Machitidwe a Atumwi 5:1-42

  • Hananiya ndi Safira (1-11)

  • Atumwi anachita zizindikiro zambiri (12-16)

  • Anamangidwa nʼkumasulidwa (17-21a)

  • Anapita nawonso ku Khoti Lalikulu la Ayuda (21b-32)

    • ‘Kumvera Mulungu osati anthu’ (29)

  • Malangizo a Gamaliyeli (33-40)

  • Kulalikira kunyumba ndi nyumba (41, 42)

5  Munthu wina, dzina lake Hananiya, ndi mkazi wake Safira, anagulitsa munda wawo.  Koma iye anachotsapo ndalama zina nʼkubisa ndipo mkazi wake anadziwa zimenezo. Ndiyeno anatenga ndalama zotsalazo nʼkukazipereka kwa atumwi.+  Koma Petulo anati: “Hananiya, nʼchifukwa chiyani Satana wakulimbitsa mtima kuti unamize+ mzimu woyera+ nʼkubisa ndalama zina za mundawo?  Kodi mundawo sunali mʼmanja mwako usanaugulitse? Ndipo utaugulitsa, ndalamazo sukanatha kuchita nazo zilizonse zimene ukufuna? Ndiye nʼchifukwa chiyani unaganiza zochita zinthu zimenezi? Apatu sunanamize anthu, koma Mulungu.”  Hananiya atamva zimenezi anagwa pansi nʼkufa. Ndipo onse amene anamva zimenezi anachita mantha kwambiri.  Ndiyeno anyamata anabwera nʼkumukulunga munsalu ndipo anatuluka naye nʼkukamuika mʼmanda.  Patapita maola pafupifupi atatu mkazi wake analowa ndipo sankadziwa zimene zachitika.  Ndiyeno Petulo anamufunsa kuti: “Tandiuza, kodi ndalama zonse zimene mwapeza mutagulitsa munda wanu ndi izi?” Iye anayankha kuti: “Inde, ndi zomwezo.”  Kenako Petulo anamufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani awirinu munagwirizana kuti muyese mzimu wa Yehova?* Ukudziwa? Anthu amene anapita kukaika mwamuna wako mʼmanda ali pakhomo. Nawenso akunyamula nʼkutuluka nawe.” 10  Nthawi yomweyo Safira anagwa pansi pafupi ndi mapazi a Petulo nʼkufa. Pamene anyamata aja ankalowa anamʼpeza atafa kale. Choncho anamunyamula nʼkutuluka naye ndipo anakamuika mʼmanda pafupi ndi mwamuna wake. 11  Zitatero mpingo wonse ndiponso anthu onse amene anamva zimenezi anachita mantha kwambiri. 12  Atumwiwo anapitiriza kuchita zizindikiro ndiponso zodabwitsa zambiri pakati pa anthu.+ Ndipo okhulupirira onse ankasonkhana Pakhonde la Zipilala la Solomo.+ 13  Nʼzoona kuti palibe aliyense amene analimba mtima kugwirizana ndi ophunzirawo, komabe anthu ankawatamanda kwambiri. 14  Komanso anthu okhulupirira Ambuye anapitiriza kuwonjezereka, chifukwa amuna ndi akazi ambirimbiri anakhala ophunzira.+ 15  Anthuwo ankabweretsa odwala mʼmisewu nʼkuwagoneka pamabedi angʼonoangʼono ndi pamphasa kuti Petulo akamadutsa, chithunzithunzi chake chokha chifike pa ena mwa odwalawo.+ 16  Ndiponso anthu ambiri ochokera mʼmizinda yozungulira Yerusalemu ankapita kumeneko ndi anthu odwala komanso amene mizimu yoipa inkawazunza. Ndipo onsewo ankachiritsidwa. 17  Koma mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, omwe anali a gulu la mpatuko la Asaduki, anachita nsanje. Choncho iwo ananyamuka 18  nʼkugwira atumwiwo ndipo anawatsekera mʼndende.+ 19  Koma usiku, mngelo wa Yehova* anatsegula zitseko za ndendeyo nʼkuwatulutsa,+ ndipo anawauza kuti: 20  “Pitani mukaime mʼkachisi ndipo mukapitirize kuuza anthu zokhudza moyo umene ukubwerawo.” 