Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Yobu

Machaputala

Mitu

  • 1

    • Kukhulupirika kwa Yobu komanso chuma chake (1-5)

    • Satana anakaikira zolinga za Yobu (6-12)

    • Chuma cha Yobu chinawonongeka ndipo ana ake anafa (13-19)

    • Yobu sanaimbe Mulungu mlandu (20-22)

  • 2

    • Satana anakaikira kachiwiri zolinga za Yobu (1-5)

    • Satana analoledwa kuti abweretse mavuto pa thupi la Yobu (6-8)

    • Mkazi wa Yobu ananena kuti: “Tukwanani Mulungu mufe!” (9, 10)

    • Anzake a Yobu atatu anabwera (11-13)

  • 3

    • Yobu anadandaula kuti anabadwiranji (1-26)

      • Anafunsa chifukwa chake ankazunzika (20, 21)

  • 4

    • Mawu oyamba a Elifazi (1-21)

      • Ananyoza kukhulupirika kwa Yobu (7, 8)

      • Anafotokoza uthenga wochokera kwa mzimu (12-17)

      • ‘Mulungu sakhulupirira atumiki ake’ (18)

  • 5

    • Mawu oyamba a Elifazi akupitirira (1-27)

      • ‘Mulungu amachititsa kuti anzeru agwere mʼmisampha yawo’ (13)

      • ‘Yobu asakane chilango cha Mulungu’ (17)

  • 6

    • Yankho la Yobu (1-30)

      • Ananena kuti akuyenera kudandaula (2-6)

      • Anthu amene ankamutonthoza anali achinyengo (15-18)

      • “Munthu akamanena zoona, sizipweteka” (25)

  • 7

    • Yankho la Yobu likupitirira (1-21)

      • Moyo uli ngati ntchito yokakamiza (1, 2)

      • “Nʼchifukwa chiyani mukulimbana ndi ine?” (20)

  • 8

    • Mawu oyamba a Bilidadi (1-22)

      • Ananena kuti ana a Yobu anachimwa (4)

      • ‘Ngati ukanakhaladi woyera, Mulungu akanakuteteza’ (6)

      • Ananena kuti Yobu ndi woipa (13)

  • 9

    • Yankho la Yobu (1-35)

      • Munthu sangalimbane ndi Mulungu (2-4)

      • ‘Mulungu amachita zinthu zosatheka kuzifufuza’ (10)

      • Palibe amene angatsutsane ndi Mulungu (32)

  • 10

    • Yankho la Yobu likupitirira (1-22)

      • ‘Nʼchifukwa chiyani Mulungu akulimbana nane?’ (2)

      • Kusiyana kwa Mulungu ndi Yobu (4-12)

      • ‘Ndipumeko pangʼono’ (20)

  • 11

    • Mawu oyamba a Zofari (1-20)

      • Ananena kuti Yobu akulankhula zopanda pake (2, 3)

      • Anauza Yobu kuti asiye kuchita zolakwika (14)

  • 12

    • Yankho la Yobu (1-25)

      • “Si ine munthu wamba poyerekezera ndi inu” (3)

      • “Ine ndakhala chinthu choseketsa” (4)

      • ‘Nzeru zili ndi Mulungu’ (13)

      • Mulungu ndi wapamwamba kuposa oweruza ndi mafumu (17, 18)

  • 13

    • Yankho la Yobu likupitirira (1-28)

      • ‘Ndikanakonda kulankhula ndi Mulungu’ (3)

      • “Nonsenu ndinu madokotala osathandiza” (4)

      • “Ine ndikudziwa kuti sindinalakwe” (18)

      • Anafunsa chifukwa chake Mulungu akumuona ngati mdani wake (24)

  • 14

    • Yankho la Yobu likupitirira (1-22)

      • Munthu amakhala ndi moyo waufupi komanso wodzaza ndi mavuto (1)

      • “Ngakhale mtengo umakhala ndi chiyembekezo” (7)

      • ‘Zikanakhala bwino mukanandibisa mʼManda’ (13)

      • “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” (14)

      • Mulungu adzalakalaka ntchito ya manja ake (15)

  • 15

    • Mawu achiwiri a Elifazi (1-35)

      • Ananena kuti Yobu saopa Mulungu (4)

      • Ananena kuti Yobu ndi wodzikuza (7-9)

      • ‘Mulungu sakhulupirira angelo ake’ (15)

      • ‘Munthu amene amavutika ndi woipa’ (20-24)

  • 16

    • Yankho la Yobu (1-22)

      • “Ndinu otonthoza obweretsa mavuto” (2)

      • Ananena kuti Mulungu wamuponyera mivi (12)

  • 17

    • Yankho la Yobu likupitirira (1-16)

      • “Anthu onyoza andizungulira” (2)

      • “Iye wachititsa kuti anthu azindinyoza” (6)

