Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 20:1-15

  • Satana adzamangidwa kwa zaka 1,000 (1-3)

  • Amene adzalamulire ndi Khristu kwa zaka 1,000 (4-6)

  • Satana adzamasulidwa, kenako adzawonongedwa (7-10)

  • Akufa adzaweruzidwa pamaso pa mpando wachifumu woyera (11-15)

20  Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa phompho+ ndi tcheni chachikulu mʼdzanja lake.  Kenako anagwira chinjoka,+ njoka yakale ija,+ amene ndi Mdyerekezi+ ndiponso Satana,+ nʼkumumanga kwa zaka 1,000.  Ndipo anamuponyera mʼphompho+ nʼkutseka pakhomo la phompholo kenako anaikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu mpaka zaka 1,000 zitatha. Pambuyo pake, adzamasulidwa kanthawi kochepa.+  Kenako ndinaona mipando yachifumu ndipo amene anakhala pamipandoyo anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndinaona miyoyo ya anthu amene anaphedwa chifukwa chochitira umboni za Yesu komanso chifukwa cholankhula za Mulungu. Inde, ndinaona miyoyo ya anthu amene sanalambire chilombo kapena chifaniziro chake ndipo sanalandire chizindikiro pazipumi zawo ndi padzanja lawo.+ Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu+ kwa zaka 1,000.  (Akufa enawo+ sanakhalenso ndi moyo mpaka zaka 1,000 zitatha.) Uku ndi kuuka koyamba kwa akufa.+  Wosangalala komanso woyera ndi aliyense amene akuuka nawo pa kuuka koyamba.+ Imfa yachiwiri+ ilibe ulamuliro pa amenewa.+ Koma adzakhala ansembe+ a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu zaka 1,000.+  Ndiye zaka 1,000 zimenezi zikadzangotha, Satana adzamasulidwa mʼndende yake,  ndipo adzatuluka kukasocheretsa mitundu ya anthu kumakona onse 4 a dziko lapansi. Mitunduyo ndi Gogi komanso Magogi ndipo adzaisonkhanitsa pamodzi kuti amenye nkhondo. Iwo ndi ochuluka ngati mchenga wakunyanja.  Iwo adzafalikira padziko lonse lapansi ndipo adzazungulira msasa wa oyera komanso mzinda wokondedwa. Koma moto udzatsika kuchokera kumwamba nʼkuwapsereza.+ 10  Mdyerekezi, amene ankawasocheretsa, adzaponyedwa mʼnyanja yamoto ndi sulufule, mmene muli kale chilombo+ ndi mneneri wabodza uja.+ Ndipo iwo adzazunzidwa masana ndi usiku* mpaka kalekale. 11  Kenako ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera komanso Mulungu atakhala pampandowo.+ Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake+ ndipo sizinapezekenso. 12  Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inatambasulidwa. Koma panali mpukutu wina umene unatambasulidwa, womwe ndi mpukutu wa moyo.+ Akufa anaweruzidwa potengera zimene zinalembedwa mʼmipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.+ 13  Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Imfa komanso Manda* zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense payekha anaweruzidwa mogwirizana ndi ntchito zake.+ 14  Ndipo imfa ndi Manda* zinaponyedwa mʼnyanja yamoto.+ Nyanja yamoto+ imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.+ 15  Komanso, aliyense amene dzina lake silinalembedwe mʼbuku la moyo+ anaponyedwa mʼnyanja yamoto.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “iwo adzaikidwa mʼndende.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.