Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 4:1-11

  • Masomphenya a Yehova ali kumwamba (1-11)

    • Yehova wakhala pampando wake wachifumu (2)

    • Akulu 24 akhala pamipando yachifumu (4)

    • Angelo 4 (6)

4  Zimenezi zitatha, ndinayangʼana kumwamba ndipo ndinaona khomo lotseguka. Mawu oyamba amene ndinamva akundilankhula anali ngati kulira kwa lipenga. Mawuwo anali akuti: “Kwera kumwamba kuno ndipo ndikuonetsa zinthu zimene zikuyenera kuchitika.”  Kenako nthawi yomweyo mzimu wa Mulungu unayamba kugwira ntchito mwa ine ndipo mpando wachifumu unaoneka uli pamalo ake kumwamba, wina atakhalapo.+  Amene anakhala pampandoyo ankaoneka ngati mwala wa yasipi+ komanso mwala wa sadiyo.* Utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi unazungulira mpando wachifumuwo.+  Kuzungulira mpando wachifumuwo panalinso mipando yachifumu yokwana 24. Pamipando yachifumuyo, ndinaona patakhala akulu 24+ atavala zovala zoyera komanso zisoti zachifumu zagolide kumutu kwawo.  Kumpando wachifumuko kunkatuluka mphezi,+ mawu komanso mabingu.+ Panalinso nyale zamoto 7 zimene zinkayaka patsogolo pa mpando wachifumuwo. Nyalezo zikuimira mizimu 7 ya Mulungu.+  Patsogolo pa mpando wachifumuwo, panali chinachake chooneka ngati nyanja ya galasi+ komanso ngati mwala wa kulusitalo. Pakati pa mpando wachifumuwo ndiponso kuzungulira mpandowo, panali angelo 4+ amene anali ndi maso ambirimbiri, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.  Mngelo woyamba ankaoneka ngati mkango.+ Mngelo wachiwiri ankaoneka ngati mwana wa ngʼombe wamphongo.+ Mngelo wachitatu+ anali ndi nkhope yooneka ngati ya munthu ndipo mngelo wa 4+ ankaoneka ngati chiwombankhanga chimene chikuuluka.+  Aliyense wa angelo 4 amenewa anali ndi mapiko 6 ndipo mapikowo anali ndi maso paliponse.+ Angelo amenewa sankapuma masana ndi usiku, ankangokhalira kunena kuti: “Woyera, woyera, woyera ndi Yehova*+ Mulungu, Wamphamvuyonse, amene analipo, amene alipo ndi amene akubwera.”+  Nthawi zonse angelowo akamapereka ulemerero ndi ulemu ndiponso akamayamikira Mulungu amene wakhala pampando wachifumuyo, Amene adzakhale ndi moyo kwamuyaya,+ 10  akulu 24 aja+ ankagwada nʼkuwerama pamaso pa Amene wakhala pampando wachifumuyo, nʼkulambira Amene adzakhale ndi moyo kwamuyayayo. Iwo ankaponya pansi zisoti zawo zachifumu pamaso pa mpando wachifumuwo nʼkunena kuti: 11  “Ndinu woyenera, inu Yehova* Mulungu wathu kulandira ulemerero,+ ulemu+ ndi mphamvu+ chifukwa munalenga zinthu zonse+ ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mwala wofiira wamtengo wapatali.”