Machitidwe a Atumwi 24:1-27

  • Milandu imene Paulo ankaimbidwa (1-9)

  • Paulo anadziteteza pamaso pa Felike (10-21)

  • Mlandu wa Paulo unaimitsidwa kwa zaka ziwiri (22-27)

24  Patatha masiku 5, kunafika mkulu wa ansembe Hananiya+ pamodzi ndi akulu ena, komanso munthu wina wodziwa kulankhula,* dzina lake Teritulo. Iwo anayamba kufotokoza mlandu wa Paulo kwa bwanamkubwa.+  Teritulo atapatsidwa mwayi kuti alankhule, anayamba kumuneneza Paulo kuti: “Tili pa mtendere wambiri chifukwa cha inu, komanso zinthu zikusintha mu mtundu wathuwu chifukwa cha nzeru zanu zoona patali.  Choncho nthawi zonse komanso kulikonse, inu Wolemekezeka a Felike, ife timaona nzeru zanuzo ndipo timayamikira kwambiri.  Koma kuti ndisakutayitseni nthawi, ndikupempha kuti mutikomere mtima ndipo mumve mawu athu pangʼono.  Ife tapeza kuti munthu uyu ndi wovutitsa kwabasi,+ ndipo akuyambitsa zoukira boma+ pakati pa Ayuda padziko lonse. Ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lampatuko la anthu a ku Nazareti.+  Komanso iyeyu ankafuna kudetsa kachisi ndipo tinamugwira.+ 7 *⁠——  Mutamufunsa, mungathe kutsimikizira nokha zonse zimene tikunenazi.”  Atanena zimenezi Ayuda nawonso analowerera ndipo ankanena motsimikiza kuti zimenezo nʼzoona. 10  Bwanamkubwayo atagwedezera Paulo mutu kuti alankhule, Paulo anayankha kuti: “Ndikudziwa kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu kwa zaka zambiri. Choncho ndine wosangalala kulankhula podziteteza pa zimene akundinenerazi.+ 11  Inu mukhoza kupeza umboni wakuti masiku 12 sanadutse kuchokera pamene ine ndinapita ku Yerusalemu+ kukalambira Mulungu. 12  Ndipo iwowa sanandipezepo mʼkachisi ndikutsutsana ndi aliyense. Sanandipezenso ndikuyambitsa chipolowe mʼmasunagoge kapena pena paliponse mumzindawu. 13  Ndipo panopa sangathe kukupatsani umboni wa zimene akundinenerazi. 14  Koma chomwe ndikuvomereza kwa inu ndi chakuti: Njira yolambirira imene iwo akuitchula kuti ‘gulu lampatuko,’ ndi imene ine ndikuitsatira potumikira Mulungu wa makolo anga.+ Chifukwa ndimakhulupirira zonse zimene zili mʼChilamulo ndi zimene aneneri analemba.+ 15  Ndipo ine ndili ndi chiyembekezo ngati chimenenso anthu awa ali nacho, kuti Mulungu adzaukitsa+ olungama ndi osalungama omwe.+ 16  Chifukwa cha zimenezi, ndikuyesetsa mwakhama kuti ndikhale ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu ndiponso kwa anthu.+ 17  Ndiyeno pambuyo pa zaka zambiri, ndinabwera kudzapereka mphatso zachifundo+ kwa anthu a mtundu wanga ndiponso kudzapereka nsembe. 18  Pamene ndinkachita zimenezi, anandipeza mʼkachisi nditadziyeretsa motsatira mwambo.+ Panalibe gulu la anthu kapena phokoso, koma panali Ayuda ena ochokera mʼchigawo cha Asia. 19  Amenewo, akanakhala ndi chifukwa, ndi amene anayenera kubwera kwa inu kudzandiimba mlandu.+ 20  Kapena muwalole anthu ali panowa, afotokoze okha ngati anandipeza ndi mlandu uliwonse pamene ndinaima pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. 21  Mawu amodzi okha amene ine ndinanena, pamene ndinaima pakati pawo ndi akuti, ‘Ine lero ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo chakuti akufa adzauka!’”+ 22  Popeza Felike ankadziwa bwino nkhani yokhudza Njira imeneyi,+ anaimitsa mlanduwo nʼkunena kuti: “Ndidzagamula mlandu wanuwu akadzafika Lusiya mkulu wa asilikali.” 23  Iye analamula mtsogoleri wa asilikali kuti amusunge mʼndende, koma amupatseko ufulu ndipo azilola anthu a mtundu wake kudzamuthandiza. 24  Patapita masiku angapo, Felike anafika pamodzi ndi mkazi wake Durusila, amene anali Myuda. Ndiyeno Felike anaitanitsa Paulo nʼkumamvetsera pamene ankafotokoza za kukhulupirira Khristu Yesu.+ 25  Koma pamene ankafotokoza zokhudza chilungamo, kudziletsa ndiponso chiweruzo chimene chikubwera,+ Felike anachita mantha ndipo anati: “Basi pita kaye, ndikadzapeza nthawi ndidzakuitananso.” 26  Komanso ankaganiza kuti Paulo amupatsa ndalama. Choncho ankamuitanitsa pafupipafupi nʼkumakambirana naye. 27  Patatha zaka ziwiri, Felike analowedwa mʼmalo ndi Porikiyo Fesito. Koma popeza Felike ankafuna kuti Ayuda azimukonda,+ anangomusiya Paulo mʼndende.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “loya wina.”