Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 5:1-14

  • Mpukutu umene anaumata ndi zidindo 7 (1-5)

  • Mwanawankhosa anatenga mpukutuwo (6-8)

  • Mwanawankhosa ndi woyenera kumatula zidindozo (9-14)

5  Kenako ndinaona mpukutu umene unalembedwa mbali zonse,* uli mʼdzanja lamanja la Mulungu amene anakhala pampando wachifumu.+ Mpukutuwo anaumata molimba ndi zidindo 7 zomatira.  Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti: “Ndi ndani ali woyenera kumatula zidindo zimene amatira mpukutuwu nʼkuutsegula?”  Koma panalibe aliyense kaya kumwamba, padziko lapansi kapena pansi pa nthaka, amene anatha kutsegula mpukutuwo kapena kuyangʼanamo ndi kuuwerenga.  Choncho ndinalira kwambiri chifukwa sipanapezeke wina aliyense woyenera kutsegula mpukutuwo kapena kuyangʼanamo nʼkuuwerenga.  Koma mmodzi wa akulu aja anandiuza kuti: “Tonthola. Taona! Mkango wa fuko la Yuda,+ muzu+ wa Davide,+ anapambana pankhondo+ moti ndi woyenera kumatula zidindo 7 zimene amatira mpukutuwo nʼkuutsegula.”  Kenako ndinaona mwana wa nkhosa+ amene ankaoneka ngati waphedwa,+ ataimirira pakati pa mpando wachifumu ndi angelo 4 aja komanso pakati pa akulu aja.+ Iye anali ndi nyanga 7 ndiponso maso 7. Maso amenewa akuimira mizimu 7 ya Mulungu,+ imene yatumizidwa padziko lonse lapansi.  Nthawi yomweyo iye anapita nʼkukatenga mpukutu umene unali mʼdzanja lamanja la Mulungu amene anakhala pampando wachifumu.+  Atatenga mpukutuwo, angelo 4 ndi akulu 24 aja+ anagwada nʼkuwerama pamaso pa Mwanawankhosa. Aliyense wa iwo anali ndi zeze komanso mbale yagolide yodzaza ndi zofukiza. (Zofukizazo zikuimira mapemphero a oyera.)+  Iwo ankaimba nyimbo yatsopano+ yakuti: “Inu ndinu woyenera kutenga mpukutuwo ndi kumatula zidindo zake zomatira, chifukwa munaphedwa ndipo ndi magazi anu munagula anthu kuti atumikire Mulungu.+ Anthuwo ndi ochokera mu fuko lililonse, chilankhulo chilichonse, mtundu uliwonse ndi dziko lililonse.+ 10  Ndipo munawapanga kuti akhale mafumu+ ndi ansembe a Mulungu wathu,+ moti adzakhala mafumu+ olamulira dziko lapansi.” 11  Kenako, ndinaona ndi kumva mawu a angelo ambiri atazungulira mpando wachifumu limodzi ndi angelo 4 komanso akulu aja. Chiwerengero chawo chinali 10 sauzande kuchulukitsa ndi 10 sauzande* ndiponso mamiliyoni kuchulukitsa ndi masauzande.+ 12  Iwo ankanena mofuula kuti: “Mwanawankhosa amene anaphedwa+ ndi woyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi madalitso.”+ 13  Ndipo cholengedwa chilichonse chakumwamba, padziko lapansi, pansi pa nthaka,+ panyanja, ndi zinthu zonse zammenemo, ndinazimva zikunena kuti: “Mulungu amene wakhala pampando wachifumu+ komanso Mwanawankhosa,+ atamandidwe, alandire ulemu,+ ulemerero komanso mphamvu mpaka kalekale.”+ 14  Ndiyeno angelo 4 aja ankanena kuti: “Ame!” Ndipo akulu aja ankagwada nʼkuwerama ndi kulambira Mulungu.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mkati ndi kunja komwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “miyanda kuchulukitsa ndi miyanda.”