Ekisodo 6:1-30

  • Anawauzanso lonjezo lakuti adzawalanditsa ku ukapolo (1-13)

    • Dzina la Yehova silinadziwike mokwanira (2, 3)

  • Mzere wobadwira wa Mose ndi Aroni (14-27)

  • Mose anakaonekeranso pamaso pa Farao (28-30)

6  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano uona zimene ndichite kwa Farao.+ Dzanja langa lamphamvu limukakamiza kuti awalole kuchoka, ndipo dzanja langa lamphamvu limukakamiza kuti awathamangitse mʼdziko lake.”+  Kenako Mulungu anauza Mose kuti: “Ine ndine Yehova.  Ndinkaonekera kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo monga Mulungu Wamphamvuyonse.+ Koma za dzina langa lakuti Yehova,+ ine sindinadzidziwikitse kwa iwo.+  Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuti ndidzawapatsa dziko la Kanani, dziko limene ankakhalamo ngati alendo.+  Tsopano ine ndamva kubuula kwa Aisiraeli, amene Aiguputo akuwagwiritsa ntchito yaukapolo, ndipo ndikukumbukira pangano langa.+  Choncho uwauze Aisiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova. Ndidzakupulumutsani ku ntchito yokakamiza imene Aiguputo akukugwiritsani ndipo ndidzakulanditsani kuti musakhalenso akapolo awo.+ Ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasula* komanso ndi ziweruzo zamphamvu.+  Choncho ndidzakutengani kuti mukhale anthu anga, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.+ Inuyo mudzadziwadi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndikukupulumutsani ku ntchito yokakamiza imene Aiguputo akukugwiritsani.  Ine ndidzakulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira* kuti ndidzalipereka kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale lanu.+ Ine ndine Yehova.’”+  Kenako Mose anapereka uthenga umenewu kwa Aisiraeli, koma iwo sanamvere Mose chifukwa chokhumudwa ndiponso chifukwa cha ntchito yowawa ya ukapolo.+ 10  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 11  “Pita kwa Farao, mfumu ya Iguputo, ukamuuze kuti alole Aisiraeli kutuluka mʼdziko lake.” 12  Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Komatu Aisiraeli sanandimvere,+ ndiye Farao akandimvera bwanji? Pajatu ndimalankhula movutikira.”*+ 13  Koma Yehova anauzanso Mose ndi Aroni malamulo oti apereke kwa Aisiraeli ndi kwa Farao, mfumu ya Iguputo, kuti atulutse Aisiraeli mʼdziko la Iguputo. 14  Atsogoleri a mafuko a Aisiraeli ndi awa: Ana aamuna a Rubeni, yemwe anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli,+ anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ Amenewa ndi mabanja a fuko la Rubeni. 15  Ana aamuna a Simiyoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shauli, mwana amene anabereka ndi mkazi wa Chikanani.+ Amenewa ndi mabanja a fuko la Simiyoni. 16  Mayina a ana aamuna a Levi,+ mogwirizana ndi mzere wobadwira wa makolo awo ndi awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ Ndipo Levi anakhala ndi moyo zaka 137. 17  Ana a Gerisoni anali Libini ndi Simeyi, mogwirizana ndi mabanja awo.+ 18  Ndipo ana a Kohati anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+ Kohati anakhala ndi moyo zaka 133. 19  Ndipo ana aamuna a Merari anali Mali ndi Musi. Amenewa anali mabanja a Alevi mogwirizana ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+ 20  Tsopano Amuramu anatenga Yokebedi, mchemwali wa bambo ake, kukhala mkazi wake.+ Ndipo Yokebedi anamʼberekera Amuramu, Aroni ndi Mose.+ Amuramu anakhala ndi moyo zaka 137. 21  Ana aamuna a Izara anali Kora,+ Nefegi ndi Zikiri. 22  Ana aamuna a Uziyeli anali Misayeli, Elizafana+ ndi Sitiri. 23  Aroni anatenga Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mchemwali wake wa Naasoni,+ kukhala mkazi wake. Ndipo Eliseba anamʼberekera Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+ 24  Ana aamuna a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu.+ Amenewa anali mabanja a Kora.+ 25  Ndipo Eleazara+ mwana wa Aroni, anatenga mwana wamkazi wa Putieli kukhala mkazi wake. Ndipo iye anamʼberekera Pinihasi.+ Amenewa ndi atsogoleri a mabanja amʼfuko la Levi, mogwirizana ndi mabanja awo.+ 26  Umenewu ndi mzere wobadwira wa Aroni ndi Mose, amene Yehova anawauza kuti: “Tulutsani Aisiraeli mʼdziko la Iguputo mʼmagulumagulu.”*+ 27  Anali Mose ndi Aroni+ amene analankhula ndi Farao mfumu ya Iguputo kuti atulutse Aisiraeli mu Iguputo. 28  Pa tsiku limene Yehova analankhula ndi Mose mʼdziko la Iguputo, 29  Yehova anamuuza kuti: “Ine ndine Yehova. Zonse zimene ndikukuuza, ukauze Farao mfumu ya Iguputo.” 30  Ndiye Mose anauza Yehova kuti: “Komatu ndimalankhula movutikira,* ndiye Farao akandimvera bwanji?”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “lamphamvu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinalumbira nditakweza dzanja langa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndili ndi milomo yosadulidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndili ndi milomo yosadulidwa.”