21  Atamva zimenezi, mʼmawa kwambiri analowa mʼkachisi nʼkuyamba kuphunzitsa. Koma mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye anasonkhanitsa Khoti Lalikulu la Ayuda ndiponso akulu onse a Aisiraeli. Kenako anatumiza alonda kundende kuja kuti akatenge atumwiwo nʼkubwera nawo. 22  Koma alonda aja atafika, sanawapeze mʼndendemo. Choncho anabwerera nʼkukanena zimenezi. 23  Iwo anati: “Tapeza ndende ili yokhoma ndiponso yotetezedwa bwino, alonda ataima mʼmakomo. Koma titatsegula sitinapezemo aliyense.” 24  Woyangʼanira kachisi ndi ansembe aakulu atamva zimenezi, anathedwa nzeru chifukwa sankadziwa kuti zitha bwanji. 25  Koma panafika munthu wina nʼkuwauza kuti: “Anthuni! Azibambo munawatsekera mʼndende aja ali mʼkachisi, aima mmenemo ndipo akuphunzitsa anthu.” 26  Zitatero woyangʼanira kachisiyo ananyamuka ndi alonda ake nʼkukawatenga. Koma sanawatenge mwachiwawa, poopa kuponyedwa miyala ndi anthu.+ 27  Choncho anabwera nawo nʼkuwaimika muholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda. Ndipo mkulu wa ansembe ananena 28  kuti: “Tinakulamulani mwamphamvu kuti musaphunzitsenso mʼdzina limeneli.+ Koma mwadzaza Yerusalemu yense ndi mfundo zimene mukuphunzitsa ndipo mwatsimikiza mtima kuti ife tikhale ndi mlandu wa magazi a munthu ameneyu.”+ 29  Petulo ndi atumwi enawo anayankha kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.+ 30  Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene inu munamupha pomupachika pamtengo.+ 31  Ndipo Mulungu anamukweza kudzanja lake lamanja+ monga Mtumiki Wamkulu+ ndi Mpulumutsi.+ Anachita zimenezi kuti Aisiraeli alape komanso kuti machimo awo akhululukidwe.+ 32  Ndipo ife ndife mboni za zinthu zimenezi,+ chimodzimodzinso mzimu woyera,+ umene Mulungu wapereka kwa anthu amene amamumvera monga wolamulira.” 33  Atamva zimenezi, anakwiya koopsa moti ankafuna kuwapha. 34  Koma Mfarisi wina dzina lake Gamaliyeli+ anaimirira mʼKhoti Lalikulu la Ayuda. Iyeyu anali mphunzitsi wa Chilamulo wolemekezedwa ndi anthu onse. Ndiyeno analamula kuti anthuwo awatulutse kwakanthawi. 35  Kenako anawauza kuti: “Inu Aisiraeli, musamale ndi zimene mukufuna kuwachita anthu awa. 36  Chifukwa mʼmasiku amʼmbuyomu, kunali Teuda amene anadzitchukitsa kwambiri ndipo anthu pafupifupi 400 analowa mʼgulu lake. Koma anaphedwa, ndipo onse amene ankamutsatira anabalalika, osapezekanso. 37  Kenako kunabwera Yudasi wa ku Galileya mʼmasiku a kalembera. Anthu ambiri anakopeka naye ndipo ankamutsatira. Koma nayenso anafa, ndipo onse amene ankamutsatira anabalalika. 38  Choncho mmene zinthu zilili apapa, ndikukuuzani kuti asiyeni anthu amenewa musalimbane nawo. Chifukwa ngati zolinga zawo kapena ntchito iyi ikuchokera kwa anthu, sipita patali. 39  Koma ngati ikuchokera kwa Mulungu, simungathe kuwaletsa.+ Ndipo mukaumirira mukhoza kupezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”+ 40  Iwo anamvera malangizo akewa ndipo anaitanitsa atumwiwo. Ndiyeno anangowakwapula*+ nʼkuwalamula kuti asiye kulankhula mʼdzina la Yesu, kenako anawamasula. 41  Zitatero atumwiwo anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. Iwo anali osangalala+ chifukwa Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu. 42  Ndipo tsiku lililonse anapitiriza kuphunzitsa mwakhama mʼkachisi ndiponso kunyumba ndi nyumba+ komanso ankalengeza uthenga wabwino wonena za Khristu Yesu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anangowamenya.”