Kwa Agalatiya 5:1-26

  • Ufulu wa Akhristu (1-15)

  • Kuyenda motsogoleredwa ndi mzimu (16-26)

    • Ntchito za thupi (19-21)

    • Makhalidwe amene anthu amakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu woyera (22, 23)

5  Khristu anatimasula kuti tikhale ndi ufulu umenewu. Choncho khalani olimba+ ndipo musalole kuti mumangidwenso mugoli la ukapolo.+  Tamverani! Ine Paulo, ndikukuuzani kuti mukadulidwa, zimene Khristu anachita sizidzakhala zaphindu kwa inu.+  Kachiwirinso ndikukumbutsa munthu aliyense amene akudulidwa, kuti afunikanso kutsatira zonse za mʼChilamulo.+  Inu amene mukufuna kuti muzionedwa kuti ndinu olungama chifukwa chotsatira chilamulo,+ mwadzilekanitsa ndi Khristu. Ndipo mwachititsa kuti musadzalandirenso kukoma mtima kwake kwakukulu.  Koma kudzera mwa mzimu, ife tikuyembekezera mwachidwi zimene zidzatichitikire chifukwa choonedwa kuti ndife olungama, chifukwa cha chikhulupiriro.  Chifukwa ngati munthu ali wogwirizana ndi Khristu Yesu, kudulidwa kapena kusadulidwa kumakhala kopanda ntchito.+ Koma chofunika kwambiri nʼkukhala ndi chikhulupiriro chimene chimaonekera posonyeza chikondi.  Munkathamanga bwino.+ Anakusokonezani ndi ndani kuti musapitirize kumvera choonadi?  Zimene anthu omwe anakusokonezaniwo ankaphunzitsa sizinachokere kwa Mulungu amene anakuitanani.  Zofufumitsa zochepa zimafufumitsa mtanda wonse.+ 10  Ndikukhulupirira kuti inu amene muli ogwirizana ndi Ambuye,+ simudzasintha maganizo. Koma munthu amene amakuvutitsaniyo+ kaya akhale ndani, adzalandira chiweruzo chomuyenerera. 11  Kunena za ine abale, ngati ndikulalikirabe kuti anthu azidulidwa, nʼchifukwa chiyani ndikuzunzidwabe? Zikanakhala choncho, ndiye kuti zimene ndimaphunzitsa zokhudza imfa ya Yesu pamtengo wozunzikirapo,*+ sizikanakhumudwitsanso anthu. 12  Ndikanakonda kuti anthu amene akufuna kukupotozani maganizowo, adzifule okha.* 13  Abale, munaitanidwa kuti mukhale aufulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu umenewu ngati mwayi woti muzichita zimene thupi lomwe si langwiro limalakalaka.+ Mʼmalomwake muzilola kuti chikondi chizikulimbikitsani kutumikirana.+ 14  Chifukwa Chilamulo chonse chagona* mulamulo limodzi lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 15  Koma mukapitiriza kulumana komanso kudyana nokhanokha,+ samalani kuti musawonongane.+ 16  Mʼmalomwake ndikuti, Pitirizani kuyenda motsogoleredwa ndi mzimu,+ ndipo simudzachita zimene thupi lomwe si langwiro likulakalaka ngakhale pangʼono.+ 17  Chifukwa zimene thupi limalakalaka zimalimbana ndi mzimu ndipo mzimu nawonso umalimbana ndi thupi. Zinthu ziwiri zimenezi zimatsutsana kuti musachite zinthu zimene mumafuna kuchita.+ 18  Komanso ngati mukutsogoleredwa ndi mzimu, simuli pansi pa chilamulo. 19  Tsopano ntchito za thupi lochimwali zimaonekera mosavuta. Ntchito zimenezi ndi chiwerewere,*+ khalidwe limene limadetsa munthu, khalidwe lopanda manyazi,*+ 20  kulambira mafano, kukhulupirira mizimu,*+ chidani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, 21  kaduka, kumwa mwauchidakwa,*+ maphwando oipa,* ndi zina zotero.+ Abale, mogwirizana ndi zimene ndinakuchenjezani kale, ndikukuchenjezaninso kuti anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.+ 22  Koma makhalidwe amene anthu amakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu woyera* ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino,+ chikhulupiriro, 23  kufatsa ndi kudziletsa.+ Palibe lamulo loletsa makhalidwe amenewa. 24  Ndiponso anthu amene ndi ophunzira a Khristu Yesu, anakhomerera pamtengo thupi lawo pamodzi ndi zimene limakhumba komanso zimene limalakalaka.+ 25  Ngati tikutsogoleredwa ndi mzimu pa moyo wathu, tiyeni tipitirize kuchita zinthu mogwirizana ndi mzimuwo.+ 26  Tisakhale odzikuza,+ tisamayambitse mpikisano pakati pathu+ komanso tisamachitirane kaduka.

Mawu a M'munsi

Izi zikanachititsa kuti akhale osayenerera kuchita zimene chilamulo chomwe ankalimbikitsacho chimanena.
Kapena kuti, “chakwaniritsidwa.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
MʼChigiriki a·sel′gei·a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kuchita zamatsenga.”
Kapena kuti, “maphwando aphokoso.”
Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “kumwa mwauchidakwa” amatanthauza kumwa mowa kwambiri ndiponso mosadziletsa nʼcholinga chofuna kuledzera.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Koma chipatso cha mzimu.”