Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 1: Tanthauzo la Kubatizidwa

Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 1: Tanthauzo la Kubatizidwa

 Chaka chilichonse, achinyamata ambiri amene akukulira m’banja la Mboni za Yehova amabatizidwa. Kodi inuyo mukuganizira zobatizidwa? Ngati zili choncho, poyamba muyenera kumvetsa tanthauzo la kudzipereka kwa Mulungu komanso kubatizidwa.

 Kodi kubatizidwa kumatanthauza chiyani?

 Mawu oti kubatizidwa omwe amapezeka m’Baibulo amatanthauza kumizidwa thupi lonse m’madzi osati kungowazidwa ndi madzi basi. Mawuwa amakhalanso ndi tanthauzo lophiphiritsa.

  •   Kumizidwa m’madzi mukabatizidwa kumasonyeza kuti mwasiya kumangochita zimene zimakusangalatsani inuyo.

  •   Kutulutsidwa m’madzi kumasonyeza kuti mwayamba moyo watsopano wochita zimene zimasangalatsa Mulungu.

 Mukabatizidwa mumasonyeza pa gulu kuti Yehova ali ndi ulamuliro wosankha zoyenera ndi zosayenera komanso kuti mwalonjeza kuchita zimene iye amafuna.

 Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani mungafune kusonyeza pa gulu kuti mwalonjeza kumvera Yehova? Onani 1 Yohane 4:19 ndi Chivumbulutso 4:11.

 Kodi kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza chiyani?

 Musanabatizidwe muyenera kudzipereka kwa Yehova muli nokha. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

 Muyenera kupemphera kwa Yehova muli nokha n’kumamuuza kuti mwalonjeza kudzamutumikira mpaka kalekale. Muyenera kumuuzanso kuti muzidzachita zimene iye amafuna zivute zitani mosatengera zimene anthu ena angasankhe kuchita.

 Mukabatizidwa mumasonyeza pa gulu zimene munachita panokha podzipereka kwa Mulungu. Mumasonyeza kwa anthu ena kuti mwasankha kuchita zimene Yehova amafuna m’malo mochita zofuna zanu.—Mateyu 16:24.

 Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani moyo wanu umakhala wabwino kwambiri mukayamba kuchita zimene Yehova amafuna? Onani Yesaya 48:17, 18 ndi Aheberi 11:6.

 N’chifukwa chiyani kubatizidwa n’kofunika?

 Yesu ananena kuti ophunzira ake ayenera kubatizidwa. (Mateyu 28:19, 20) Choncho masiku anonso, Akhristu ayenera kubatizidwa. Baibulo limanena kuti munthu ayenera kubatizidwa kuti adzapulumuke.—1 Petulo 3:21.

 Koma muyenera kubatizidwa chifukwa chokonda Yehova ndi kuyamikira zimene iye amachita. Muyenera kukhala ndi mtima umene wolemba masalimo unali nawo polemba kuti: “Yehova ndidzamubwezera chiyani pa zabwino zonse zimene wandichitira? . . . Ndidzaitana pa dzina la Yehova. Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova.”—Salimo 116:12-14.

 Zoti muganizire: Kodi Yehova wakuchitirani zinthu zotani, nanga mungamubwezere bwanji? Onani Deuteronomo 10:12, 13 ndi Aroma 12:1.