Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1

Kodi Ndimayendera Mfundo Ziti?

Kodi Ndimayendera Mfundo Ziti?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Kudziwa mfundo zimene mumayendera, kungakuthandizeni kuti muzisankha zochita mwanzeru anzanu akamakukakamizani kuchita zosayenera.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Tiyerekeze kuti mtsikana wina dzina lake Karen wangofika kumene paphwando. Ndiyeno mnzake akumufunsa kuti:

“Kodi iwe, bwanji wangokhala?”

Mnzakeyo ndi Jessica ndipo wanyamula mabotolo awiri a mowa otsegula kale. Kenako Jessica akumupatsa Karen botolo linalo n’kunena kuti: “Eko imwa, kumasangalalako nthawi zina.”

Karen akufuna kukana. Koma zikumuvuta chifukwa choti Jessica ndi mnzake choncho sakufuna kuoneka wotsalira. Komanso Karen amaona kuti Jessica ndi munthu wabwino ndipo ngati akumwa, ndiye kuti kumwa kulibe vuto. Karen akudziuza kuti, ‘Komansotu ndi mowa basi sikuti ndi mankhwala osokoneza ubongo.’

Kodi inuyo mukanakhala Karen, mukanatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Kuti musankhe zochita mwanzeru pa zinthu ngati zimenezi, muyenera kukhala ndi mfundo zimene mumayendera. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzidziwa zoyenera kuchita m’malo momangoyendera maganizo a anzanu.—1 Akorinto 9:26, 27.

Koma kodi mungatani kuti mukhale ndi mfundo zoti muziyendera? Poyambira pabwino ndi kupeza mayankho a mafunso otsatirawa.

1 KODI NDI ZINTHU ZITI ZOMWE NDIMACHITA BWINO?

Kudziwa zinthu zimene mumachita bwino komanso makhalidwe abwino amene muli nawo, kungakuthandizeni kuti musamadzikayikire.

CHITSANZO CHA M’BAIBULO: Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati ndilibe luso la kulankhula, sikuti ndine wosadziwanso zinthu.” (2 Akorinto 11:6) Chifukwa Paulo ankadziwa bwino Malemba, sankadzikayikira ngakhale kuti anthu ankamutsutsa. Komanso sankalola kuti zolankhula za ena zimufooketse.—2 Akorinto 10:10; 11:5.

DZIFUFUZENI: Lembani luso limene muli nalo pamzere uli m’munsiwu.

Lembaninso khalidwe labwino limene muli nalo. (Mwachitsanzo, kodi mumaganizira anthu ena, ndinu wowolowa manja, wodalirika kapena wosunga nthawi?)

2 KODI NDI ZINTHU ZITI ZOMWE SINDICHITA BWINO?

Muyenera kudziwa zinthu zimene simuchita bwino. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamangoganizira zinthu zimene simuchita bwinozo n’kufika polephera kutsatira mfundo zimene mumayendera.

CHITSANZO CHA M’BAIBULO: Paulo ankadziwa zinthu zimene sankachita bwino. Mwachitsanzo analemba kuti: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu, koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo.”—Aroma 7:22, 23.

DZIFUFUZENI: Kodi ndi zinthu ziti zimene simuchita bwino zomwe mukufuna mutasintha?

3 KODI ZOLINGA ZANGA NDI ZOTANI?

Kodi mungachite hayala galimoto n’kumuuza dalaivala kuti azingozungulira pamalo amodzimodzi mpaka mafuta kutha? Ayi, simungatero. Chifukwa kuchita zimenezo kungakhale kupanda nzeru komanso kuwononga ndalama.

Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kukhala ndi zolinga kumathandiza kuti munthu azichita zaphindu zokhazokha. Munthu akakhala ndi zolinga amadziwa kumene akupita osati kumangozungulira pamodzimodzi.

CHITSANZO CHA M’BAIBULO: Paulo analemba kuti: “Sikuti ndikungothamanga osadziwa kumene ndikulowera.” (1 Akorinto 9:26) M’malo momangochita zinthu mwachisawawa, Paulo anali ndi zolinga ndipo ankayesetsa kuzikwaniritsa.—Afilipi 3:12-14.

DZIFUFUZENI: Lembani zinthu zitatu zimene mukufuna kukwaniritsa pofika chaka chamawa.

4 KODI NDIMAKHULUPIRIRA ZINTHU ZITI?

Mukakhala ndi mfundo zimene mumayendera, mumakhala ngati mtengo wolimba umene sungagwe ndi mphepo yamphamvu

Ngati zinthu zimene mumaphunzira simuzikhulupirira, simungadziwe zoyenera kuchita. Mumakhala ngati birimankhwe n’kumangosinthasintha kuti musakhale osiyana ndi anzanu.

Koma ngati mumakhulupirira zimene mumaphunzira, mumayesetsa kuzitsatira ndipo simulola kuti anzanu azingokuuzani zochita.

CHITSANZO CHA M’BAIBULO: Mneneri Danieli ali wachinyamata, “anatsimikiza mumtima mwake” kutsatira malamulo a Mulungu, ngakhale kuti anali kutali ndi makolo ake komanso atumiki anzake. (Danieli 1:8) Izi zinamuthandiza kuti asachite zosiyana ndi mfundo zimene ankakhulupirira.

DZIFUFUZENI: Kodi inuyo mumakhulupirira zinthu ziti? Mwachitsanzo: Kodi mumakhulupirira zoti kuli Mulungu? N’chifukwa chiyani mumakhulupirira? Nanga muli ndi umboni wotani woti alikodi?

Kodi mumakhulupirira kuti mfundo za Mulungu zingakuthandizeni? N’chifukwa chiyani mumakhulupirira zimenezi?

Kodi inuyo mungafune kukhala ngati tsamba limene limangouluka ndi mphepo, kapena mtengo wolimba umene sungagwe ngakhale kutawomba chimphepo champhamvu? Ngati mukufuna kukhala ngati mtengo wolimba, muyenera kukhala ndi mfundo zimene mumayendera. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamangotengera zochita za anzanu.