Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kudziphoda Komanso Kuvala Zodzikongoletsera?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kudziphoda Komanso Kuvala Zodzikongoletsera?

Yankho la m’Baibulo

 Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza mwatsatanetsatane za nkhaniyi, silimaletsa kudziphoda, kuvala zibangili ndi ndolo, kapena kugwiritsa ntchito njira zina zodzikongoletsera. Komabe, m’malo mofotokoza kwambiri za kaonekedwe ka kunja, Baibulo limalimbikitsa kudzikongoletsa ndi “zovala zosawonongeka, ndizo mzimu wabata ndi wofatsa.”—1 Petulo 3:3, 4.

Kudzikongoletsa sikoletsedwa

  •   Akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo ankadzikongoletsa. Rabeka, yemwe anakwatiwa ndi mwana wa Abulahamu dzina lake Isaki, ankavala ndolo yagolide ya pamphuno, zibangili zagolide komanso zinthu zina za mtengo wapatali zomwe Abulahamu yemwe anali kudzakhala mpongozi wake anamupatsa monga mphatso. (Genesis 24:22, 30, 53) Nayenso Esitere analola kupakidwa “mafuta okongoletsa” pokonzekera udindo wake wodzakhala mfumukazi ya Ufumu wa Perisiya. (Esitere 2:7, 9, 12) Zodzikongoletserazi ziyenera kuti zinkaphatikizapo “zodzoladzola za mitundu yosiyanasiyana.”—New International Version; Easy-to-Read Version.

  •   Mafanizo a m’Baibulo amayerekezera zibangili komanso ndolo ndi zinthu zabwino. Mwachitsanzo, limanena kuti munthu wanzeru amene akupereka malangizo kwa “munthu wa khutu lomvetsera, amakhala ngati ndolo yagolide.” (Miyambo 25:12) Komanso, Mulungu anayerekezera zimene iye ankachitira mtundu wa Isiraeli ndi mwamuna amene amakongoletsa mkwatibwi ndi zibangili, mkanda wa m’khosi, komanso ndolo. Zimenezi zinakongoletsa kwambiri mtunduwo “ndipo unakhala chiphadzuwa.”—Ezekieli 16:11-13.

Maganizo olakwika pa nkhani yodziphoda ndi kuvala zodzikongoletsera

 Maganizo olakwika: Pa lemba la 1 Petulo 3:3, Baibulo limaletsa ‘kumanga tsitsi ndi kuvala zodzikongoletsera zagolide.’

 Zoona zake: Nkhaniyi ikusonyeza kuti Baibulo limalimbikitsa kwambiri kukongola kwa mkati poyerekezera ndi maonekedwe abwino akunja. (1 Petulo 3:3-6) Palinso mavesi ena m’Baibulo amene amasonyeza kuti chofunika kwambiri ndi maonedwe amkati osati akunja.—1 Samueli 16:7; Miyambo 11:22; 31:30; 1 Timoteyo 2:9, 10.

 Maganizo olakwika: Zimene Mfumukazi yoipa Yezebeli anachita “podzipaka utoto wakuda m’maso mwake” ndi umboni wakuti kuphoda n’kolakwika.—2 Mafumu 9:30.

 Zoona zake: Yehova anapha Yezebeli chifukwa cha zoipa zimene anachita osati chifukwa cha kudzikongoletsa.​—2 Mafumu 9:7, 22, 36, 37.