Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingaphunzitse Bwanji Chikumbumtima Changa?

Kodi Ndingaphunzitse Bwanji Chikumbumtima Changa?

Kodi chikumbumtima tingachiyerekezere ndi chiyani pa zinthu zili m’munsizi?

  • kampasi

  • galasi

  • mnzanu

  • woweruza

Yankho lolondola ndi lakuti tingachiyerekezere ndi zinthu 4 zonsezi. Nkhaniyi ifotokoza chifukwa chake tikutero.

 Kodi chikumbumtima n’chiyani?

Chikumbumtima ndi munthu wanu wamkati yemwe amakuthandizani kudziwa zoyenera ndi zosayenera kuchita. Baibulo limanena kuti chili ngati chilamulo cholembedwa m’mitima yathu. (Aroma 2:15) Chikumbumtima chabwino chingakuthandizeni kuona ngati zimene munachita kale m’mbuyomu kapena zimene mukufuna kuchita zili zabwino kapena ayi.

  • Chikumbumtima chanu chili ngati kampasi. Chimakutsogolerani kumene muyenera kupita kuti musakumane ndi mavuto.

  • Chikumbumtima chanu chili ngati galasi. Chimakuthandizani kuona kuti muli ndi khalidwe lotani. Chingakuthandizeninso kudziwa umunthu wanu weniweni.

  • Chikumbumtima chanu chili ngati mnzanu wabwino. Chingakupatseni malangizo anzeru omwe angakuthandizeni ngati mutasankha kuwatsatira.

  • Chikumbumtima chanu chili ngati woweruza. Chimakuimbani mlandu mukachita zinthu zolakwika.

Chikumbumtima chabwino chingakuthandizeni kuti muzisankha bwino zochita

Mfundo yofunika: Chikumbumtima chanu ndi chofunika kwambiri chifukwa chingakuthandizeni (1) kusankha zinthu mwanzeru, komanso (2)  kukonza zimene munalakwitsa.

 N’chifukwa chiyani muyenera kuphunzitsa chikumbumtima chanu?

Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizikhala ndi chikumbumtima chabwino.’ (1 Petulo 3:16) Zimenezi zingakhale zovuta ngati chikumbumtima chanu sichinaphunzitsidwe.

“Ndinkanamiza makolo anga zokhudza kumene ndinapita ndipo ndinkabisira aliyense nkhani imeneyi. Poyamba chikumbumtima changa chinkandivutitsa, koma kenako ndinayamba kuona kuti si nkhani yaikulu.”—Jennifer.

Koma kenako, chikumbumtima cha Jennifer chinamulimbikitsa kuti aulule nkhaniyi kwa makolo ake, ndipo anasiya kuwanamiza.

Zoti muganizire: Kodi ndi nthawi iti imene chikumbumtima cha Jennifer chimayenera kumuthandiza kuchita zimenezi?

“Kukhala moyo wachiphamaso kumachititsa kuti munthu asamasangalale. Chikumbumtima chikakulola kuchita choipa, zimakhala zosavuta kuti uchitenso zoipa zina.”—Matthew.

Anthu ena samvera chikumbumtima chawo. Baibulo limanena kuti anthu oterewa sathanso “kuzindikira makhalidwe abwino.” (Aefeso 4:19) Baibulo lina linamasulira mawu amenewa kuti, “amasiya kuchita manyazi.”—Good News Translation.

Zoti muganizire: Kodi anthu amene sadziimba mlandu akachita zoipa amakhala moyo wabwino? Kodi ndi mavuto otani amene anthu oterewa angakumane nawo?

Mfundo yofunika: Kuti mukwanitse kukhala ndi chikumbumtima chabwino, muyenera kuphunzitsa mphamvu zanu za kuzindikira kuti zizikuthandizani kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.—Aheberi 5:14.

 Kodi mungaphunzitse bwanji chikumbumtima chanu?

Kuti mukwanitse kuphunzitsa chikumbumtima chanu muyenera kukhala ndi mfundo zokuthandizani kudziwa makhalidwe abwino. Ena amatsatira mfundo zomwe zinakhazikitsidwa ndi:

  • banja kapena chikhalidwe chawo

  • anzawo

  • anthu otchuka

Komabe, mfundo za m’Baibulo ndi zabwino kwambiri kuposa mfundo zokhazikitsidwa ndi anthu. Zimenezi si zodabwitsa chifukwa Baibulo ‘linauziridwa ndi Mulungu,’ yemwe anatilenga komanso amadziwa zimene tingachite kuti zinthu zitiyendere bwino.—2 Timoteyo 3:16.

Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.

  • Kodi mfundo imeneyi ingathandize bwanji kuti chikumbumtima chanu chizikuchenjezani mukamayesedwa kuti muonere mayeso, munamize makolo anu kapena mube?

  • Ngati chikumbumtima chanu chimakuthandizani kumachita zinthu zonse moona mtima, kodi mungapindule bwanji panopa komanso m’tsogolo?

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Thawani dama.”—1 Akorinto 6:18.

  •   Kodi mfundo imeneyi ingathandize bwanji kuti chikumbumtima chanu chizikuchenjezani mukamayesedwa kuti muonere zolaula kapena kuti muchite chiwerewere?

  • Ngati chikumbumtima chanu chimakuthandizani kuthawa dama, kodi mungapindule bwanji panopa komanso m’tsogolo?

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.”—Aefeso 4:32.

  •   Kodi mfundo imeneyi ingakuthandizeni bwanji mukasemphana maganizo ndi m’bale wanu kapena mnzanu?

  • Ngati chikumbumtima chanu chikukuthandizani kuti mukhale achifundo komanso kuti muzikhululuka ena akakulakwirani, kodi mungapindule bwanji panopa komanso m’tsogolo?

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Yehova . . . amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.”—Salimo 11:5.

  •   Kodi mfundo imeneyi ingakuthandizeni bwanji kuti muzisankha bwino mafilimu, mapulogalamu a pa TV komanso magemu oyenera kusewera?

  • Ngati chikumbumtima chanu chimakuthandizani kupewa zosangalatsa zachiwawa, kodi mungapindule bwanji panopa komanso m’tsogolo?

ZOMWE ZINACHITIKADI: “Anzanga ankasewera magemu achiwawa ndipo nanenso ndinkasewera nawo. Ndiye tsiku lina bambo anga anandiuza kuti ndisamasewerenso magemu amenewo. Koma ndikapita kwa anzanga aja ndinkakasewerabe magemuwa. Ndikabwerera kunyumba, sindinkauza aliyense zimenezi. Bambo anga akandifunsa ngati pali vuto linalake, ndinkawayankha kuti palibe. Ndiye tsiku lina ndinawerenga lemba la Salimo 11:5 ndipo ndinayamba kudziimba mlandu kwambiri. Ndinazindikira kuti ndikufunika kusiya kusewera magemuwo. Ulendo umenewu ndinasiyadi. Mnzanga wina ataona zimene ndinachitazi, nayenso anasiya kusewera magemu achiwawa.”—Jeremy.

Zoti muganizire: Kodi ndi pa nthawi iti pamene chikumbumtima cha Jeremy chinayamba kugwira ntchito, nanga ndi pa nthawi iti imene anayamba kuchimvera? Kodi mwaphunzira zotani pa zomwe zinachitikira Jeremy?

Mfundo yofunika: Chikumbumtima chanu chimasonyeza kuti ndinu munthu wotani. Chimasonyezanso mfundo zimene mumakhulupirira. Ndiye kodi chikumbumtima chanu chimasonyeza zotani zokhudza inuyo?