Genesis 17:1-27

  • Abulahamu adzakhala tate wa mitundu yambiri (1-8)

    • Dzina la Abulamu linasinthidwa kukhala Abulahamu (5)

  • Pangano la mdulidwe (9-14)

  • Dzina la Sarai linasinthidwa kukhala Sara (15-17)

  • Analonjezedwa za kubadwa kwa Isaki (18-27)

17  Abulamu ali ndi zaka 99, Yehova anaonekera kwa iye nʼkumuuza kuti: “Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse. Uziyenda mʼnjira zanga ndipo ukhale wopanda cholakwa.  Ndidzakhazikitsa pangano langa pakati pa ine ndi iwe+ ndipo ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa zako.”+  Abulamu atamva zimenezi anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi. Kenako Mulungu anapitiriza kulankhula naye kuti:  “Ine ndinachita pangano ndi iwe,+ ndipo iwe udzakhaladi tate wa mitundu yambiri.+  Dzina lako silikhalanso Abulamu* koma likhala Abulahamu,* chifukwa ndidzakupangitsa kukhala tate wa mitundu yambiri.  Ndidzakupatsa mbadwa zambirimbiri, ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu ndi mafumu.+  Ndidzasunga pangano limene ine ndachita ndi iwe+ komanso ndi mbadwa zako* mʼmibadwo yawo yonse. Lidzakhala pangano losatha kusonyeza kuti ndine Mulungu wako ndi wa mbadwa zako.  Dziko limene ukukhalamo ngati mlendoli,+ ndidzalipereka kwa iwe ndi mbadwa zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala lawo mpaka kalekale, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”+  Mulungu anapitiriza kuuza Abulahamu kuti: “Koma iwe usunge pangano langa, iwe ndi mbadwa zako mʼmibadwo yawo yonse. 10  Ili ndi pangano la pakati pa ine ndi iwe, lakuti iwe ndi mbadwa zako muzilisunga: Mwamuna aliyense pakati panu azidulidwa.+ 11  Muzichita mdulidwe* kuti ukhale chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi inu.+ 12  Mwana aliyense wamwamuna amene wakwanitsa masiku 8 azidulidwa+ mʼmibadwo yanu yonse. Aliyense amene wabadwira mʼnyumba yanu komanso aliyense amene si mbadwa yanu koma munamugula ndi ndalama kwa mlendo azidulidwa. 13  Mwamuna aliyense wobadwira mʼnyumba mwanu komanso mwamuna aliyense amene mwamugula ndi ndalama zanu ayenera kudulidwa.+ Pangano langa, lomwe chizindikiro chake chili pathupi lanu, lidzakhala pangano losatha. 14  Mwamuna aliyense wosadulidwa akapanda kudulidwa, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu ake. Munthuyo waphwanya pangano langa.” 15  Kenako Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Mkazi wako Sarai,*+ usamamuitanenso kuti Sarai, chifukwa dzina lake tsopano likhala Sara.* 16  Ndidzamudalitsa ndipo adzakuberekera mwana wamwamuna.+ Iye ndidzamudalitsa moti adzakhala mayi wa mitundu yambiri ya anthu ndi wa mafumu a mitundu yambiri ya anthu.” 17  Abulahamu atamva zimenezi anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi, kenako anayamba kuseka nʼkunena mumtima mwake kuti:+ “Kodi mwamuna wa zaka 100 angabereke mwana zoona? Komanso Sara mkazi wa zaka 90, zoona angakhale ndi mwana?”+ 18  Kenako Abulahamu anauza Mulungu woona kuti: “Ndikukupemphani kuti mudalitse Isimaeli.”+ 19  Ndiyeno Mulungu anati: “Ndithu Sara mkazi wako adzakuberekera mwana wamwamuna ndipo udzamʼpatse dzina lakuti Isaki.*+ Ndidzakhazikitsa pangano ndi iye, kuti likhale pangano losatha kwa mbadwa zake.+ 20  Koma za Isimaeli ndamva pempho lako. Iye ndidzamudalitsa ndipo ndidzamupatsa ana ambiri, komanso ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa zake. Adzabereka ana 12 amene adzakhale atsogoleri a mafuko, ndipo ndidzamupangitsa kukhala mtundu waukulu.+ 21  Koma ndidzakhazikitsa pangano langa ndi Isaki,+ amene Sara adzakuberekera nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa.”+ 22  Mulungu atamaliza kulankhula ndi Abulahamu, anachoka. 23  Ndiyeno Abulahamu anatenga mwana wake Isimaeli ndi amuna onse obadwira mʼnyumba yake, ndi aliyense amene anamugula ndi ndalama zake. Anatenga amuna onse amʼnyumba yake ndipo anawadula tsiku lomwelo monga mmene Mulungu anamuuzira.+ 24  Abulahamu anadulidwa+ ali ndi zaka 99. 25  Ndipo mwana wake Isimaeli anadulidwa ali ndi zaka 13.+ 26  Choncho pa tsiku limenelo Abulahamu ndi mwana wake Isimaeli anadulidwa. 27  Amuna onse amʼnyumba yake, aliyense wobadwira mʼnyumba yake ndi aliyense wogulidwa ndi ndalama zake kwa mlendo, nawonso anadulidwa naye limodzi.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kuti, “Atate Ndi Wapamwamba (Ndi Wokwezeka).”
Kutanthauza kuti, “Tate wa Anthu Ambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yako.” MʼChiheberi mawu akuti “mbadwa zako” akunena za mbadwa imodzi koma angaimirenso gulu la anthu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Muzichita mdulidwe wa khungu lanu lakunsonga.”
Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Wolongolola.”
Kutanthauza kuti, “Mfumukazi.”
Kutanthauza kuti, “Kuseka.”