Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Yesaya

Machaputala

Mitu

  • 1

    • Bambo ndi ana ake opanduka (1-9)

    • Yehova amadana ndi kumulambira mwamwambo (10-17)

    • “Tiyeni tikambirane” (18-20)

    • Ziyoni adzabwezeretsedwa kukhala mzinda wokhulupirika (21-31)

  • 2

    • Phiri la Yehova lakwezedwa (1-5)

      • Adzasula malupanga kukhala makasu a pulawo (4)

    • Anthu odzikweza adzachititsidwa manyazi pa tsiku la Yehova (6-22)

  • 3

    • Atsogoleri a Yuda akusocheretsa anthu (1-15)

    • Kuweruzidwa kwa ana aakazi a Ziyoni amene amakopa amuna (16-26)

  • 4

    • Akazi 7 mwamuna mmodzi (1)

    • Chinthu chimene Yehova adzachiphukitse chidzakhala chaulemerero (2-6)

  • 5

    • Nyimbo yonena za munda wa mpesa wa Yehova (1-7)

    • Masoka amene anagwera munda wa mpesa wa Yehova (8-24)

    • Mulungu anakwiyira anthu ake (25-30)

  • 6

    • Masomphenya okhudza Yehova ali mʼkachisi wake (1-4)

      • “Woyera, woyera, woyera ndi Yehova” (3)

    • Milomo ya Yesaya inayeretsedwa (5-7)

    • Yesaya anapatsidwa utumiki (8-10)

      • “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (8)

    • “Mpaka liti, inu Yehova?” (11-13)

  • 7

    • Uthenga wopita kwa Mfumu Ahazi (1-9)

      • Seari-yasubu (3)

    • Chizindikiro cha Emanueli (10-17)

    • Mavuto obwera chifukwa cha kusakhulupirika (18-25)

  • 8

    • Kuukiridwa ndi Asuri (1-8)

      • Maheri-salala-hasi-bazi (1-4)

    • Musachite mantha⁠—“Mulungu ali nafe” (9-17)

    • Yesaya ndi ana ake anali ngati zizindikiro (18)

    • Muzifufuza chilamulo, osati kufunsira kwa ziwanda (19-22)

  • 9

    • Anthu a ku Galileya anaona kuwala kwakukulu (1-7)

      • Kubadwa kwa “Kalonga Wamtendere” (6, 7)

    • Dzanja la Mulungu lidzaukira Isiraeli (8-21)

  • 10

    • Dzanja la Mulungu lidzaukira Isiraeli (1-4)

    • Asuri⁠—​Ndodo yosonyezera mkwiyo wa Mulungu (5-11)

    • Kulangidwa kwa Asuri (12-19)

    • Otsala a Yakobo adzabwerera (20-27)

    • Mulungu adzaweruza Asuri (28-34)

  • 11

    • Ulamuliro wolungama wa nthambi ya Jese (1-10)

      • Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa (6)

      • Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova (9)

    • Otsala adzabwerera kwawo (11-16)

  • 12

    • Nyimbo yosonyeza kuyamikira (1-6)

      • “Ya, Yehova ndi mphamvu zanga” (2)

  • 13

    • Uthenga wokhudza Babulo (1-22)

      • Tsiku la Yehova lili pafupi (6)

      • Amedi adzaukira Babulo (17)

      • MʼBabulo simudzakhalanso anthu (20)

  • 14

    • Isiraeli adzakhala mʼdziko lake (1, 2)

    • Kunyozedwa kwa mfumu ya Babulo (3-23)

      • Wonyezimira adzagwa kuchokera kumwamba (12)

    • Dzanja la Yehova lidzaphwanya Asuri (24-27)

    • Uthenga wokhudza Filisitiya (28-32)

  • 15

    • Uthenga wokhudza Mowabu (1-9)

  • 16

    • Uthenga wokhudza Mowabu ukupitirira (1-14)

  • 17

    • Uthenga wokhudza Damasiko (1-11)

    • Yehova adzadzudzula mitundu ya anthu (12-14)

  • 18

    • Uthenga wokhudza Itiyopiya (1-7)

  • 19

    • Uthenga wokhudza Iguputo (1-15)

    • Aiguputo adzadziwa Yehova (16-25)

