Kwa Afilipi 4:1-23

  • Mgwirizano, kusangalala, maganizo abwino (1-9)

    • Musamade nkhawa ndi chinthu chilichonse (6, 7)

  • Anayamikira mphatso zimene Afilipi anapereka (10-20)

  • Moni womaliza (21-23)

4  Choncho inu abale anga amene ndimakukondani ndipo ndikulakalaka kukuonani, ndinu chimwemwe changa ndi chipewa changa chaulemerero.+ Okondedwa anga, ndikukulimbikitsani kuti mupitirize kukhala okhulupirika+ kwa Ambuye.  Ndikudandaulira Eodiya komanso ndikudandaulira Suntuke kuti athetse kusemphana maganizo kwawo monga otsatira a Ambuye.*+  Ndikupempha iwenso wantchito mnzanga weniweni,* kuti upitirize kuwathandiza azimayi amenewa. Iwo ayesetsa mwakhama kugwira ntchito yolengeza uthenga wabwino limodzi ndi ine. Achita zimenezi limodzinso ndi Kilementi komanso antchito anzanga ena onse amene mayina awo ali mʼbuku la moyo.+  Nthawi zonse muzisangalala chifukwa cha Ambuye. Ndikubwerezanso kunena kuti, Muzisangalala!+  Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.+ Ambuye ali pafupi.  Musamade nkhawa ndi chinthu chilichonse.+ Mʼmalomwake, nthawi zonse muzipemphera kwa Mulungu, muzimuchonderera kuti azikutsogolerani pa chilichonse ndipo nthawi zonse muzimuthokoza.+  Mukatero, mtendere+ wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa, udzateteza mitima yanu+ ndi maganizo anu pamene mukutsatira Khristu Yesu.  Chomalizira abale, pitirizani kuganizira* zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zolimbikitsa chikondi, zilizonse zimene anthu amaziyamikira, khalidwe labwino lililonse komanso chilichonse chotamandika.+  Zinthu zimene munaphunzira, zimene munazivomereza, zimene munamva kwa ine komanso zimene munandiona ndikuchita, muzichita zimenezo+ ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu. 10  Ine ndikusangalala kwambiri mwa Ambuye kuti tsopano mwayambiranso kundiganizira.+ Ndikudziwa kuti mwakhala mukundiganizira nthawi yonseyi, koma kungoti mumasowa mpata wosonyeza zimenezi. 11  Sindikulankhula zimenezi chifukwa chakuti ndikusowa kanthu, chifukwa ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo posatengera mmene zinthu zilili pa moyo wanga.+ 12  Ndikudziwa mmene zimakhalira ukakhala ndi zinthu zochepa+ komanso mmene umasangalalira ukakhala ndi zochuluka. Pa chilichonse komanso pa zochitika zosiyanasiyana, ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhuta ndi chokhala wanjala. Ndaphunziranso chinsinsi chokhala ndi zochuluka komanso chokhala wopanda kalikonse. 13  Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa Mulungu amene amandipatsa mphamvu zimene ndikufunikira.+ 14  Komabe, munachita bwino pondithandiza pa mavuto anga. 15  Ndipo inu Afilipi, mukudziwanso kuti pamene ndinkachoka ku Makedoniya, mutangomva kumene uthenga wabwino, panalibe mpingo ngakhale umodzi umene unathandizana nane pa nkhani ya kupatsa ndi kulandira, kupatulapo inu nokha.+ 16  Chifukwa pamene ndinali ku Tesalonika, inu munanditumizira kenakake kuti kandithandize pa zimene ndinkafunikira ndipo simunachite zimenezi kamodzi kokha, koma kawiri. 17  Sikuti ndikufuna kuti mundipatse mphatso, koma ndikufunitsitsa kuti muzichita zinthu zabwino zimene zingakupindulireni kwambiri. 18  Komabe, ine ndili ndi zonse zimene ndikufunikira ndipo zikuposa pa zimene ndikufunikira. Sindikusowa kanthu chifukwa Epafurodito+ wandipatsa zinthu zimene mwanditumizira. Zinthu zimenezi zili ngati fungo lonunkhira bwino+ ndiponso nsembe yovomerezeka yomwe ndi yosangalatsa kwa Mulungu. 19  Chifukwa cha zimenezi, Mulungu wanga adzakupatsani zonse zimene mukufunikira+ mogwirizana ndi kuchuluka kwa chuma chake chaulemerero, kudzera mwa Khristu Yesu. 20  Tsopano Mulungu amene ndi Atate wathu alandire ulemerero mpaka muyaya. Ame. 21  Mundiperekere moni kwa woyera aliyense amene ndi wophunzira wa Khristu Yesu. Abale amene ali ndi ine akukupatsani moni. 22  Oyera onse akupereka moni, koma makamaka a mʼnyumba ya Kaisara.+ 23  Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale nanu, chifukwa muli ndi maganizo abwino.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kuti akhale ndi maganizo amodzi pamene akutumikira Ambuye.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mnzanga weniweni wosenza naye limodzi goli.”
Kapena kuti, “kuganizira mozama.”