Yesaya 2:1-22

  • Phiri la Yehova lakwezedwa (1-5)

    • Adzasula malupanga kukhala makasu a pulawo (4)

  • Anthu odzikweza adzachititsidwa manyazi pa tsiku la Yehova (6-22)

2  Izi ndi zimene Yesaya mwana wa Amozi anaona zokhudza Yuda ndi Yerusalemu:+   Mʼmasiku otsiriza,Phiri la nyumba ya YehovaLidzakhazikika pamwamba penipeni pa mapiri akuluakulu,+Ndipo lidzakwezedwa kupitirira mapiri angʼonoangʼono.Anthu a mitundu yonse adzapita kumeneko.+   Anthu ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana adzabwera nʼkunena kuti: “Bwerani. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova,Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+ Iye akatiphunzitsa njira zake,Ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.”+ Chifukwa chilamulo chidzaphunzitsidwa* mu Ziyoni,Ndipo mawu a Yehova adzaphunzitsidwa mu Yerusalemu.+   Mulungu adzaweruza anthu a mitundu yosiyanasiyanaNdipo adzakonza zinthu zimene ndi zolakwika pakati pawo. Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo,Ndipo mikondo yawo adzaisula kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake,Ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+   Inu a mʼnyumba ya Yakobo bwerani,Tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.+   Inu mwasiya anthu anu, nyumba ya Yakobo,+Chifukwa iwo ayamba kutsatira miyambo yambiri ya Kumʼmawa.Akuchita zamatsenga+ ngati AfilisitiNdiponso ali ndi ana ambiri a alendo.   Dziko lawo ladzaza ndi siliva komanso golide,Ndipo ali ndi chuma chopanda malire. Dziko lawo ladzaza ndi mahatchi,Ndipo ali ndi magaleta osawerengeka.+   Dziko lawo ladzaza ndi milungu yopanda phindu.+ Iwo amagwadira ntchito ya manja awo,Amagwadira chinthu chimene zala zawo zapanga.   Choncho anthu agwada, anyozeka,Ndipo simungawakhululukire. 10  Lowani muthanthwe ndipo mubisale mufumbiChifukwa cha kuopsa kwa mkwiyo wa Yehova,Ndiponso chifukwa cha ulemerero wake waukulu.+ 11  Maso odzikuza a munthu adzatsitsidwa,Ndipo anthu odzikweza adzachititsidwa manyazi. Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe tsiku limenelo. 12  Chifukwa ndi tsiku la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+ Tsikulo lidzafikira aliyense wodzitukumula ndi wodzikweza,Lidzafikira aliyense kaya ndi wolemekezeka kapena wonyozeka,+ 13  Lidzafikira mikungudza yonse ya ku Lebanoni yomwe ndi yonyada komanso yodzikweza.Lidzafikiranso mitengo ikuluikulu yonse ya ku Basana, 14  Lidzafikira mapiri onse akuluakulu odzikwezaNdi mapiri onse angʼonoangʼono okwezeka, 15  Lidzafikiranso nsanja iliyonse yaitali ndi mpanda uliwonse wolimba kwambiri, 16  Lidzafikira sitima zonse zapamadzi za ku Tarisi+Ndi ngalawa zonse zabwinozabwino. 17  Munthu wodzikuza adzatsitsidwa,Ndipo anthu odzikweza adzachititsidwa manyazi. Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe tsiku limenelo. 18  Milungu yopanda phindu idzatheratu.+ 19  Anthu adzalowa mʼmapanga a muthanthweNdiponso mʼmayenje a munthaka,+Chifukwa cha kuopsa kwa mkwiyo wa YehovaNdiponso chifukwa cha ulemerero wake waukulu+Akaimirira kuti achititse dziko lapansi kunjenjemera ndi mantha. 20  Pa tsiku limenelo, anthu adzatenga milungu yawo yopanda pake yasiliva ndi yagolide,Imene anaipanga kuti aziigwadiraNdipo adzaitayira kumene kumakhala aswiswiri* ndi mileme,+ 21  Kuti abisale mʼmayenje a mʼmatanthweNdi mʼmingʼalu ya mʼmiyala ikuluikulu,Chifukwa cha kuopsa kwa mkwiyo wa YehovaNdiponso chifukwa cha ulemerero wake waukuluAkaimirira kuti achititse dziko lapansi kunjenjemera ndi mantha. 22  Kuti zinthu zikuyendereni bwino, siyani kudalira munthu wamba,Amene ali ngati mpweya chabe wa mʼmphuno mwake. Kodi pali chifukwa chilichonse choti munthu azimudalira?

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malangizo adzaphunzitsidwa.”
Ena amati suntche.