Genesis 3:1-24

  • Kuchimwa kwa munthu (1-13)

    • Bodza loyamba (4, 5)

  • Chiweruzo chimene Yehova anapereka kwa opanduka (14-24)

    • Ananeneratu za mbadwa ya mkazi  (15)

    • Anathamangitsidwa mu Edeni (23, 24)

3  Tsopano njoka+ inali yochenjera kwambiri kuposa nyama zonse zakutchire zimene Yehova Mulungu anapanga. Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo kuti: “Eti nʼzoona kuti Mulungu ananena kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse wamʼmundamu?”+  Mkaziyo anayankha njokayo kuti: “Anatiuza kuti tingathe kudya zipatso za mitengo yamʼmundamu.+  Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda,+ Mulungu ananena kuti: ‘Musadye zipatso zake, ndipo musayerekeze kuukhudza, chifukwa mukatero mudzafa.’”  Kenako njokayo inauza mkaziyo kuti: “Si zoona zimenezo, simudzafa ayi.+  Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”+  Mkaziyo atamva zimenezo, anayamba kuona kuti zipatso za mtengowo nʼzokoma kudya, zosiririka komanso zooneka bwino. Choncho anathyola chipatso cha mtengowo nʼkudya.+ Kenako anatenga zina nʼkukapatsa mwamuna wake pa nthawi imene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.+  Atatero onse maso awo anatseguka ndipo anazindikira kuti ali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nʼkuwamangirira mʼchiuno mwawo.+  Pambuyo pake, iwo anamva mawu a Yehova Mulungu pamene iye ankayendayenda mʼmundamo pa nthawi imene kamphepo kayeziyezi kankaomba. Mwamuna ndi mkaziyo atamva, anabisala pakati pa mitengo ya mʼmundamo kuti Yehova Mulungu asawaone.  Koma Yehova Mulungu anapitiriza kuitana mwamunayo kuti: “Kodi uli kuti?” 10  Kenako mwamunayo anayankha kuti: “Ndinamva kuitana kwanu mʼmunda muno, koma ndinachita mantha poona kuti ndili maliseche. Choncho ndinabisala.” 11  Ndiyeno Mulungu anati: “Wakuuza ndi ndani kuti uli maliseche?+ Kodi wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti usadzadye uja?”+ 12  Mwamunayo anayankha kuti: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa chipatso cha mtengowo, ndipo ine ndadya.” 13  Ndiyeno Yehova Mulungu anafunsa mkaziyo kuti: “Ndiye chiyani wachitachi?” Mkaziyo anayankha kuti: “Njoka ndi imene yandipusitsa, ndipo ine ndadya.”+ 14  Zitatero Yehova Mulungu anauza njokayo kuti:+ “Chifukwa cha zimene wachitazi, ukhala wotembereredwa pa nyama zonse zoweta ndi zakutchire. Udzakwawa ndi mimba yako ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako. 15  Ndidzaika chidani+ pakati pa iwe+ ndi mkaziyo,+ komanso pakati pa mbadwa* yako+ ndi mbadwa yake.+ Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako,+ ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”+ 16  Ndiyeno Mulungu anauza mkaziyo kuti: “Ndidzawonjezera kwambiri kuvutika kwako pa nthawi imene uli woyembekezera. Ndipo pobereka ana udzamva ululu. Uzidzafunitsitsa kukhala ndi mwamuna wako, ndipo iye azidzakulamulira.” 17  Kenako Mulungu anauza Adamu* kuti: “Popeza wamvera mawu a mkazi wako, ndipo wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti,+ ‘Usadzadye zipatso zake,’ nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi.+ Udzavutika kulima nthakayo masiku onse a moyo wako+ kuti upeze chakudya. 18  Minga ndi zitsamba zobaya zidzamera panthaka, ndipo chakudya chako chidzakhala zomera zamʼnthaka. 19  Udzadya chakudya kuchokera mʼthukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, chifukwa nʼkumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+ 20  Pambuyo pa zimenezi, Adamu anapatsa mkazi wake dzina lakuti Hava,* chifukwa anali woti adzakhala mayi wa anthu onse.+ 21  Kenako Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zazitali zachikopa, nʼkuwaveka.+ 22  Ndiyeno Yehova Mulungu anati: “Tsopano munthu wakhala ngati ife chifukwa wadziwa zabwino ndi zoipa.+ Choncho kuti asathyolenso ndi kudya chipatso cha mtengo wa moyo,+ nʼkukhala ndi moyo mpaka kalekale,—”* 23  Atatero Yehova Mulungu anatulutsa munthuyo mʼmunda wa Edeni,+ kuti akalime nthaka imene anatengedwako.+ 24  Choncho anathamangitsa munthuyo mʼmundamo, nʼkuika akerubi+ kumʼmawa kwa munda wa Edeniwo. Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linkazungulira nthawi zonse, kutchinga njira yopita kumtengo wa moyo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.” Mawuwa mʼChiheberi angatanthauze mbewu zambiri kapena imodzi.
Kutanthauza kuti “Munthu Wochokera Kufumbi; Mtundu wa Anthu.”
Dzina limeneli limatanthauza “Wamoyo.”
Kamzere kameneka kakusonyeza kuti mawuwa anathera mʼmalere.