Wolembedwa ndi Mateyu 20:1-34

  • Anthu amene ankagwira ntchito mʼmunda wampesa analandira malipiro ofanana (1-16)

  • Yesu ananeneratunso zokhudza imfa yake (17-19)

  • Anapempha kuti adzapatsidwe malo apadera mu Ufumu (20-28)

    • Yesu anapereka dipo kuwombola anthu ambiri (28)

  • Amuna awiri osaona anachiritsidwa (29-34)

20  “Ufumu wakumwamba uli ngati munthu amene anali ndi munda wa mpesa, amene analawirira mʼmawa kwambiri kukafuna anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa.+  Aganyu amenewa atagwirizana nawo kuti aziwapatsa ndalama ya dinari* imodzi pa tsiku, anawatumiza kumunda wake wa mpesa.  Cha mʼma 9 koloko mʼmawa* anapitanso kukafuna anthu ena, ndipo anaona ena atangoimaima pamsika alibe chochita.  Amenewonso anawauza kuti, ‘Inunso kagwireni ntchito mʼmunda wa mpesa. Ndidzakupatsani malipiro oyenerera.’  Choncho iwo anapita. Cha mʼma 12 koloko ndi 3 koloko masana,* mwinimunda uja anapitanso kukachita chimodzimodzi.  Pamapeto pake, cha mʼma 5 koloko madzulo* anapitanso ndipo anakapeza ena atangoimaima. Iye anawafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwangoimaima pano tsiku lonse osagwira ntchito?’  Iwo anamuyankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba ganyu.’ Iye anawauza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito kumunda wanga wa mpesa.’  Madzulowo, mwiniwake wa munda wa mpesa uja anauza kapitawo wake kuti, ‘Itana antchito aja uwapatse malipiro awo,+ kuyambira omalizira, kutsiriza ndi oyambirira.’  Anthu amene anayamba ntchito 5 koloko aja atafika, aliyense analandira dinari* imodzi. 10  Choncho oyambirira aja atafika, anaganiza kuti alandira zambiri, koma nawonso malipiro amene analandira anali dinari* imodzi. 11  Atalandira, anayamba kudandaulira mwiniwake wa munda wa mpesa uja 12  kuti, ‘Omalizirawa agwira ntchito ola limodzi lokha, koma mwawapatsa malipiro ofanana ndi ife amene tagwira ntchito yakalavulagaga tsiku lonse padzuwa lotentha!’ 13  Koma poyankha kwa mmodzi wa iwo, mwinimundayo anati, ‘Bwanawe, sindinakulakwire. Tinapangana malipiro a dinari* imodzi, si choncho?+ 14  Ingolandira malipiro ako uzipita. Ndikufuna kupatsa womalizirayu malipiro ofanana ndi amene ndapereka kwa iwe. 15  Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi zinthu zanga? Kapena kodi diso lako lachita njiru* chifukwa chakuti ndine wabwino?’*+ 16  Choncho omalizira adzakhala oyambirira ndipo oyambirira adzakhala omalizira.”+ 17  Ali panjira yopita ku Yerusalemu, Yesu anatengera pambali ophunzira ake 12 aja nʼkuwauza kuti:+ 18  “Tsopano tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi. Iwo akamuweruza kuti aphedwe+ 19  ndipo akamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amuchitire chipongwe, kumukwapula ndi kumupachika pamtengo+ ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ 20  Kenako mkazi wa Zebedayo+ anafika kwa Yesu ndi ana ake aamuna ndipo anamugwadira nʼkumupempha kanthu kena.+ 21  Iye anafunsa mayiyo kuti: “Mukufuna chiyani?” Mayiyo anayankha kuti: “Lonjezani kuti ana anga aamuna awiriwa, mmodzi adzakhale kudzanja lanu lamanja, wina kudzanja lanu lamanzere mu Ufumu wanu.”+ 22  Yesu anayankha kuti: “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwe zimene ine ndatsala pangʼono kumwa?”+ Iwo anayankha kuti: “Inde tingamwe.” 23  Iye anawauza kuti: “Inde mudzamwadi zimene ndatsala pangʼono kumwa.+ Koma si ine woyenera kusankha amene adzakhale kudzanja langa lamanja kapena lamanzere. Atate wanga adzapereka mwayi umenewo kwa amene anawakonzera.”+ 24  Ophunzira 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndi amuna awiri apachibalewo.+ 25  Koma Yesu anawaitana nʼkuwauza kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira a anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo.+ 26  Sizikuyenera kukhala choncho pakati panu.+ Koma aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu+ 27  ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wanu.+ 28  Izi zikufanana ndi zimene Mwana wa munthu anachita. Iye sanabwere kudzatumikiridwa koma kudzatumikira+ ndi kudzapereka moyo wake dipo* kuti awombole anthu ambiri.”+ 29  Pamene iwo ankatuluka mu Yeriko, gulu lalikulu la anthu linamutsatira. 30  Ndiyeno amuna awiri amene anali ndi vuto losaona anakhala pansi mʼmphepete mwa msewu ndipo atamva kuti Yesu akudutsa, anafuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”+ 31  Ndiye gulu la anthulo linawakalipira nʼkuwauza kuti akhale chete. Koma mʼpamene iwo anafuula kwambiri kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!” 32  Choncho Yesu anaima, ndipo anawaitana nʼkuwafunsa kuti: “Mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” 33  Iwo anamuyankha kuti: “Ambuye, tithandizeni kuti tiyambe kuona.” 34  Atagwidwa ndi chifundo, Yesu anagwira maso awo.+ Nthawi yomweyo anthu amene anali ndi vuto losaonawo anayamba kuona ndipo anamutsatira.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6 ndi ola la 9,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 11,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi loipa.”
Kapena kuti, “wowolowa manja.”