Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamasinthesinthe Mmene Ndimamvera?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamasinthesinthe Mmene Ndimamvera?

“Tsiku lina ndimatha kukhala bwinobwino koma tsiku lotsatira ndimapezeka kuti sizikundiyendera. Zinthu zimene dzulo ndinaziona ngati zazing’ono lero ndimayamba kuziona ngati zovuta.”​—Carissa.

Kodi maganizo anunso amatha kusinthasintha ngati msewu wazigwembe? a Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani kwambiri!

 Chifukwa chake zimachitika

Ana ambiri akamakula amakhala ndi vuto losinthasintha mmene akumvera ndipo zimenezi zimachitika pamene thupi lawonso likusintha. Komabe ngakhale munthu atakula n’kukhala wachinyamata nthawi zina amadabwa kuti zimenezi zimamuchitikirabe.

Ngati nanunso zimenezi zimakuchitikirani, muzikumbukira kuti munthu ukamakula mahomoni amasinthasintha komanso pa nthawiyi umakhala ndi mantha enaake ndiponso umaona ngati ndiwe wosatetezeka. Koma chosangalatsa n’choti mungathe kudziwa bwino chifukwa chake zimenezi zikuchitika komanso mungathe kupirira vutoli.

Mfundo yothandiza: Kudziwa zoyenera kuchita mukayamba kusinthasintha mmene mukumvera kungadzakuthandizeni kwambiri kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana mukadzakula.

Maganizo olakwika amangofanana ndi zigwembe zamumsewu. Munthu waluso amayesetsa kuzemba zigwembe n’kutha kuyenda bwinobwino

 Zinthu zitatu zimene mungachite

Muziyankhula. Baibulo limati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

“Tili ndi anzathu ena amene ndimangowatenga ngati mayi anga aan’gono. Ndikamawafotokozera zinthu amandimvetsera ndipo ndimamasuka nawo. Ndikanena mfundo inayake yabwino amandiyamikira ndipo ndikalakwitsa amandilangiza mwachikondi.”​—Yolanda.

Zimene zingakuthandizeni: M’malo momangokambirana zokhudza vuto lanulo ndi achinyamata anzanu, muzikambirana ndi makolo anu kapena munthu wina wachikulire amene mumamukhulupirira.

Muzilemba. Baibulo limanena zomwe Yobu ananena pa nthawi imene anali ndi nkhawa kwambiri. Iye anati: “Ndilankhula mwamphamvu za nkhawa zanga. Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.” (Yobu 10:1) Kuwonjezera pa kuuzako munthu wina, kulemba mmene mukumvera ndi njira inanso ‘yolankhulira.’

“Ndimatenga kabuku kulikonse kumene ndikupita. Chinachake chikandikhumudwitsa, ndimalemba. Kulemba zimene zandikhumudwitsa kumandithandiza kuti ndiyambe kumva bwino.”​—Iliana.

Zimene zingakuthandizeni: Muzisunga kabuku koti muzilembamo mmene mukumvera, zomwe zachititsa kuti muzimva choncho, komanso zimene mungachite kuti muthetse vutolo. Tsamba la zoti muchite lomwe lili m’nkhaniyi likuthandizani kuchita zimenezi.

Muzipemphera. Baibulo limati: “Umutulire Yehova nkhawa zako, Ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.”—Salimo 55:22.

“Ndikakhala ndi nkhawa ndimapemphera kwa Yehova pafupipafupi. Ndipo ndikangomuuza nkhawa zanga, nthawi zonse ndimamva kupepuka mumtimamu.”​—Jasmine.

Zimene zingakuthandizeni: M’malo mongoganizira zinthu zomwe zikukudetsani nkhawa, ganizirani zinthu zabwino zitatu zimene mukusangalala nazo. Mukamapemphera kwa Yehova muzimupempha kuti akuthandizeni komanso musamaiwale kumuthokoza chifukwa cha zinthu zabwino zimene wakhala akukuchitirani.

a Nkhaniyi ikufotokoza mavuto a kusinthasintha mmene munthu amamvera ndipo zimenezi zimachitikira achinyamata ambiri. Ngati muli ndi matenda ovutika maganizo a mtundu wina uliwonse, onani nkhani ya mutu wakuti “Kodi Ndingatani Ngati Ndili ndi Matenda Ovutika Maganizo?”