      • Mu Iguputo mudzakhala guwa lansembe la Yehova (19)

  • 20

    • Chizindikiro chochenjeza Iguputo ndi Itiyopiya (1-6)

  • 21

    • Uthenga wokhudza chipululu chimene chili ngati nyanja (1-10)

      • Kulondera pansanja ya mlonda (8)

      • “Babulo wagwa!” (9)

    • Uthenga wokhudza Duma komanso chipululu (11-17)

      • “Mlonda, kodi kwatsala nthawi yaitali bwanji kuti kuche?” (11)

  • 22

    • Uthenga wokhudza Chigwa cha Masomphenya (1-14)

    • Eliyakimu analowa mʼmalo mwa Sebina yemwe anali kapitawo (15-25)

      • Chikhomo chophiphiritsa (23-25)

  • 23

    • Uthenga wokhudza Turo (1-18)

  • 24

    • Yehova adzachotsa anthu onse mʼdziko (1-23)

      • Yehova ndi Mfumu mu Ziyoni (23)

  • 25

    • Anthu a Mulungu adzadalitsidwa kwambiri (1-12)

      • Phwando la Yehova la vinyo wabwino kwambiri (6)

      • Imfa sidzakhalaponso (8)

  • 26

    • Nyimbo yonena za kudalira Yehova komanso chipulumutso (1-21)

      • Ya, Yehova ndi Thanthwe lamuyaya (4)

      • Anthu apadziko lapansi adzaphunzira chilungamo (9)

      • “Anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo” (19)

      • Lowani mʼzipinda zanu zamkati nʼkukabisala (20)

  • 27

    • Leviyatani adzaphedwa ndi Yehova (1)

    • Nyimbo yosonyeza kuti Isiraeli ndi munda wa mpesa (2-13)

  • 28

    • Tsoka kwa zidakwa za ku Efuraimu (1-6)

    • Ansembe ndi aneneri a ku Yuda akuyenda modzandira (7-13)

    • “Pangano ndi Imfa” (14-22)

      • Mwala wapakona wamtengo wapatali mu Ziyoni (16)

      • Ntchito yachilendo ya Yehova (21)

    • Chitsanzo chosonyeza kuti malangizo a Yehova ndi anzeru (23-29)

  • 29

    • Tsoka kwa Ariyeli! (1-16)

      • Mulungu sasangalala ndi kumulambira ndi pakamwa pokha (13)

    • Amene ali ndi vuto losamva adzamva ndipo amene ali ndi vuto losaona adzaona (17-24)

  • 30

    • Thandizo lochokera ku Iguputo ndi losathandiza ngakhale pangʼono (1-7)

    • Anthu anakana uthenga waulosi (8-14)

    • Mudzakhala amphamvu mukamadalira Mulungu (15-17)

    • Yehova amakomera mtima anthu ake (18-26)

      • Yehova ndi Mlangizi Wamkulu (20)

      • “Njira ndi iyi” (21)

    • Yehova adzapereka chilango kwa Asuri (27-33)

  • 31

    • Thandizo lenileni limachokera kwa Mulungu, osati kwa anthu (1-9)

      • Mahatchi a ku Iguputo ndi zinyama (3)

  • 32

    • Mfumu ndi akalonga adzalamulira mwachilungamo chenicheni (1-8)

    • Chenjezo kwa akazi ochita zinthu motayirira (9-14)

    • Adzadalitsidwa akadzalandira mzimu (15-20)

  • 33

    • Chiweruzo komanso chiyembekezo kwa anthu olungama (1-24)

      • Yehova ndi Woweruza, Wotipatsa Malamulo komanso Mfumu (22)

      • Palibe amene adzanene kuti: “Ine ndikudwala” (24)

  • 34

    • Yehova adzabwezera mitundu ya anthu (1-4)

    • Edomu adzakhala bwinja (5-17)

  • 35

    • Paradaiso adzabwezeretsedwa (1-7)

      • Amene ali ndi vuto losaona adzaona, amene ali ndi vuto losamva adzamva (5)

    • Msewu Wopatulika wa anthu owomboledwa (8-10)

  • 36

    • Senakeribu anapita kukachita nkhondo ndi Yuda (1-3)

    • Rabisake ananyoza Yehova (4-22)

