Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 9:1-15

  • Analimbikitsidwa kukhala opatsa (1-15)

    • Mulungu amakonda wopereka mosangalala (7)

9  Ponena za utumiki wothandiza oyerawo,+ nʼzosafunika kuti ndichite kukulemberani.  Chifukwa ndikudziwa kuti muli ndi mtima wofunitsitsa ndipo ndikunena zimenezi monyadira kwa anthu a ku Makedoniya. Ndikumawauza kuti abale a ku Akaya akhala okonzeka kwa chaka chimodzi tsopano, ndipo kudzipereka kwanu kwalimbikitsa abale ambiri kumeneko.  Koma ndikutumiza abale kuti tisangokunyadirani pachabe pa nkhani imeneyi, koma kuti mukhaledi okonzeka, mogwirizana ndi zimene ndawauza.  Chifukwatu ndikadzafika kumeneko ndi anthu a ku Makedoniya nʼkupeza kuti simunakonzeke, ifeyo ndi inu nomwe, tidzachita manyazi chifukwa tinkakhulupirira kuti mukonzeka.  Choncho ndaona kuti ndi bwino kuti ndiuze abale kuti abwere kumeneko ife tisanafike, nʼcholinga choti adzakuthandizeni kukonzeratu mphatso imene munalonjeza kuti mudzapereka mowolowa manja. Zikatero, mphatsoyi idzakhala itakonzedwa kale ndipo zidzaonekeratu kuti mukuipereka mowolowa manja, osati mokakamizidwa.  Pa nkhani imeneyi, wodzala moumira adzakolola zochepa ndipo wodzala mowolowa manja adzakolola zambiri.+  Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika,+ chifukwa Mulungu amakonda munthu amene amapereka mosangalala.+  Komanso, Mulungu akhoza kukusonyezani kwambiri kukoma mtima kwake kwakukulu kuti musasowe zinthu zofunika pa moyo komanso kuti mukhale ndi zinthu zambiri zokuthandizani kugwira ntchito iliyonse yabwino.+  (Mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Iye wagawira mowolowa manja. Wapereka kwa anthu osauka, ndipo chilungamo chake chidzakhalapo mpaka kalekale.”+ 10  Tsopano amene amapereka mowolowa manja mbewu kwa wodzala komanso chakudya kuti anthu adye, adzakupatsani mowolowa manja mbewu zoti mudzale. Adzawonjezeranso zokolola za chilungamo chanu.) 11  Mulungu akukudalitsani pa chilichonse kuti muthe kupereka mowolowa manja mʼnjira zosiyanasiyana ndipo anthu akuyamika Mulunguyo chifukwa cha mphatso yanu imene ife tikupereka kwa anthu ena. 12  Chifukwa utumiki wothandiza anthuwu sikuti ukungothandiza kuti oyerawo apeze zimene akufunikira,+ koma ukuchititsanso kuti anthu ambiri aziyamikira Mulungu mʼmapemphero awo. 13  Chifukwa cha umboni umene utumikiwu ukupereka, iwo akulemekeza Mulungu. Akutero chifukwa inuyo mwagonjera uthenga wabwino wonena za Khristu umene mukulengeza poyera ndiponso mwapereka mowolowa manja kwa iwowo ndi kwa anthu onse.+ 14  Iwo amakupemphererani mochonderera kwa Mulungu ndipo amasonyeza kuti amakukondani chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wakusonyezani. 15  Tikuthokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yake yaulere, imene sitingathe kuifotokoza.

Mawu a M'munsi