Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Genesis

Machaputala

Mitu

  • 1

    • Kulengedwa kwa dziko lapansi ndi kumwamba (1, 2)

    • Masiku 6 okonza dziko lapansi  (3-31)

      • Tsiku Loyamba: kuwala; masana ndi usiku (3-5)

      • Tsiku Lachiwiri: mlengalenga (6-8)

      • Tsiku Lachitatu: mtunda ndi zomera (9-13)

      • Tsiku la 4: zounikira zakumwamba (14-19)

      • Tsiku la 5: nsomba ndi mbalame (20-23)

      • Tsiku la 6: nyama ndi anthu (24-31)

  • 2

    • Mulungu anapuma pa tsiku la 7 (1-3)

    • Yehova Mulungu anapanga kumwamba ndi dziko lapansi (4)

    • Mwamuna ndi mkazi mʼmunda wa Edeni  (5-25)

      • Munthu anapangidwa kuchokera kudothi (7)

      • Mtengo woletsedwa wodziwitsa chabwino ndi choipa (15-17)

      • Kulengedwa kwa mkazi (18-25)

  • 3

    • Kuchimwa kwa munthu (1-13)

      • Bodza loyamba (4, 5)

    • Chiweruzo chimene Yehova anapereka kwa opanduka (14-24)

      • Ananeneratu za mbadwa ya mkazi  (15)

      • Anathamangitsidwa mu Edeni (23, 24)

  • 4

    • Kaini ndi Abele (1-16)

    • Mbadwa za Kaini (17-24)

    • Seti ndi mwana wake Enosi (25, 26)

  • 5

    • Kuyambira pa Adamu kudzafika pa Nowa (1-32)

      • Adamu anabereka ana aamuna ndi aakazi (4)

      • Inoki anayenda ndi Mulungu (21-24)

  • 6

    • Ana a Mulungu anakwatira akazi padziko lapansi (1-3)

    • Kubadwa kwa Anefili (4)

    • Yehova anamva chisoni chifukwa cha kuipa kwa anthu (5-8)

    • Nowa anapatsidwa ntchito yopanga chingalawa (9-16)

    • Mulungu ananena kuti adzabweretsa chigumula (17-22)

  • 7

    • Kulowa mʼchingalawa (1-10)

    • Chigumula cha dziko lonse (11-24)

  • 8

    • Kuphwa kwa madzi a chigumula (1-14)

      • Anatumiza njiwa (8-12)

    • Kutuluka mʼchingalawa (15-19)

    • Lonjezo la Mulungu lokhudza dziko lapansi (20-22)

  • 9

    • Malangizo opita kwa anthu onse (1-7)

      • Lamulo lokhudza magazi (4-6)

    • Pangano la utawaleza (8-17)

    • Maulosi okhudza mbadwa za Nowa (18-29)

  • 10

    • Mitundu ya anthu (1-32)

      • Mbadwa za Yafeti  (2-5)

      • Mbadwa za Hamu (6-20)

        • Nimurodi anatsutsana ndi Yehova (8-12)

      • Mbadwa za Semu (21-31)

  • 11

    • Nsanja ya Babele (1-4)

    • Yehova anasokoneza chilankhulo (5-9)

    • Kuchokera pa Semu kudzafika pa Abulamu (10-32)

      • Banja la Tera (27)

      • Abulamu anachoka ku Uri (31)

  • 12

    • Abulamu anachoka ku Harana kupita ku Kanani (1-9)

      • Lonjezo la Mulungu kwa Abulamu (7)

    • Abulamu ndi Sarai ku Iguputo (10-20)

  • 13

    • Abulamu anabwerera ku Kanani (1-4)

    • Abulamu anasiyana ndi Loti (5-13)

    • Mulungu anabwereza lonjezo lake kwa Abulamu (14-18)

  • 14

    • Abulamu anapulumutsa Loti (1-16)

    • Melekizedeki anadalitsa Abulamu (17-24)

  • 15

    • Pangano la Mulungu ndi Abulamu (1-21)