  • 37

    • Hezekiya anapempha thandizo kwa Mulungu kudzera mwa Yesaya (1-7)

    • Senakeribu anaopseza Yerusalemu (8-13)

    • Pemphero la Hezekiya (14-20)

    • Yesaya anapereka yankho lochokera kwa Mulungu (21-35)

    • Mngelo anapha Asuri 185,000 (36-38)

  • 38

    • Kudwala kwa Hezekiya komanso kuchira kwake (1-22)

      • Nyimbo yosonyeza kuyamikira (10-20)

  • 39

    • Amithenga ochokera ku Babulo (1-8)

  • 40

    • Uthenga wolimbikitsa wopita kwa anthu a Mulungu (1-11)

      • Mawu anamveka mʼchipululu (3-5)

    • Mulungu ndi wamkulu (12-31)

      • Mitundu ya anthu ili ngati dontho lamadzi lochokera mumtsuko (15)

      • Mulungu amakhala pamwamba “pa dziko lapansi lomwe ndi lozungulira” (22)

      • Nyenyezi iliyonse amaiitana poitchula dzina lake (26)

      • Mulungu satopa (28)

      • Amene amayembekezera Yehova amapezanso mphamvu (29-31)

  • 41

    • Amene adzawagonjetse adzachokera kotulukira dzuwa (1-7)

    • Isiraeli anasankhidwa kuti akhale mtumiki wa Mulungu (8-20)

      • “Mnzanga Abulahamu” (8)

    • Milungu ina ndi yosathandiza (21-29)

  • 42

    • Mtumiki wa Mulungu komanso ntchito imene wapatsidwa (1-9)

      • ‘Dzina langa ndi Yehova’ (8)

    • Nyimbo yatsopano yotamanda Yehova (10-17)

    • Isiraeli ali ndi vuto losaona komanso losamva (18-25)

  • 43

    • Yehova akusonkhanitsanso anthu ake (1-7)

    • Milungu ikuyesedwa (8-13)

      • “Inu ndinu mboni zanga” (10, 12)

    • Kumasulidwa kuchoka ku Babulo (14-21)

    • “Tiye tiimbane mlandu” (22-28)

  • 44

    • Anthu osankhidwa a Mulungu adzadalitsidwa (1-5)

    • Palibe Mulungu wina kupatulapo Yehova (6-8)

    • Mafano opangidwa ndi munthu ndi opanda pake (9-20)

    • Yehova, Wowombola Isiraeli (21-23)

    • Yerusalemu adzamangidwanso kudzera mwa Koresi (24-28)

  • 45

    • Koresi anadzozedwa kuti agonjetse Babulo (1-8)

    • Dongo silikuyenera kulimbana ndi Woliumba (9-13)

    • Anthu a mitundu ina anazindikira Isiraeli (14-17)

    • Mulungu ndi wodalirika polenga zinthu komanso poulula zamʼtsogolo (18-25)

      • Dziko lapansi linalengedwa kuti anthu azikhalamo (18)

  • 46

    • Mafano a Ababulo sangafanane ndi Mulungu wa Isiraeli (1-13)

      • Yehova amaneneratu zamʼtsogolo (10)

      • Mbalame yodya nyama yochokera kotulukira dzuwa (11)

  • 47

    • Kugwa kwa Babulo (1-15)

      • Anthu okhulupirira nyenyezi ndi osathandiza (13-15)

  • 48

    • Isiraeli anadzudzulidwa komanso kuyeretsedwa (1-11)

    • Yehova adzalanga Babulo (12-16a)

    • Zimene Mulungu amatiphunzitsa nʼzopindulitsa (16b-19)

    • “Tulukani mʼBabulo!” (20-22)

  • 49

    • Ntchito ya mtumiki wa Yehova (1-12)

      • Kuwala kwa mitundu ya anthu (6)

    • Uthenga wotonthoza wopita kwa Isiraeli (13-26)

  • 50

    • Kuchimwa kwa Isiraeli kunayambitsa mavuto (1-3)

    • Mtumiki womvera wa Yehova (4-11)

      • Lilime ndi khutu la anthu ophunzitsidwa bwino (4)

  • 51

    • Ziyoni adzabwezeretsedwa nʼkukhala ngati munda wa Edeni (1-8)

