Yesaya 42:1-25

  • Mtumiki wa Mulungu komanso ntchito imene wapatsidwa (1-9)

    • ‘Dzina langa ndi Yehova’ (8)

  • Nyimbo yatsopano yotamanda Yehova (10-17)

  • Isiraeli ali ndi vuto losaona komanso losamva (18-25)

42  Taonani mtumiki wanga+ amene ndikumuthandiza, Wosankhidwa wanga+ amene amandisangalatsa,+ Ine ndaika mzimu wanga mwa iye.+Iye adzabweretsa chilungamo kwa anthu a mitundu ina.+   Iye sadzafuula kapena kulankhula mokweza mawu,Ndipo sadzachititsa kuti mawu ake amveke mumsewu.+   Bango lophwanyika sadzalithyola,Ndipo chingwe cha nyale chimene chikufuka utsi sadzachizimitsa.+ Iye adzabweretsa chilungamo mokhulupirika.+   Iye sadzafooka kapena kutaya mtima mpaka atakhazikitsa chilungamo padziko lapansi.+Ndipo zilumba zikudikirirabe malamulo ake.*   Mulungu woona Yehova,Amene analenga kumwamba ndiponso Mulungu Wamkulu amene anakutambasula,+Amene anapanga dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo,+Amene amapereka mpweya kwa anthu amene ali mmenemo,+Komanso mzimu* kwa anthu amene amayenda padzikolo,+ wanena kuti:   “Ineyo Yehova pofuna kusonyeza chilungamo, ndinakuitana.Ndakugwira dzanja. Ndidzakuteteza ndipo udzakhala ngati pangano pakati pa ine ndi anthu+Ndiponso ngati kuwala ku mitundu ya anthu,+   Kuti ukatsegule maso a anthu amene ali ndi vuto losaona,+Kuti ukatulutse mkaidi mʼdzenje lamdimaNdiponso kuti anthu amene ali mumdima akawatulutse mʼndende.+   Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.Sindipereka ulemerero wanga kwa wina aliyenseNdipo sindifuna kuti aliyense azitamanda zifaniziro zogoba mʼmalo mwa ine.+   Taonani, zinthu zimene ndinaneneratu kalekale zachitika,Tsopano ndikulengeza zinthu zatsopano. Zisanayambe kuonekera, ndimakuuzani.”+ 10  Imbirani Yehova nyimbo yatsopano.+Mʼtamandeni kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+Inu nonse amene mumadalira nyanja komanso zonse zimene zimakhala mmenemo,Inu zilumba ndi anthu amene amakhala mʼzilumbazo.+ 11  Chipululu ndi mizinda yake zifuule+Komanso midzi imene kumakhala Akedara.+ Anthu amene amakhala mʼdera lamatanthwe afuule mosangalala.Anthuwo afuule kuchokera pamwamba pa mapiri. 12  Anthuwo apereke ulemerero kwa YehovaNdipo anthu amʼzilumba anene za ulemerero wake.+ 13  Yehova adzapita kunkhondo ngati munthu wamphamvu.+ Iye adzachita zinthu modzipereka kwambiri ngati msilikali.+ Adzafuula, inde adzafuula ngati anthu amene akupita kunkhondo.Iye adzasonyeza kuti ndi wamphamvu kwambiri kuposa adani ake.+ 14  Mulungu wanena kuti: “Ndakhala chete kwa nthawi yaitali. Ndinangokhala phee osachita chilichonse. Mofanana ndi mkazi amene akubereka,Ndibuula, ndipuma movutikira komanso mwawefuwefu. Zonsezi zichitika nthawi imodzi. 15  Ndidzawononga mapiri ndi zitundaNdi kuumitsa zomera zonse zimene zili mmenemo. Mitsinje ndidzaisandutsa zilumba*Ndipo ndidzaumitsa madambo onse amadzi.+ 16  Anthu amene ali ndi vuto losaona ndidzawatsogolera kuti ayende mʼnjira imene sakuidziwa.+Ndidzawadutsitsa mʼnjira zachilendo.+ Mdima ndidzausandutsa kuwala pamaso pawo+Ndipo malo okumbikakumbika ndidzawasalaza.+ Zimenezi ndi zimene ndidzawachitire ndipo sindidzawasiya.” 17  Anthu amene akudalira zifaniziro zosema,Amene akuuza zifaniziro zachitsulo* kuti: “Ndinu milungu yathu,”+Adzathawa ndipo adzachita manyazi kwambiri. 18  Inu amene muli ndi vuto losamva, mvetserani.Inu amene muli ndi vuto losaona, yangʼanani kuti muone.+ 19  Kodi pali winanso amene ali ndi vuto losaona ngati mtumiki wanga,Amene ali ndi vuto losamva ngati munthu amene ndamutuma kukapereka uthenga? Kodi ndi ndani amene ali ndi vuto losaona ngati munthu amene wapatsidwa mphoto,Amene saona ngakhale pangʼono ngati mtumiki wa Yehova?+ 20  Umaona zinthu zambiri, koma sukhala tcheru. Umatsegula makutu ako koma sumvetsera.+ 21  Chifukwa cha chilungamo chake,Yehova akufunitsitsa kusonyeza kuti malamulo* ake ndi apamwamba komanso aulemerero. 22  Koma awa ndi anthu amene katundu wawo wabedwa komanso kulandidwa.+Onse agwera mʼmaenje amene sangathe kutulukamo ndipo atsekeredwa mʼndende.+ Iwo atengedwa popanda wowapulumutsa,+Agwidwa popanda wonena kuti: “Bwererani nawo!” 23  Ndi ndani pakati panu amene adzamvetsere zinthu zimenezi? Ndi ndani amene adzatchere khutu ndi kumvetsera zinthu zimene zidzamuthandize mʼtsogolo? 24  Ndi ndani wachititsa kuti Yakobo alandidwe katundu wakeNdiponso kupereka Isiraeli kwa anthu olanda? Kodi si Yehova amene iwo amuchimwira? Iwo anakana kuyenda mʼnjira zake,Ndipo sanamvere malamulo* ake.+ 25  Choncho Mulungu anapitiriza kuwakhuthulira ukali ndi mkwiyo wake,Anawabweretsera nkhondo yoopsa.+ Moto unapsereza chilichonse chimene anali nacho, koma iwo sanalabadire.+ Motowo unapitiriza kuwawotcha koma iwo sizinawakhudze.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malangizo ake.”
Kapena kuti, “mphamvu ya moyo.”
Kapena kuti, “mayiko amʼmbali mwa nyanja.”
Kapena kuti, “zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Kapena kuti, “malangizo.”