Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapanikizike Kwambiri?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapanikizike Kwambiri?

 Kodi mukuvutika chifukwa chopanikizika ndi zinazake? Ngati ndi choncho ndiye kuti nkhaniyi ingakuthandizeni.

 Zimene zimachititsa

  •   Kukhala ndi zochita zambiri. Mtsikana wina dzina lake Julie ananena kuti: “Pa zilizonse zomwe timachita, timauzidwa kuti tiziyesetsa kuzichita bwino kwambiri komanso kukhoza bwino. Zimenezi zimachititsa kuti tizipanikizika kwambiri.”

  •   Zipangizo zamakono. Chifukwa cha zipangizo ngati mafoni, matabuleti komanso zipangizo zina zomwe tikugwiritsa ntchito panopo, anthu ena akhoza kukuimbira kapena kukutumizira meseji nthawi ina iliyonse. Zimenezi zimatopetsa ndipo kenako umayamba kupanikizika.

  •   Kusagona mokwanira. Mtsikana wina dzina lake Miranda ananena kuti: “Achinyamata ambiri amadzuka m’mawa kwambiri komanso kugona mochedwa. Amakhala ndi zochita zambiri monga kupita kusukulu, kugwira ntchito komanso kuchita zosangalatsa.” Zimenezi zimachititsa kuti munthu azipanikizika.

 Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?

 Baibulo limatilimbikitsa kugwira ntchito mwakhama. (Miyambo 6:​6-8; Aroma 12:11) Koma sikuti limati tizigwira ntchito kwambiri mpaka kufika poika moyo wathu pangozi kapena kulephera kuchita zinthu zinanso zofunika.

 Mtsikana wina dzina lake Ashley ananena kuti: “Nthawi ina ndinakhala tsiku lonse osadya kanthu pofuna kuwonetsetsa kuti ndakwanitsa kuchita zonse zomwe ndimafuna kuchita tsiku limenelo. Ndaphunzira kuti ndizitha kukanako zinthu zina chifukwa sibwino kumangovomera ntchito iliyonse yomwe ungapatsidwe mpaka kufika poika moyo wako pangozi.”

 Ndipo ndi pomveka kuti Baibulo limanena kuti: “Galu wamoyo ali bwino kuposa mkango wakufa.” (Mlaliki 9:4) Mogwirizana ndi lembali, kudzikakamiza kugwira ntchito zina kungakupangitsenidi kudzimva kuti muli ndi mphamvu ngati mkango. Koma ngati nthawi zonse mumangokhalira kupanikizika chifukwa cha zochita zambiri, mutha kuika moyo wanu pangozi.

 Zimene mungachite

  •   Muzitha kukana zinthu zina. Baibulo limanena kuti: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Munthu wodzichepetsa amadziwa zomwe sangakwanitse kuchita ndipo savomera kugwira ntchito zambirimbiri.

     Jordan ananena kuti: “Munthu amene amavomera kugwira ntchito iliyonse yomwe wapemphedwa, ndi amene amapanikizika kwambiri. Kumeneko sikudzichepetsa ndipo pakapita nthawi yochepa, amayamba kumva kuti akupanikizika.”

  •   Muzipuma mokwanira. Baibulo limanena kuti: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6) Ambiri amanena kuti tulo ndi mankhwala. Koma achinyamata ambiri sagona maola okwanira. Akatswiri amanena kuti munthu amafunika kugona maola 8 kapena 10 pa tsiku.

     Mnyamata wina dzina lake Brooklyn ananena kuti: “Ndinkalolera kugona kwa maola ochepa ndikakhala ndi zochita zambiri. Koma nthawi zambiri sindinkaganizirako kuti nthawi yotsalayo ndi imene inali yofunikanso kuti ndichite zinthu zolongosoka kukacha.”

  •   Muzikhala ndi pulogalamu. Baibulo limati: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” (Miyambo 21:5) Mukazolowera kugawa bwino nthawi komanso kudziwa ntchito zomwe mungayambirire kuzigwira, zidzakuthandizani kwa moyo wanu wonse.

     Vanessa ananena kuti: “Munthu amene amakhala ndi pulogalamu sapanikizika kwambiri. Ukamachita zinthu motsatira pulogalamu yomwe wakonza, umadziwa zinthu zimene ungafunike kusintha kuti pamapeto pake usapanikizike kwambiri.”