    • Mawu olimbikitsa ochokera kwa amene anapanga Ziyoni yemwe ndi wamphamvu (9-16)

    • Kapu ya mkwiyo wa Yehova (17-23)

  • 52

    • Dzuka, iwe Ziyoni!! (1-12)

      • Mapazi a munthu amene akubweretsa uthenga wabwino ndi okongola (7)

      • Alonda a mu Ziyoni akufuula pamodzi (8)

      • Amene akunyamula ziwiya za Yehova ayenera kukhala oyera (11)

    • Mtumiki wa Yehova adzalemekezedwa (13-15)

      • Maonekedwe ake anasintha (14)

  • 53

    • Kuvutika, imfa komanso kuikidwa mʼmanda kwa mtumiki wa Yehova (1-12)

      • Ananyozedwa komanso kupewedwa (3)

      • Ananyamula matenda ndi zowawa (4)

      • “Anamutengera kumalo oti akamuphere ngati nkhosa” (7)

      • Ananyamula tchimo la anthu ambiri  (12)

  • 54

    • Ziyoni yemwe ndi wosabereka adzakhala ndi ana ambiri (1-17)

      • Yehova, mwamuna wa Ziyoni (5)

      • Ana a Ziyoni azidzaphunzitsidwa ndi Yehova (13)

      • Zida zoti zivulaze Ziyoni sizidzapambana (17)

  • 55

    • Kuitanidwa kuti adzadye ndi kumwa kwaulere (1-5)

    • Funafunani Yehova komanso mawu ake omwe ndi odalirika (6-13)

      • Njira za Mulungu nʼzapamwamba kuposa za anthu (8, 9)

      • Mawu a Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake (10, 11)

  • 56

    • Mlendo komanso munthu wofulidwa adzadalitsidwa (1-8)

      • Nyumba yopemphereramo anthu onse (7)

    • Alonda akhungu, agalu opanda mawu (9-12)

  • 57

    • Wolungama komanso anthu okhulupirika awonongedwa (1, 2)

    • Uhule wauzimu wa Isiraeli waonekera (3-13)

    • Uthenga wotonthoza wopita kwa anthu onyozeka (14-21)

      • Anthu oipa ali ngati nyanja imene ikuchita mafunde (20)

      • Oipa alibe mtendere (21)

  • 58

    • Kusala kudya koyenera komanso kwachinyengo (1-12)

    • Kusangalala posunga Sabata (13, 14)

  • 59

    • Kuchimwa kwa Isiraeli kunachititsa kuti atalikirane ndi Mulungu (1-8)

    • Kuulula machimo (9-15a)

    • Yehova anathandiza anthu amene analapa (15b-21)

  • 60

    • Ulemerero wa Yehova ukuunikira Ziyoni (1-22)

      • Ngati nkhunda zimene zikuulukira mʼmakola awo (8)

      • Golide mʼmalo mwa kopa (17)

      • Wamngʼono adzasanduka anthu 1,000 (22)

  • 61

    • Anadzozedwa kuti alengeze uthenga wabwino (1-11)

      • “Chaka cha Yehova chokomera anthu mtima” (2)

      • “Mitengo ikuluikulu ya chilungamo” (3)

      • Alendo azidzawathandiza (5)

      • “Ansembe a Yehova” (6)

  • 62

    • Dzina latsopano la Ziyoni (1-12)

  • 63

    • Yehova adzabwezera mitundu ya anthu (1-6)

    • Chikondi chokhulupirika cha Yehova nthawi yakale (7-14)

    • Pemphero losonyeza kulapa (15-19)

  • 64

    • Pemphero losonyeza kulapa likupitirira (1-12)

      • Yehova ndi “Wotiumba” (8)

  • 65

    • Yehova adzalanga anthu olambira mafano (1-16)

      • Mulungu wa Mwayi komanso mulungu wa Zokonzedweratu (11)

      • “Atumiki anga adzadya” (13)

    • Kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano (17-25)

      • Kumanga nyumba; kudzala minda ya mpesa (21)

      • Palibe amene adzagwire ntchito mwakhama pachabe (23)

  • 66

    • Kulambira koona komanso kwabodza (1-6)

    • Ziyoni ndi ana ake amuna (7-17)

    • Anthu adzasonkhana mu Yerusalemu kuti alambire (18-24)