Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA

Kodi Mumatani Wina Akakupatsani Malangizo pa Zomwe Mwalakwitsa?

Kodi Mumatani Wina Akakupatsani Malangizo pa Zomwe Mwalakwitsa?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

“Munthu wina akakudzudzulani, zimasonyeza kuti mwalakwitsa zinazake. Koma sindinamvepo munthu atanena kuti ‘Ndimasangalala munthu akamandipatsa malangizo ngati ndalakwitsa zinazake.’”—Amy, wazaka 17. *

”Munthu amene amakana kulandira malangizo amakhala ngati munthu amene akuyendetsa ndege, n’kumakana kutsatira zimene akuuzidwa kuchokera kwa munthu yemwe amaona za kayendedwe ka ndege pabwalo la ndege. Zimenezi zikhoza kuchititsa ngozi yaikulu.”

Kodi simufuna kuti makolo anu, aphunzitsi kapena munthu wina wachikulire, akuuzeni kuti mwalakwitsa zinazake? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Aliyense amafunika kudzudzulidwa.

“Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.”—Yakobo 3:2.

“Si zochititsa manyazi, munthu wina akakudzudzula pa zimene walakwitsa.”—Jessica.

Munthu wina akakuuza kuti walakwitsa chinachake, sizitanthauza kuti palibe chabwino chimene umachita.

“Yehova * amadzudzula munthu amene amam’konda, monga momwe bambo amadzudzulira mwana amene amakondwera naye.”—Miyambo 3:12.

“Munthu akandipatsa malangizo pa zimene ndalakwitsa, ndimayamikira chifukwa ndimadziwa kuti ngati munthuyo walimba mtima kundiuza, ndiye kuti amandikonda.”—Tamara.

Malangizo angakuthandizeni kukhala munthu wabwino.

“Mverani malangizo kuti mukhale anzeru.”—Miyambo 8:33.

“Munthu wina akatipatsa malangizo chifukwa cha zimene talakwitsa, zimathandiza. Zimakuthandiza kudziwa mmene ena amakuonera komanso zimakuthandiza kuti usiye makhalidwe enaake oipa omwe sumadziwa kuti uli nawo.”—Deanne.

 ZIMENE MUNGACHITE

Musafulumire kukwiya. Munthu wina akakupatsani malangizo mwina mungakhumudwe. Komabe yesetsani kuugwira mtima. Kuti muchite zimenezi, yerekezerani kuti walakwitsayo ndi mng’ono wanu ndipo mukufunika kumudzudzula. Kodi tsopano mukuona kufunika kodzudzula munthu amene walakwitsa chinachake? Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa kuti nanunso mumafunika kudzudzulidwa.—Lemba lothandiza: Mlaliki 7:9.

“Nthawi zina mungakhumudwe chifukwa chakuti munthu wina wakudzudzulani, n’kuiwala kuti munthuyo wachita zimenezo chifukwa chokukondani osati kufuna kukukhumudwitsani.”—Theresa.

Khalani odzichepetsa. Musalole kuti kunyada kukulepheretseni kutsatira malangizo amene munthu wina wakupatsani chifukwa cha zimene mwalakwitsa. Komanso, munthu akakudzudzulani, si bwino kukhumudwa kwambiri n’kumangoganizira zimene munalakwitsazo. Kudzichepetsa kungakuthandizeni kuti musalephere kutsatira malangizo amene mwapatsidwa. Komanso kudzichepetsa kungakuthandizeni kuti musakhumudwe kwambiri chifukwa cha zomwe mwalakwitsa. Kumbukirani kuti: Malangizo amene angakhale owawa kwambiri, mwina ndi amene angakuthandizeni kwambiri. Ngati simungatsatire malangizo oterowo, mungalephere kusintha zinthu zolakwika zimene munachita.—Lemba lothandiza: Miyambo 16:18.

Malangizo amene angakhale owawa kwambiri, mwina ndi amene angakuthandizeni kwambiri

“Kustatira malangizo omwe wapatsidwa n’kofunika kwambiri makamaka ukamakula. Munthu akhoza kukumana ndi mavuto aakulu ngati atapanda kutsatira zimene amalangizidwa.”—Lena.

Muziyamikira. Ngakhale mutaona kuti kutsatira zimene mwalangizidwazo n’kovuta, muyenera kuyamikira munthu amene wakupatsani malangizowo. N’zosakayikitsa kuti munthuyo amafuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino ndiponso amakukondani kwambiri.—Lemba lothandiza: Salimo 141:5.

“Kuthokoza munthu amene watipatsa malangizo amene timafunikiradi, n’kothandiza. Koma ngakhale zitakhala kuti malangizowo si othandiza kwa inuyo, mungachitebe bwino kumuthokoza munthuyo chifukwa choyesetsa kufuna kukuthandizani.”—Carla.

^ ndime 4 Tasintha maina ena m’nkhaniyi.

^ ndime 11 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.