Yeremiya 29:1-32

  • Kalata imene Yeremiya analembera anthu amene anatengedwa ukapolo ku Babulo (1-23)

    • Aisiraeli adzabwerera kwawo pambuyo pa zaka 70 (10)

  • Uthenga wopita kwa Semaya (24-32)

29  Awa ndi mawu amʼkalata imene mneneri Yeremiya anatumiza kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu onse amene anali mʼgulu la anthu amene anali ku ukapolo, kwa ansembe, kwa aneneri ndi kwa anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga ku Yerusalemu nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo.  Analemba kalata imeneyi pambuyo poti Mfumu Yekoniya,+ mayi a mfumu,+ nduna zapanyumba ya mfumu, akalonga a Yuda ndi Yerusalemu, amisiri komanso anthu osula zitsulo* achoka ku Yerusalemu.+  Yeremiya anatumiza kalatayi ku Babulo kudzera mwa Elasa mwana wa Safani+ ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Mfumu Zedekiya+ ya ku Yuda inawatuma kwa Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo. Kalatayo inali ndi mawu akuti:  “Kwa anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo, amene Mulungu anawachititsa kuti achoke ku Yerusalemu nʼkupita ku ukapolo ku Babulo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli akuti,  ‘Mangani nyumba nʼkumakhalamo. Limani minda nʼkumadya zipatso zake.  Tengani akazi ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwapezere akazi ndipo ana anu aakazi muwalole kuti akwatiwe kuti nawonso abereke ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko, musakhale ochepa ayi.  Ndipo mzinda umene ndakupititsani kuti mukakhale akapolo, muziufunira mtendere. Muziupempherera kwa Yehova chifukwa mzindawo ukakhala pa mtendere inunso mudzakhala pa mtendere.+  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Musalole kuti aneneri anu komanso anthu ochita zamaula amene ali pakati panu akupusitseni+ ndipo musamvere maloto amene alota.  Chifukwa ‘akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa. Ine sindinawatume,’+ akutero Yehova.”’” 10  “Yehova wanena kuti, ‘Zaka 70 zikadzakwana muli ku Babulo, ndidzakusamalirani+ ndipo ndidzakwaniritsa lonjezo langa pokubwezeretsani kumalo ano.’+ 11  ‘Ndikudziwa bwino zimene ndikuganiza zokhudza inu. Ndikuganiza zokupatsani mtendere osati masoka+ ndiponso zokupatsani tsogolo labwino ndi chiyembekezo chabwino,’ akutero Yehova.+ 12  ‘Mudzandiitana komanso mudzabwera nʼkupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.’+ 13  ‘Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza+ chifukwa mudzandifunafuna ndi mtima wanu wonse.+ 14  Ndidzakulolani kuti mundipeze,’+ akutero Yehova. ‘Ndidzasonkhanitsa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kumayiko ena kuchokera mʼmitundu yonse ndi kumalo onse kumene ndinakubalalitsirani,’+ akutero Yehova. ‘Kenako ndidzakubwezeretsani kumalo amene ndinakuchotsani pa nthawi imene ndinakupititsani ku ukapolo.’+ 15  Koma inu mwanena kuti, ‘Yehova watiikira aneneri ku Babulo.’ 16  Izi ndi zimene Yehova akunena kwa mfumu imene ikukhala pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso kwa anthu onse amene akukhala mumzinda wa Yerusalemu, abale anu amene sanapite nanu ku ukapolo, 17  ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndikuwatumizira lupanga, njala ndi mliri*+ ndipo ndidzawachititsa kuti akhale ngati nkhuyu zowola* zimene ndi zoipa kwambiri moti munthu sangadye.”’+ 18  ‘Ndidzawathamangitsa ndi lupanga,+ njala ndi mliri ndipo ndidzawapangitsa kuti akhale chinthu chochititsa mantha kwa maufumu onse apadziko lapansi.+ Komanso ndidzawachititsa kuti akhale chinthu chotembereredwa, chodabwitsa, chochiimbira mluzu+ ndiponso kuchinyoza pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene ndidzawabalalitsireko.+ 19  Ndidzawachitira zimenezi chifukwa sanamvere mawu anga amene ndinawatumizira kudzera mwa atumiki anga omwe ndi aneneri, amene ndinkawatumiza mobwerezabwereza,’* akutero Yehova.+ ‘Koma inu simunamvere,’+ akutero Yehova. 20  Choncho imvani mawu a Yehova, inu nonse amene muli ku ukapolo, amene ndinakuchotsani ku Yerusalemu nʼkukupititsani ku Babulo. 21  Ponena za Ahabu mwana wa Kolaya komanso Zedekiya mwana wa Maaseya, amene akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa,+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu amenewa ndikuwapereka mʼmanja mwa Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo ndipo adzawapha inu mukuona. 22  Ndipo zimene zidzawachitikire zidzakhala temberero limene anthu amene anatengedwa ku Yuda kupita ku ukapolo ku Babulo azidzanena kuti: “Yehova akuchititse kuti ukhale ngati Zedekiya ndi Ahabu amene mfumu ya Babulo inawawotcha pamoto!” 23  Chifukwa anachita zinthu zochititsa manyazi mu Isiraeli.+ Ankachita chigololo ndi akazi a anzawo komanso akulankhula zabodza mʼdzina langa zimene ine sindinawalamule.+ “Ine ndikuzidziwa zimenezi ndipo ndine mboni,”+ akutero Yehova.’” 24  “Ndiyeno Semaya+ wa ku Nehelamu ukamuuze kuti, 25  ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Chifukwa chakuti watumiza makalata mʼdzina lako kwa anthu onse amene ali ku Yerusalemu, kwa Zefaniya+ mwana wa Maaseya, amene ndi wansembe ndi kwa ansembe onse, onena kuti, 26  ‘Yehova wakuika kuti ukhale wansembe mʼmalo mwa Yehoyada wansembe, kuti ukhale woyangʼanira mʼnyumba ya Yehova komanso kuti uzimanga munthu aliyense wamisala, amene akuchita zinthu ngati mneneri ndipo uzimuika mʼmatangadza, miyendo, manja ndi mutu womwe.+ 27  Nanga nʼchifukwa chiyani sunalange Yeremiya wa ku Anatoti,+ amene akuchita zinthu ngati mneneri pamaso pako?+ 28  Iye watitumizira kalata kuno ku Babulo yonena kuti: “Mukhala akapolo kwa nthawi yaitali. Mangani nyumba nʼkumakhalamo. Limani minda nʼkumadya zipatso zake,+ . . .”’”’” 29  Zefaniya+ wansembe atawerengera mneneri Yeremiya kalata imeneyi, 30  Yehova anauza Yeremiya kuti: 31  “Anthu onse amene ali ku ukapolo uwatumizire uthenga wakuti, ‘Ponena za Semaya wa ku Nehelamu, Yehova wanena kuti: “Popeza Semaya analosera kwa inu, ngakhale kuti ine sindinamutume ndipo anayesetsa kukuchititsani kuti mukhulupirire zinthu zabodza,+ 32  Yehova wanena kuti, ‘Ine ndilanga Semaya wa ku Nehelamu ndi mbadwa zake. Sipadzapezeka mwamuna aliyense wochokera mʼbanja lake amene adzapulumuke pakati pa anthu awa. Ndipo iye sadzaona zabwino zimene ndidzachitire anthu anga chifukwa walimbikitsa anthu kuti apandukire Yehova,’ akutero Yehova.”’”

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “komanso anthu omanga makoma achitetezo.”
Mabaibulo ena amati, “zophulika.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ndinkadzuka mʼmawa nʼkuwatumiza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.