      • Ananeneratu kuti adzazunzidwa kwa zaka 400 (13)

      • Mulungu anabwereza lonjezo lake kwa Abulamu (18-21)

  • 16

    • Hagara ndi Isimaeli (1-16)

  • 17

    • Abulahamu adzakhala tate wa mitundu yambiri (1-8)

      • Dzina la Abulamu linasinthidwa kukhala Abulahamu (5)

    • Pangano la mdulidwe (9-14)

    • Dzina la Sarai linasinthidwa kukhala Sara (15-17)

    • Analonjezedwa za kubadwa kwa Isaki (18-27)

  • 18

    • Angelo atatu anapita kwa Abulahamu (1-8)

    • Analonjeza kuti Sara adzabereka mwana wamwamuna; Sara anaseka (9-15)

    • Abulahamu anapempha zokhudza Sodomu (16-33)

  • 19

    • Angelo anapita kwa Loti (1-11)

    • Loti ndi banja lake anauzidwa kuti asamuke (12-22)

    • Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora (23-29)

      • Mkazi wa Loti anasanduka chipilala chamchere (26)

    • Loti ndi ana ake aakazi (30-38)

      • Kumene Amowabu ndi Aamoni anachokera (37, 38)

  • 20

    • Sara anapulumutsidwa kwa Abimeleki (1-18)

  • 21

    • Kubadwa kwa Isaki (1-7)

    • Isimaeli ankaseka Isaki (8, 9)

    • Hagara ndi Isimaeli anathamangitsidwa (10-21)

    • Pangano la Abulahamu ndi Abimeleki (22-34)

  • 22

    • Abulahamu anauzidwa kuti apereke Isaki nsembe (1-19)

      • Madalitso chifukwa cha mbadwa ya Abulahamu (15-18)

    • Banja la Rabeka (20-24)

  • 23

    • Imfa ya Sara komanso manda ake (1-20)

  • 24

    • Anafunira Isaki mkazi (1-58)

    • Rabeka anapita kukakumana ndi Isaki (59-67)

  • 25

    • Abulahamu anakwatiranso (1-6)

    • Imfa ya Abulahamu (7-11)

    • Ana a Isimaeli (12-18)

    • Kubadwa kwa Yakobo ndi Esau (19-26)

    • Esau anagulitsa ukulu wake (27-34)

  • 26

    • Isaki ndi Rabeka ku Gerari (1-11)

      • Mulungu anatsimikizira lonjezo lake kwa Isaki (3-5)

    • Kukanganirana zitsime (12-25)

    • Pangano la Isaki ndi Abimeleki (26-33)

    • Akazi awiri a Chihiti a Esau (34, 35)

  • 27

    • Yakobo anadalitsidwa ndi Isaki (1-29)

    • Esau ankafuna madalitso koma sanalape (30-40)

    • Esau anayamba kudana ndi Yakobo (41-46)

  • 28

    • Isaki anatumiza Yakobo ku Padani-aramu (1-9)

    • Maloto a Yakobo ku Beteli (10-22)

      • Mulungu anatsimikizira Yakobo za lonjezo lake (13-15)

  • 29

    • Yakobo anakumana ndi Rakele (1-14)

    • Yakobo anakonda Rakele (15-20)

    • Yakobo anakwatira Leya ndi Rakele (21-29)

    • Ana 4 aamuna a Yakobo amene Leya anamuberekera: Rubeni, Simiyoni, Levi ndi Yuda (30-35)

  • 30

    • Biliha anabereka Dani ndi Nafitali (1-8)

    • Zilipa anabereka Gadi ndi Aseri (9-13)

    • Leya anabereka Isakara ndi Zebuloni (14-21)

    • Rakele anabereka Yosefe (22-24)

    • Ziweto za Yakobo zinachuluka (25-43)

  • 31

    • Yakobo anachoka ku Kanani mozemba (1-18)

    • Labani anapezana ndi Yakobo (19-35)

    • Pangano la Yakobo ndi Labani (36-55)

  • 32

    • Angelo anakumana ndi Yakobo (1, 2)

