Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Chivumbulutso

Machaputala

Mitu

  • 1

    • Chivumbulutso chochokera kwa Mulungu, kudzera mwa Yesu (1-3)

    • Moni wopita kumipingo 7 (4-8)

      • “Ine ndine Alefa ndi Omega” (8)

    • Atadzazidwa ndi mzimu woyera, Yohane anapezeka kuti ali mʼtsiku la Ambuye (9-11)

    • Masomphenya a Yesu, atalandira ulemerero (12-20)

  • 2

    • Mauthenga opita ku Efeso (1-7), ku Simuna (8-11), ku Pegamo (12-17), ku Tiyatira (18-29)

  • 3

    • Mauthenga opita ku Sade (1-6), ku Filadefiya (7-13), ku Laodikaya (14-22)

  • 4

    • Masomphenya a Yehova ali kumwamba (1-11)

      • Yehova wakhala pampando wake wachifumu (2)

      • Akulu 24 akhala pamipando yachifumu (4)

      • Angelo 4 (6)

  • 5

    • Mpukutu umene anaumata ndi zidindo 7 (1-5)

    • Mwanawankhosa anatenga mpukutuwo (6-8)

    • Mwanawankhosa ndi woyenera kumatula zidindozo (9-14)

  • 6

    • Mwanawankhosa anamatula zidindo 6 zoyambirira (1-17)

      • Wogonjetsa adani anakwera pahatchi yoyera (1, 2)

      • Amene anakwera pahatchi yofiira ngati moto analoledwa kuchotsa mtendere (3, 4)

      • Amene anakwera pahatchi yakuda anabweretsa njala (5, 6)

      • Amene anakwera pahatchi yotuwa dzina lake ndi Imfa (7, 8)

      • Pansi pa guwa lansembe panali anthu amene anaphedwa (9-11)

      • Chivomerezi chachikulu (12-17)

  • 7

    • Angelo 4 anagwira mphepo kuti zisawononge (1-3)

    • Anthu okwana 144,000 anaikidwa chidindo (4-8)

    • Khamu lalikulu limene lavala mikanjo yoyera (9-17)

  • 8

    • Anamatula chidindo cha 7 (1-6)

    • Kuliza malipenga 4 oyambirira (7-12)

    • Analengeza zokhudza masoka atatu (13)

  • 9

    • Lipenga la 5 (1-11)

    • Tsoka limodzi lapita, masoka ena awiri akubwera (12)

    • Lipenga la 6 (13-21)

  • 10

    • Mngelo wamphamvu amene anali ndi mpukutu waungʼono (1-7)

      • “Nthawi yodikira yatha” (6)

      • Chinsinsi chopatulika chidzakwaniritsidwa (7)

    • Yohane anadya mpukutu waungʼono (8-11)

  • 11

    • Mboni ziwiri (1-13)

      • Zinanenera kwa masiku 1,260 zitavala ziguduli (3)

      • Zinaphedwa koma sizinaikidwe mʼmanda (7-10)

      • Zinakhalanso ndi moyo patatha masiku atatu ndi hafu (11, 12)

    • Tsoka lachiwiri lapita, tsoka lachitatu likubwera (14)

    • Lipenga la 7 (15-19)

      • Ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake (15)

      • Amene akuwononga dziko lapansi adzawonongedwa (18)

  • 12

    • Mkazi, mwana wamwamuna ndi chinjoka (1-6)

    • Mikayeli anamenyana ndi chinjoka (7-12)

      • Chinjoka chinaponyedwa padziko lapansi (9)

      • Mdyerekezi akudziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa (12)

    • Chinjoka chinazunza mkazi (13-17)

  • 13

    • Chilombo cha mitu 7 chinatuluka mʼnyanja (1-10)

    • Chilombo cha nyanga ziwiri chinatuluka pansi (11-13)

    • Chifaniziro cha chilombo cha mitu 7 (14, 15)

    • Chizindikiro komanso nambala ya chilombo (16-18)

  • 14

    • Mwanawankhosa ndi enanso 144,000 (1-5)

    • Mauthenga ochokera kwa angelo atatu (6-12)

      • Mngelo amene ali ndi uthenga wabwino, akuuluka mumlengalenga (6, 7)

    • Osangalala ndi anthu amene akufa ali ogwirizana ndi Khritsu (13)

    • Anakolola mpesa kawiri padziko lapansi (14-20)

  • 15

    • Angelo 7 amene anali ndi miliri 7 (1-8)

      • Nyimbo ya Mose komanso ya Mwanawankhosa (3, 4)

  • 16

    • Mbale 7 za mkwiyo wa Mulungu (1-21)

      • Anathira padziko lapansi (2), mʼnyanja (3), pamitsinje ndi pa akasupe (4-7), padzuwa (8, 9), pampando wachifumu wa chilombo (10, 11), pa Firate (12-16) ndi pampweya (17-21)

      • Nkhondo ya Mulungu pa Aramagedo (14, 16)

  • 17

    • Chiweruzo cha “Babulo Wamkulu” (1-18)

      • Hule lalikulu lakhala pachilombo chofiira kwambiri (1-3)

      • Chilombo chimene ‘chinalipo, panopa kulibe, koma chidzatuluka kuphompho’ (8)

      • Nyanga 10 zidzamenyana ndi Mwanawankhosa (12-14)

      • Nyanga 10 zidzadana ndi hule (16, 17)

  • 18

    • Kugwa kwa “Babulo Wamkulu” (1-8)

      • “Tulukani mwa iye anthu anga” (4)

    • Kulirira Babulo amene wagwa (9-19)

    • Kumwamba kudzakhala chisangalalo chifukwa cha kugwa kwa Babulo (20)

    • Babulo adzaponyedwa mʼnyanja ngati mwala (21-24)

  • 19

    • Tamandani Ya chifukwa cha ziweruzo zake (1-10)

      • Ukwati wa Mwanawankhosa (7-9)

    • Amene anakwera pahatchi yoyera (11-16)

    • Phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo (17, 18)

    • Chilombo chinagonjetsedwa (19-21)

  • 20

    • Satana adzamangidwa kwa zaka 1,000 (1-3)

    • Amene adzalamulire ndi Khristu kwa zaka 1,000 (4-6)

    • Satana adzamasulidwa, kenako adzawonongedwa (7-10)

    • Akufa adzaweruzidwa pamaso pa mpando wachifumu woyera (11-15)

  • 21

    • Kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano (1-8)

      • Sikudzakhalanso imfa (4)

      • Zinthu zonse zidzakhala zatsopano (5)

    • Anafotokoza zokhudza Yerusalemu watsopano (9-27)

  • 22

    • Mtsinje wa madzi amoyo (1-5)

    • Mawu omaliza (6-21)

      • ‘Bwerani! Mudzamwe madzi opatsa moyo kwaulere’ (17)

      • “Bwerani, Ambuye Yesu” (20)