Wolembedwa ndi Yohane 13:1-38

  • Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake (1-20)

  • Yesu ananena kuti Yudasi adzamupereka (21-30)

  • Lamulo latsopano (31-35)

    • “Ngati mukukondana” (35)

  • Ananeneratu kuti Petulo adzamukana (36-38)

13  Tsopano Yesu anadziwiratu chikondwerero cha Pasika chisanafike kuti nthawi yake yochoka mʼdzikoli kupita kwa Atate+ yakwana.+ Ndipo popeza kuti ankakonda otsatira akewo amene anali mʼdzikoli, anawakonda mpaka pamapeto a moyo wake.+  Chakudya chamadzulo chinali chili mkati ndipo Mdyerekezi anali ataika kale maganizo ofuna kupereka Yesu+ mumtima mwa Yudasi Isikariyoti,+ mwana wa Simoni.  Yesu ankadziwa kuti Atate anapereka zinthu zonse mʼmanja mwake komanso kuti anabwera kuchokera kwa Mulungu ndiponso kuti ankapita kwa Mulungu.+  Choncho anaimirira pa chakudya chamadzulocho nʼkuvula malaya ake akunja. Kenako anatenga thaulo nʼkulimanga mʼchiuno mwake.+  Atatero anathira madzi mʼbeseni nʼkuyamba kusambitsa mapazi a ophunzirawo komanso kuwapukuta ndi thaulo limene anamanga mʼchiuno lija.  Kenako anafika pa Simoni Petulo. Koma Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, inuyo mukufuna musambitse mapazi anga?”  Yesu anayankha kuti: “Zimene ndikuchitazi sungazimvetse panopa, koma pambuyo pake udzamvetsa.”  Petulo anati: “Ndithu, sizitheka kuti musambitse mapazi anga.” Yesu anamuyankha kuti: “Ndikapanda kukusambitsa,+ palibe chako kwa ine.”  Simoni Petulo anati: “Ambuye, musandisambitse mapazi okha, koma mundisambitsenso manja ndi mutu womwe.” 10  Yesu anamuuza kuti: “Amene wasamba mʼthupi amangofunika kusamba mapazi okha basi, chifukwa thupi lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, koma osati nonsenu.” 11  Iye ankadziwa munthu amene anakonza zoti amupereke.+ Nʼchifukwa chake ananena kuti: “Sikuti nonsenu ndinu oyera.” 12  Tsopano atasambitsa mapazi awo nʼkuvalanso malaya ake akunja aja, anakhalanso patebulo. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa chifukwa chake ndasambitsa mapazi anu? 13  Inu mumanditchula kuti ‘Mphunzitsiʼ komanso ‘Ambuye,’ mumalondola, chifukwa ndinedi Mphunzitsi komanso Ambuye.+ 14  Choncho ngati ine amene ndi Ambuye komanso Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu,+ inunso mukuyenera kusambitsana mapazi.+ 15  Chifukwa ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.+ 16  Ndithudi ndikukuuzani, kapolo saposa mbuye wake, ndiponso wotumidwa saposa amene wamutuma. 17  Ngati zimenezi mukuzidziwa, mudzakhala osangalala mukamazichita.+ 18  Sindikunena nonsenu, ndikudziwa amene ndawasankha. Koma zimenezi zachitika kuti lemba likwaniritsidwe,+ limene limati: ‘Munthu amene ankadya chakudya changa, watukula chidendene chake nʼkundiukira.’*+ 19  Kuyambira panopa kupita mʼtsogolo, ndizikuuziranitu zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire kuti amene munkamuyembekezera uja ndi ine.+ 20  Ndithudi ndikukuuzani, aliyense amene walandira yemwe ine ndamutuma walandiranso ine.+ Ndipo amene walandira ine, walandiranso amene anandituma.”+ 21  Atanena zimenezi, Yesu anavutika kwambiri mumtima, ndipo anachitira umboni kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipereka.”+ 22  Ophunzirawo anayamba kuyangʼanizana chifukwa sankadziwa kuti akunena ndani.+ 23  Mmodzi wa ophunzirawo, amene Yesu ankamukonda,+ anakhala pafupi ndi Yesu.* 24  Choncho Simoni Petulo anamugwedezera mutu nʼkumuuza kuti: “Tiuze kuti akunena ndani.” 25  Ndiyeno wophunzira winayo anatsamira pachifuwa pa Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ambuye, mukunena ndani?”+ 26  Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse mkate umene ndisunse.”+ Choncho atasunsa mkatewo, anapatsa Yudasi, mwana wa Simoni Isikariyoti. 27  Yudasi atalandira mkatewo, Satana analowa mwa iye.+ Choncho Yesu anamuuza kuti: “Zimene wakonza kuti uchite, zichite mwamsanga.” 28  Koma pa anthu amene anakhala nawo patebulowo, panalibe aliyense amene anadziwa chifukwa chake anamuuza zimenezo. 29  Popeza Yudasi ankasunga bokosi la ndalama,+ ena ankaganiza kuti Yesu ankamuuza kuti, “Ugule zinthu zonse zimene zikufunikira pachikondwerero,” kapena kuti apereke kenakake kwa osauka. 30  Choncho Yudasi atalandira mkatewo, anatuluka nthawi yomweyo ndipo unali usiku.+ 31  Yudasi atatuluka, Yesu anati: “Tsopano Mwana wa munthu walemekezedwa,+ ndipo Mulungu walemekezedwa kudzera mwa iye. 32  Mulungu amulemekeza+ ndipo amulemekeza nthawi yomwe ino. 33  Anzanga apamtima inu,* ndikhala nanu kanthawi kochepa chabe. Mudzandifunafuna, ndipo mogwirizana ndi zimene ndinauza Ayuda aja kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kukafikako,’+ tsopano ndikuuzanso inuyo. 34  Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mofanana ndi mmene ine ndakukonderani,+ inunso muzikondana choncho.+ 35  Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.”+ 36  Simoni Petulo anamufunsa kuti: “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu anayankha kuti: “Kumene ndikupita sunganditsatire panopa, koma udzanditsatira mʼtsogolo.”+ 37  Petulo anafunsanso kuti: “Ambuye, nʼchifukwa chiyani sindingakutsatireni panopa? Ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha inu.”+ 38  Yesu anayankha kuti: “Kodi udzapereka moyo wako chifukwa cha ine? Ndithudi ndikukuuza iwe, tambala asanalire undikana katatu.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wandiukira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anakhala pachifuwa pa Yesu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aangʼono inu.”