    • Yakobo anakonzekera kukumana ndi Esau (3-23)

    • Yakobo analimbana ndi mngelo (24-32)

      • Yakobo anasinthidwa dzina kukhala Isiraeli (28)

  • 33

    • Yakobo anakumana ndi Esau (1-16)

    • Yakobo anapita ku Sekemu  (17-20)

  • 34

    • Dina anagwiriridwa (1-12)

    • Ana a Yakobo anachita zinthu mwachinyengo (13-31)

  • 35

    • Yakobo anachotsa milungu yachilendo (1-4)

    • Yakobo anabwerera ku Beteli (5-15)

    • Kubadwa kwa Benjamini; imfa ya Rakele (16-20)

    • Ana 12 a Isiraeli (21-26)

    • Imfa ya Isaki (27-29)

  • 36

    • Mbadwa za Esau (1-30)

    • Mafumu a ku Edomu (31-43)

  • 37

    • Maloto a Yosefe (1-11)

    • Yosefe ndi abale ake ansanje (12-24)

    • Yosefe anagulitsidwa ku ukapolo (25-36)

  • 38

    • Yuda ndi Tamara (1-30)

  • 39

    • Yosefe mʼnyumba ya Potifara (1-6)

    • Yosefe anakana kugona ndi mkazi wa Potifara (7-20)

    • Yosefe anaikidwa mʼndende (21-23)

  • 40

    • Yosefe anamasulira maloto a akaidi (1-19)

      • ‘Mulungu ndi amene amamasulira’ (8)

    • Phwando lokondwerera tsiku lobadwa la Farao (20-23)

  • 41

    • Yosefe anamasulira maloto a Farao (1-36)

    • Yosefe anapatsidwa udindo ndi Farao (37-46a)

    • Yosefe ankayangʼanira ntchito yogawa chakudya (46b-57)

  • 42

    • Azichimwene ake a Yosefe anapita ku Iguputo (1-4)

    • Yosefe anakumana ndi azichimwene ake ndipo anawayesa (5-25)

    • Azichimwene ake a Yosefe anabwerera kwa Yakobo (26-38)

  • 43

    • Ulendo wachiwiri wa azichimwene ake a Yosefe wopita ku Iguputo limodzi ndi Benjamini (1-14)

    • Yosefe anakumananso ndi azichimwene ake (15-23)

    • Phwando la Yosefe ndi azichimwene ake (24-34)

  • 44

    • Kapu yasiliva ya Yosefe inapezeka mʼthumba la Benjamini (1-17)

    • Yuda anapempha kuti akhale kapolo mʼmalo mwa Benjamini (18-34)

  • 45

    • Yosefe anadziulula kwa azichimwene ake (1-15)

    • Azichimwene ake a Yosefe anabwerera kwawo kukatenga Yakobo (16-28)

  • 46

    • Yakobo ndi banja lake anasamukira ku Iguputo (1-7)

    • Mayina a anthu amene anasamukira ku Iguputo (8-27)

    • Yosefe anakumana ndi Yakobo ku Goseni (28-34)

  • 47

    • Yakobo anakumana ndi Farao (1-12)

    • Yosefe anagwira ntchito yoyangʼanira mwanzeru (13-26)

    • Isiraeli anakhazikika ku Goseni (27-31)

  • 48

    • Yakobo anadalitsa ana awiri a Yosefe (1-12)

    • Efuraimu analandira madalitso ambiri (13-22)

  • 49

    • Ulosi umene Yakobo ananena atatsala pangʼono kumwalira (1-28)

      • Silo adzachokera mwa Yuda (10)

    • Yakobo anapereka malangizo okhudza kuikidwa mʼmanda kwake (29-32)

    • Imfa ya Yakobo (33)

  • 50

    • Yosefe anaika mʼmanda Yakobo ku Kanani (1-14)

    • Yosefe anatsimikizira abale ake kuti anawakhululukira (15-21)

    • Masiku akumapeto kwa moyo wa Yosefe ndi imfa yake (22-26)

      • Lamulo la Yosefe lokhudza mafupa ake (25)