Yesaya 45:1-25

  • Koresi anadzozedwa kuti agonjetse Babulo (1-8)

  • Dongo silikuyenera kulimbana ndi Woliumba (9-13)

  • Anthu a mitundu ina anazindikira Isiraeli (14-17)

  • Mulungu ndi wodalirika polenga zinthu komanso poulula zamʼtsogolo (18-25)

    • Dziko lapansi linalengedwa kuti anthu azikhalamo (18)

45  Izi ndi zimene Yehova akunena kwa wodzozedwa wake, kwa Koresi,+Amene wamugwira dzanja lake lamanja+Kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+Kuti alande zida zankhondo za mafumu,*Kuti amutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri,Kuti mageti adzakhale osatseka. Iye wamuuza kuti:   “Ine ndidzakhala patsogolo pako+Ndipo ndidzasalaza zitunda. Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zakopa,*Ndipo ndidzadula zitsulo zotsekera zitseko.+   Ndidzakupatsa chuma chimene chili mumdimaNdiponso chuma chimene chabisidwa mʼmalo achinsinsi,+Kuti udziwe kuti ine ndine Yehova,Mulungu wa Isiraeli, amene ndikukuitana pokutchula dzina lako.+   Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo ndi Isiraeli wosankhidwa wanga,Ine ndikukuitana pokutchula dzina lako. Ndikukupatsa dzina laulemu, ngakhale kuti sukundidziwa.   Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina. Palibenso Mulungu wina kupatulapo ine.+ Ndidzakupatsa mphamvu* ngakhale kuti sukundidziwa,   Kuti anthu adziweKuyambira kumene kumatulukira dzuwa mpaka kumene limalowera*Kuti palibenso wina kupatulapo ine.+ Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+   Ndimapanga kuwala+ ndiponso ndimabweretsa mdima.+Ndimabweretsa mtendere+ komanso tsoka.+Ine Yehova ndimapanga zonsezi.   Inu kumwamba, chititsani kuti mvula igwe.+Chititsani kuti mitambo igwetse chilungamo ngati mvula. Dziko lapansi litseguke ndipo libale chipulumutso,Pa nthawi imodzimodziyo lichititse kuti chilungamo chiphuke.+ Ine Yehova ndachititsa zimenezi.”   Tsoka kwa amene akulimbana* ndi amene anamupanga,Chifukwa iye ali ngati phaleLimene lili pakati pa mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo lingafunse woumba mbiya* kuti: “Kodi ukupanga chiyani?”+ Kapena kodi chinthu chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”?* 10  Tsoka kwa amene akufunsa bambo kuti: “Kodi nʼchiyani mwaberekachi?” Ndiponso wofunsa mkazi kuti: “Kodi nʼchiyani mukuberekachi?”* 11  Yehova, Woyera wa Isiraeli+ ndiponso amene anamuumba, wanena kuti: “Kodi ukukaikira mawu anga okhudza zinthu zimene zikubweraNdipo ukundilamula zinthu zokhudza ana anga+ komanso ntchito ya manja anga? 12  Ineyo ndinapanga dziko lapansi+ ndipo ndinalenga munthu nʼkumuika padzikolo.+ Ndinatambasula kumwamba ndi manja angawa,+Ndipo zinthu zonse zimene zili kumwambako* ndimazipatsa malamulo.+ 13  Ine ndapatsa munthu mphamvu kuti achitepo kanthu mwachilungamo,+Ndipo njira zake zonse ndidzaziwongola. Iye ndi amene adzamange mzinda wanga+Komanso kumasula anthu anga amene ali ku ukapolo,+ popanda malipiro kapena chiphuphu,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 14  Yehova wanena kuti: “Phindu la ku Iguputo,* malonda* a ku Itiyopiya ndi Asabeya, anthu ataliatali,Adzabwera kwa iwe ndipo adzakhala ako. Iwo adzayenda pambuyo pako atamangidwa mʼmaunyolo Adzabwera nʼkudzakugwadira.+ Adzapemphera kwa iwe kuti, ‘Zoonadi Mulungu ali ndi iwe,+Ndipo palibenso wina. Palibenso Mulungu wina.’” 15  Ndithu, inu ndinu Mulungu amene amadzibisa,Inu Mulungu wa Isiraeli, Mpulumutsi.+ 16  Anthu onse adzachititsidwa manyazi ndipo adzanyozeka.Anthu onse amene amapanga mafano adzachoka mwamanyazi.+ 17  Koma Isiraeli adzapulumutsidwa ndi Yehova ndipo chipulumutso chake chidzakhala chosatha.+ Inu simudzachititsidwa manyazi kapena kunyozeka mpaka kalekale.+ 18  Chifukwa Yehova,Mlengi wakumwamba,+ Mulungu woona,Amene anaumba dziko lapansi, amene analipanga ndi kulikhazikitsa mwamphamvu,+Amene sanalilenge popanda cholinga,* koma analiumba kuti anthu akhalemo,+ wanena kuti: “Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina. 19  Ine sindinalankhule mʼmalo obisika,+ mʼdziko lamdima.Sindinauze mbadwa* za Yakobo kuti,‘Muzindifunafuna pachabe.’ Ine ndine Yehova, amene ndimalankhula zolungama komanso kulengeza zinthu zimene ndi zolondola.+ 20  Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere. Mubwere pamodzi, inu anthu amene mwapulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula zifaniziro zawo zogoba sadziwa chilichonseNdipo amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+ 21  Lankhulani ndipo mufotokoze mlandu wanu. Mukambirane mogwirizana. Kodi ndi ndani ananeneratu zimenezi kalekaleNʼkuzilengeza kuyambira kalekale? Kodi si ine, Yehova? Palibenso Mulungu wina koma ine ndekha.Ine ndi Mulungu wolungama komanso Mpulumutsi+ ndipo palibenso wina kupatulapo ine.+ 22  Tembenukirani kwa ine kuti mupulumuke,+ inu nonse amene muli kumalekezero a dziko lapansi,Chifukwa ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.+ 23  Ndalumbira pa dzina langa.Mawu amene atuluka pakamwa panga ndi olondola,Ndipo adzakwaniritsidwa ndithu:+ Bondo lililonse lidzandigwadira,Ndipo lilime lililonse lidzalumbira kuti lidzakhala lokhulupirika kwa ine,+ 24  Nʼkunena kuti, ‘Zoonadi, kwa Yehova kuli chilungamo chechicheni komanso mphamvu. Onse omukwiyira adzabwera kwa iye mwamanyazi. 25  Mbadwa* zonse za Isiraeli zidzaona kuti zinachita bwino kutumikira Yehova,+Ndipo zidzadzitama chifukwa cha zinthu zimene iye anazichitira.’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimasule mʼchiuno mwa mafumu.”
Kapena kuti, “zamkuwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzakumanga mwamphamvu mʼchiuno mwako.”
Kapena kuti, “Kuchokera kumʼmawa kukafika kumadzulo.”
Kapena kuti, “akutsutsana.”
Kapena kuti, “amene akuliumba.”
Mabaibulo ena amati, “Kapena kodi dongo linganene kuti: ‘Chimene waumbacho chilibe zogwiriraʼ?”
Kapena kuti, “Mukuvutikiranji ndi ululu wa pobereka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “magulu awo onse ankhondo.”
Mabaibulo ena amati, “Antchito a ku Iguputo.”
Mabaibulo ena amati, “amalonda.”
Mabaibulo ena amati, “sanalipange kuti likhale lopanda kanthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”