudzibisa mmene ulili. Zotsatirapo zake n’zakuti umakhala munthu wachinyengo.”​—Erin.

 Kodi mukudziwa? Moyo wachiphamaso umaphatikizapo kuchita mobisa zinthu zomwe ukudziwa kuti Yehova sasangalala nazo.

 “Ndili zaka 14, ndinayamba kuona zithunzi ndi mavidiyo olaula pa intaneti. Ndikakhala ndi anzanga ndinkachita zinthu ngati kuti ndimadana ndi zolaula koma mumtima mwanga ndinkadziwa ndithu kuti si zili choncho.”​—Nolan.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo.”​—Mateyu 6:24.

 Kodi kukhala moyo wachiphamaso kungandichititse kuti ndikhale munthu woipa?

 Osati kwenikweni. N’zoona kuti anthu ena anasankha kuti asamayendere mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo. Koma kodi inunso munasankha choncho? Kapena pali zinthu zina zomwe zikukuchititsani kuchita zimenezo, monga:

  •   Kuchita mantha mukamachita zinthu zosiyana ndi zimene anzanu akuchita.

  •   Kuganiza kuti pali zinthu zambiri zimene mumachita zofanana ndi anzanu akusukulu kuposa akumpingo.

  •   Kuganiza kuti simungakwanitse kutsatira malamulo onse a Mulungu.

 “Ndikuganiza kuti achinyamata ena omwe amakhala moyo wachiphamaso amamasuka kwambiri ndi anthu omwe satsatira mfundo za Chikhristu chifukwa amaona kuti akufunikira kukhala ndi anzawo ambiri ndipo saona vuto lililonse.”​—David.

 Komabe, sikuti zimenezi zikutanthauza kuti muli ndi zifukwa zomveka zoti muzikhala moyo wachiphamaso. Koma zikutithandiza kudziwa kuti ngakhale anthu amene mumawaona kuti ndi abwino akhoza kukodwa mumsampha umenewu. Mungatani ngati zimenezi zitakuchitikirani?

 Ndingatani kuti ndisiye kukhala moyo wachiphamaso?

  1.  1. Ganizirani mmene mumachitira zinthu pa moyo wanu. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikufuna kumakhaladi moyo umenewu? Ngati nditapitiriza kukhala moyo umenewu, kodi zotsatirapo zake zingakhale zotani?’

     Mfundo ya m’Baibulo: ‘Wochenjera amaona tsoka . . . , koma anthu osadziwa zinthu amene amangopitabe amalangidwa.’​—Miyambo 27:12.

  2.  2. Muzikhala oona mtima. Muzikambirana ndi makolo anu kapena munthu wina wolimba mwauzimu yemwe amalemekeza malamulo a Yehova. Iwo adzasangalala kwambiri kudziwa kuti munawapempha kuti akuthandizeni komanso kuti mwachita zinthu zoyenera.

    Ngati mwazindikira kuti mwayamba kukhala moyo wachiphamaso, pemphani thandizo

     “Zinali zovuta kwambiri kuvomereza zomwe ndinalakwitsa kwa anthu ena. Koma nditatero ndinamva bwino kwambiri.”​—Nolan.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.”​—Miyambo 28:13.

  3.  3. Muzivomereza zotsatirapo zake. Kumbukirani kuti ngati mwakhala mukubisira makolo anu komanso mpingo zinazake, zimakhala zovuta kwambiri kuti azikukhulupirirani. Zotsatirapo zake n’zakuti makolo anu kapena akulu mumpingo angakuletseni kuchita zinthu zina kwa kanthawi. Muzivomereza zimenezi ndipo muziyesetsa “kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Mvera uphungu ndipo utsatire malangizo kuti udzakhale wanzeru m’tsogolo.”​—Miyambo 19:20.

  4.  4. Muzikhulupirira kwambiri kuti Mulungu amakukondani. Yehova amadziwa zonse zimene timachita chifukwa chakuti amatikonda. Ndiye ngati mumakhala moyo wachiphamaso, amadziwa zimenezo ndipo zimamukhumudwitsa. Komabe, iye ndi wofunitsitsa kukuthandizani kuti muzichita zabwino, ‘chifukwa amakuderani nkhawa.’​—1 Petulo 5:7.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”​—2 Mbiri 16:9.