Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Kugonana Kwa Amuna Kapena Akazi Okhaokha N’kolakwika?

Kodi Kugonana Kwa Amuna Kapena Akazi Okhaokha N’kolakwika?

David amene ali ndi zaka 23, ananena kuti: “Pamene ndinkakula, ndinkalimbana ndi vuto lokopeka ndi amuna anzanga. Ndinkaona kuti mwina zidzasintha ndikadzakula koma ndikulimbanabe ndi vutoli mpaka pano.”

David ndi Mkhristu amene amafuna kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu. Koma kodi angathedi kusangalatsa Mulungu kwinaku ali ndi chilakolako chofuna amuna anzake? Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona anthu omwe amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo?

 Kodi Baibulo limanena zotani?

Maganizo a anthu amasiyanasiyana pa nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, mogwirizana ndi chikhalidwe kapena mayiko ochokera. Komanso mmene achikulire ndi achinyamata amaonera nkhaniyi, zimasiyananso. Akhristu satsatira zinthu zinazake chifukwa chakuti anthu ambiri akuganiza choncho kapena ‘kutengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso.’ (Aefeso 4:14) Koma amaona nkhani iliyonse ngakhale nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.

Baibulo limafotokoza momveka bwino za khalidwe limeneli. Limati:

  • “Usagone ndi mwamuna mmene umagonera ndi mkazi.”​—Levitiko 18:22.

  • “Malinga ndi zilakolako za m’mitima mwawo, . . . Mulungu anawasiya kuti atsatire zilakolako zamanyazi za kugonana, popeza akazi pakati pawo anasiya njira yachibadwa ya matupi awo n’kumachita zosemphana ndi chibadwa.”​—Aroma 1:24, 26.

  • “Musasocheretsedwe. Adama, opembedza mafano, achigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo, akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”​—1 Akorinto 6:9, 10.

Mfundo zimene Mulungu anaperekazi, n’zofunika kwa munthu aliyense. Kaya munthu wina amagonana ndi mwamuna kapena mkazi mnzake, kapena amagonana ndi munthu woti si mwamuna kapena mkazi mnzake, amayenera kutsatira mfundozi. Mfundo ndi yakuti, aliyense amafunika kukhala wodziletsa kuti asamakopeke ndi chilakolako chofuna kuchita zinthu zomwe Mulungu amadana nazo.​—Akolose 3:5.

 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti . . . ?

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Baibulo limalimbikitsa zodana ndi anthu omwe amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo?

Ayi. Baibulo sililimbikitsa zodana ndi aliyense kaya munthuyo amagonana ndi amuna kapena akazi anzake kapena ayi. Koma limatilimbikitsa “kukhala pa mtendere ndi anthu onse” kaya anthuwo akhale ndi khalidwe lotani. (Aheberi 12:14) Choncho sibwino kumenya, kunyoza kapena kuchitira nkhanza anthu omwe amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Akhristu azitsutsa malamulo omwe amavomereza ukwati wa amuna kapena akazi okhaokha?

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anakonza zoti ukwati uzikhala wa mwamuna m’modzi ndi mkazi m’modzi. (Mateyu 19:4-6) Komabe kukambirana za malamulo aboma pa nkhani yonena za ukwati wa amuna kapena akazi okhaokha, kumagwirizana ndi nkhani za ndale osati kulimbikitsa makhalidwe abwino. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti asamalowerere nawo nkhani za ndale. (Yohane 18:36) Choncho Akhristuwa, salimbikitsa kapena kutsutsa malamulo aboma omwe amanena za ukwati kapena za kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.

 Koma bwanji ngati . . . ?

Koma bwanji ngati munthu wina amagonana ndi mwamuna kapena mkazi mnzake, kodi munthu wotereyu angasinthe?

Inde. Anthu ena m’nthawi ya atumwi ankachitanso zomwezo. Baibulo litafotokoza zakuti amuna [kapena akazi] amene amagona ndi amuna [kapena akazi] anzawo sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu, linanenanso kuti: “Ena mwa inu munali otero.”​—1 Akorinto 6:11.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu omwe anasiya khalidweli samalakalakanso atagonana ndi amuna kapena akazi anzawo? Ayi. Baibulo limanena kuti: “Muvale umunthu watsopano umene Mulungu amapereka, kutanthauza kuti mwa kudziwa zinthu molondola, muchititse umunthu wanu kukhala watsopano.” (Akolose 3:10) Kusintha sikutha ndipo kumatenga nthawi.

Koma bwanji ngati munthu amene akufuna kutsatira zimene Mulungu amafuna, akulimbanabe ndi chilakolako chofuna kugonana ndi mwamuna kapena mkazi mnzake?

Monga mmene zimakhalira ndi chilakolako chilichonse, munthu amasankha kukhutiritsa chilakolakocho kapena kuchinyalanyaza. Kodi angachite bwanji zimenezi? Baibulo limanena kuti: “Pitirizani kuyenda mwa mzimu, ndipo simudzatsatira chilakolako cha thupi ngakhale pang’ono.”​—Agalatiya 5:16.

Ngati mwaonetsetsa, lembali silikunena kuti munthuyo sangakhalenso ndi chilakolako cha thupi. Koma likusonyeza kuti angathe kulimbana ndi chilakolakochi. Angathe kuchita zimenezi ngati atakhala ndi pulogalamu yophunzira Baibulo komanso kupemphera.

David amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi akuvomerezanso zimenezi. David akufotokoza kuti anakwanitsa kulimbana ndi vutoli atapempha makolo ake omwenso ndi Akhristu, kuti amuthandize. Iye ananena kuti: “Ndimamva ngati ndinatula chimtolo cholemera. Ndipo ndimaona kuti zinthu zikanandiyendera bwino ndikanawauza makolo anga za vutoli mwamsanga.”

Zinthu zimatiyendera bwino tikamayesetsa kutsatira malamulo a Yehova. Timaona kuti malamulo ake ndi “olungama, amasangalatsa mtima” komanso ‘munthu wowasunga amapeza mphoto yaikulu.’​—Salimo 19:8, 11.