Wolembedwa ndi Yohane 20:1-31

  • Manda opanda kanthu (1-10)

  • Yesu anaonekera kwa Mariya wa ku Magadala (11-18)

  • Yesu anaonekera kwa ophunzira ake (19-23)

  • Tomasi anakayikira koma kenako anakhulupirira (24-29)

  • Cholinga cha mpukutuwu (30, 31)

20  Tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya wa ku Magadala anapita kumandako* mʼmawa kwambiri,+ kudakali mdima, ndipo anaona kuti mwala wachotsedwa kale pamandawo.*+  Choncho anathamanga kupita kwa Simoni Petulo ndi kwa wophunzira wina, amene Yesu ankamukonda kwambiri uja.+ Iye anawauza kuti: “Ambuye awachotsa mʼmanda*+ muja, ndipo sitikudziwa kumene awaika.”  Atatero Petulo ndi wophunzira wina uja ananyamuka kupita kumandako.  Onse awiri anayambira limodzi kuthamanga, koma wophunzira winayo ankathamanga kwambiri kuposa Petulo ndipo anali woyambirira kukafika kumandako.  Atawerama nʼkusuzumira mkatimo, anaona nsalu zili pansi,+ koma sanalowemo.  Kenako Simoni Petulo amene ankabwera mʼmbuyo mwake anafikanso, ndipo analowa mʼmandamo. Mmenemo anaona nsalu zija zili pansi.  Nsalu imene anamukulungira kumutu sinaikidwe pamodzi ndi nsalu zina zija, koma anaipindapinda nʼkuiika payokha.  Kenako wophunzira amene anayambirira kufika kumanda uja analowanso mkatimo, ndipo anaona nʼkukhulupirira zimene anauzidwa.  Iwo anali asanamvetse zimene malemba amanena kuti Yesu ayenera kuuka kwa akufa.+ 10  Choncho ophunzirawo anabwerera kunyumba kwawo. 11  Koma Mariya anatsala atangoima panja pafupi ndi mandawo, akulira. Akulira choncho, anawerama kuti aone mʼmandamo 12  ndipo anaona angelo awiri+ amene anavala zoyera atakhala pamene panali mtembo wa Yesu. Mmodzi anakhala pansi kumutu ndipo wina anakhala kumiyendo. 13  Iwo anamufunsa kuti: “Mayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?” Mayiwo anawayankha kuti: “Atenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene awaika.” 14  Atanena zimenezi, anatembenuka ndipo anaona Yesu ataima pamenepo, koma sanamuzindikire kuti ndi Yesu.+ 15  Yesu anafunsa mayiyo kuti: “Mayi iwe, nʼchifukwa chiyani ukulira? Kodi ukufuna ndani?” Poganiza kuti ndi amene ankasamalira mundawo, iye anamuyankha kuti: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika ndipo ine ndikamutenga.” 16  Yesu anamuuza kuti: “Mariya!” Iye anatembenuka nʼkumuuza mʼChiheberi kuti: “Rab·boʹni!” (kutanthauza kuti “Mphunzitsi!”) 17  Yesu anamuuza kuti: “Usandikangamire chifukwa nthawi yoti ndipite kwa Atate sinakwane. Koma pita kwa abale anga+ ndipo ukawauze kuti, ‘Ine ndikupita kwa Atate wanga+ ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga+ ndi Mulungu wanu.’” 18  Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzirawo ndipo anawauza kuti: “Ambuye ndawaona ine!” Ndipo anawauza zimene Yesu anamuuza zija.+ 19  Madzulo a tsiku limenelo, limene linali tsiku loyamba la mlungu, ophunzirawo anasonkhana pamodzi. Mʼnyumba imene anasonkhanayo anakhoma zitseko chifukwa ankaopa Ayuda. Koma Yesu analowa nʼkuima pakati pawo ndipo anawauza kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 20  Atanena zimenezi, anawaonetsa manja ake ndi munthiti mwake.+ Choncho ophunzirawo anasangalala ataona Ambuyewo.+ 21  Yesu anawauzanso kuti: “Mtendere ukhale nanu.+ Mofanana ndi mmene Atate ananditumira,+ inenso ndikukutumani.”+ 22  Atanena zimenezi, anauzira mpweya pa iwo nʼkuwauza kuti: “Landirani mzimu woyera.+ 23  Mukakhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu wamukhululukira kale. Koma mukapanda kukhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu sanamukhululukire.” 24  Koma Tomasi,+ amene ankadziwikanso kuti Didimo, mmodzi wa ophunzira 12 aja sanali nawo limodzi pamene Yesu anabwera. 25  Choncho ophunzira enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anawayankha kuti: “Ndikapanda kuona mabala a misomali mʼmanja mwawo ndi kuika chala changa mʼmabala a misomaliwo ndiponso kuika dzanja langa munthiti mwawo,+ ndithu ine sindikhulupirira.” 26  Patapita masiku 8, ophunzira akewo analinso mʼnyumba ndipo Tomasi anali nawo limodzi. Yesu analowa ngakhale kuti zitseko zinali zokhoma ndipo anaimirira pakati pawo nʼkunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 27  Kenako anauza Tomasi kuti: “Ika chala chako apa ndiponso ona mʼmanja mwangamu. Bweretsa dzanja lako ugwire munthiti mwangamu ndipo usiye kukayikira* koma ukhulupirire.” 28  Tomasi anayankha kuti: “Mbuyanga komanso Mulungu wanga!” 29  Yesu anamufunsa kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona? Osangalala ndi amene amakhulupirira ngakhale asanaone.” 30  Kunena zoona, Yesu anachitanso zizindikiro zina zambiri pamaso pa ophunzirawo, zimene sizinalembedwe mumpukutu uno.+ 31  Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, komanso chifukwa choti mwakhulupirira, mukhale ndi moyo mʼdzina lake.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”
Kapena kuti, “pamanda achikumbutsowo.”
Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kukhala wosakhulupirira.”