Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limaletsa Kugonana?

Kodi Baibulo Limaletsa Kugonana?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo sililetsa kugonana koma limasonyeza kuti kugonanako ndi mphatso yochokera kwa Mulungu imene anthu okwatirana ayenera kusangalala nayo. Mulungu analenga “mwamuna ndi mkazi” ndipo anaona kuti zonse zimene analenga zinali “zabwino kwambiri.” (Genesis 1:27, 31) Pa nthawi imene Mulungu ankapereka Hava kwa Adamu kuti akhale mkazi wake, ananena kuti “iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Umenewu unali ukwati woyambirira ndipo Adamu ndi mkazi wake anafunika kumakondana kwambiri komanso kumasangalala ndi mphatso ya kugonana.

 Ponena za chisangalalo chimene mwamuna wokwatira amapeza mwa mkazi wake, Baibulo limati: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako . . . Mabere ake akukhutiritse nthawi zonse. Nthawi zonse uzikhala wokondwa kwambiri ndi chikondi chake.” (Miyambo 5:18, 19) Mulungu amafunanso kuti akazi okwatiwa azisangalala kwambiri akamagonana ndi amuna awo. Baibulo limati: “Mwamuna azikhutiritsa mkazi wake pogonana nayenso mkazi azikhutiritsa mwamuna wake.”—1 Akorinto 7:3, God’s Word Bible.

Zimene Baibulo limaletsa pa nkhani yogonana

 Mulungu anakonza zoti anthu okhawo amene ayenera kugonana ndi okwatirana basi. Pamfundo imeneyi, lemba la Aheberi 13:4 limati: “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.” Choncho anthu okwatirana ayenera kukhala okhulupirika ndipo sayenera kugonana ndi munthu wina aliyense yemwe si mkazi kapena mwamuna wawo. Ndipotu mwamuna kapena mkazi wapabanja amakhala wosangalala kwambiri akamapewa mtima wadyera wongofuna kudzikhutiritsa, koma akamatsatira mfundo ya m’Baibulo iyi: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.