Kalata Yoyamba ya Petulo 4:1-19

  • Muzichita zimene Mulungu amafuna, ngati mmene Khristu ankachitira (1-6)

  • Mapeto a zinthu zonse ayandikira (7-11)

  • Kuvutika chifukwa chokhala Mkhristu (12-19)

4  Popeza Khristu anavutika pa nthawi imene anali munthu,+ nanunso konzekerani pokhala ndi maganizo ofanana ndi amene Khristu anali nawo. Zili choncho chifukwa munthu amene akuvutika ndiye kuti anasiya kuchita machimo.+  Anachita zimenezi kuti pa nthawi yonse imene ali moyo asamachite zofuna za anthu+ koma za Mulungu.+  Mʼmbuyomu munkangokhalira kuchita zofuna za anthu amʼdzikoli.+ Pa nthawi imeneyo munkachita khalidwe lopanda manyazi,* munkalakalaka zoipa, munkamwa vinyo mopitirira muyezo, munkakonda maphwando oipa,* munkapanga mipikisano yomwa mowa komanso munkapembedza mafano, komwe kunali kuphwanya malamulo.+  Chifukwa choti munasiya kuthamanga nawo limodzi mʼchithaphwi cha* makhalidwe oipa, anthu amʼdzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.+  Koma anthu amenewa adzayankha mlandu kwa Khristu yemwe adzaweruze amoyo ndi akufa omwe.+  Nʼchifukwa chake uthenga wabwino unalengezedwanso kwa akufa,+ kuti ngakhale akuweruzidwa malinga ndi mmene akuonekera,* mogwirizana ndi kuona kwa anthu, akhale ndi moyo mwa mzimu mogwirizana ndi kuona kwa Mulungu.  Koma mapeto a zinthu zonse ayandikira. Choncho khalani oganiza bwino,+ ndipo khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.+  Koposa zonse, muzikondana kwambiri+ chifukwa chikondi chimakwirira machimo ochuluka.+  Muzicherezana popanda kudandaula.+ 10  Aliyense wa inu analandira mphatso, choncho muzigwiritsa ntchito mphatso zanuzo potumikirana. Muzichita zimenezi monga atumiki amene amathandiza ena kuti apindule ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kumene amakusonyeza mʼnjira zosiyanasiyana.+ 11  Ngati wina ali ndi mphatso ya kulankhula, azilankhula mogwirizana ndi mawu opatulika a Mulungu. Ngati wina akutumikira ena, aziwatumikira modalira mphamvu imene Mulungu amapereka.+ Azichita zimenezi kuti Mulungu alemekezeke mʼzinthu zonse+ kudzera mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Ame. 12  Okondedwa, musadabwe ndi mayesero oyaka moto amene mukukumana nawo+ ngati kuti mukukumana ndi chinachake chachilendo. 13  Koma muzisangalala+ chifukwa mukukumana ndi mayesero ofanana ndi amene Khristu anakumana nawo+ kuti mudzasangalalenso kwambiri pa nthawi imene ulemerero wake udzaonekere.*+ 14  Ndinu osangalala*+ ngati anthu akukunyozani chifukwa cha dzina la Khristu chifukwa zimenezi zikusonyeza kuti mzimu woyera wa Mulungu komanso ulemerero wake zili pa inu. 15  Koma sindikufuna kuti wina wa inu azivutika chifukwa choti wayamba kuba, kupha anthu, kuchita zoipa kapena chifukwa choti akulowerera nkhani za eni.+ 16  Koma ngati wina akuvutika chifukwa chokhala Mkhristu, asachite manyazi,+ koma apitirize kulemekeza Mulungu kwinaku akudziwikabe monga Mkhristu. 17  Inoyo ndi nthawi imene Mulungu anasankhiratu kuti apereke chiweruzo, ndipo chiyambira panyumba yake.+ Komano ngati chikuyambira pa ifeyo,+ ndiye anthu osamvera uthenga wabwino wa Mulungu zidzawathera bwanji?+ 18  “Ndipo ngati munthu wolungama angadzapulumuke movutikira, kodi chidzachitike nʼchiyani kwa munthu wosaopa Mulungu komanso wochimwa?”+ 19  Choncho amene akuvutika chifukwa choti akuchita zimene Mulungu amafuna, apereke moyo wawo kwa Mlengi wathu amene ndi wokhulupirika nʼkumapitiriza kuchita zabwino.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “munkachita makhalidwe opanda manyazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “maphwando aphokoso.”
Kapena kuti, “mʼmatope onyansa a.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akuweruzidwa mwa thupi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “udzaululike.”
Kapena kuti, “Ndinu odala.”