      • “Ku Manda kudzakhala kunyumba kwanga” (13)

  • 18

    • Mawu achiwiri a Bilidadi (1-21)

      • Anafotokoza zimene zimachitikira anthu ochimwa (5-20)

      • Ananena kuti Yobu sadziwa Mulungu (21)

  • 19

    • Yankho la Yobu (1-29)

      • Anakana kudzudzulidwa ndi anzake achinyengo (1-6)

      • Ananena kuti anzake apamtima amuthawa (13-19)

      • “Wondiwombola ali moyo” (25)

  • 20

    • Mawu achiwiri a Zofari (1-29)

      • Anaona kuti Yobu wamunyoza (2, 3)

      • Ananena kuti Yobu ndi woipa (5)

      • Ananena kuti Yobu amasangalala kuchita machimo (12, 13)

  • 21

    • Yankho la Yobu (1-34)

      • ‘Nʼchifukwa chiyani anthu oipa zinthu zimawayendera bwino?’ (7-13)

      • Anaonetsa kuti anzakewo anali achinyengo (27-34)

  • 22

    • Mawu achitatu a Elifazi (1-30)

      • ‘Kodi munthu angachite chilichonse chopindulitsa Mulungu?’ (2, 3)

      • Ananena kuti Yobu ndi wadyera komanso wopanda chilungamo (6-9)

      • ‘Bwerera kwa Mulungu ndipo udzabwezeretsedwa mwakale’ (23)

  • 23

    • Yankho la Yobu (1-17)

      • Ankafuna kupititsa mlandu wake kwa Mulungu (1-7)

      • Ananena kuti Mulungu sakupezeka (8, 9)

      • “Ndapitiriza kuyenda mʼnjira yake ndipo sindinapatuke” (11)

  • 24

    • Yankho la Yobu likupitirira (1-25)

      • ‘Nʼchifukwa chiyani Mulungu sanakhazikitse nthawi’ (1)

      • Ananena kuti Mulungu amalola kuti zinthu zoipa zizichitika (12)

      • Anthu ochimwa amakonda mdima (13-17)

  • 25

    • Mawu achitatu a Bilidadi (1-6)

      • ‘Kodi munthu angakhale wosalakwa pamaso pa Mulungu?’ (4)

      • Ananena kuti kukhulupirika kwa munthu nʼkopanda phindu (5, 6)

  • 26

    • Yankho la Yobu (1-14)

      • “Komatu ndiye wathandiza munthu wopanda mphamvu!” (1-4)

      • ‘Mulungu anaika dziko lapansi mʼmalere’ (7)

      • ‘Kambali kakangʼono chabe ka zochita za Mulungu’ (14)

  • 27

    • Yobu anatsimikiza ndi mtima wonse kukhalabe wokhulupirika (1-23)

      • “Sindidzasiya kukhala wokhulupirika” (5)

      • Anthu oipa alibe chiyembekezo (8)

      • “Nʼchifukwa chiyani mukulankhula zopanda nzeru?” (12)

      • Anthu oipa sapindula chilichonse (13-23)

  • 28

    • Yobu anasiyanitsa chuma chapadziko lapansi ndi nzeru (1-28)

      • Zimene anthu amachita akamakumba miyala yamtengo wapatali (1-11)

      • Nzeru ndi zamtengo wapatali kuposa ngale (18)

      • Kuopa Yehova ndi nzeru zenizeni (28)

  • 29

    • Yobu anakumbukira masiku amene ankasangalala asanayambe kukumana ndi mayesero (1-25)

      • Ankalemekezedwa pageti la mzinda (7-10)

      • Ankachita zinthu zachilungamo (11-17)

      • Aliyense ankamvera malangizo ake (21-23)

  • 30

    • Yobu anafotokoza mmene zinthu zinasinthira pa moyo wake (1-31)

      • Anthu opanda pake ankamunyoza (1-15)

      • Ankaona kuti Mulungu sakumuthandiza (20, 21)

      • “Khungu langa lada” (30)

  • 31

    • Yobu ananena kuti adzapitirizabe kukhala wokhulupirika (1-40)

      • “Pangano ndi maso anga” (1)

      • Anapempha kuti Mulungu amuyeze pasikelo (6)

      • Sanali wachigololo (9-12)

      • Sankakonda ndalama (24, 25)

      • Sankalambira mafano (26-28)

  • 32

    • Elihu, amene anali wachinyamata anayamba kulankhula (1-22)

      • Anakwiyira Yobu ndi anzakewo (2, 3)

      • Anayembekezera mwaulemu asanayambe kulankhula (6, 7)

      • Si zaka zokha zimene zimapangitsa kuti munthu akhale wanzeru (9)

      • Elihu anali wokonzeka kulankhula (18-20)

  • 33

    • Elihu anadzudzula Yobu chifukwa chodzilungamitsa (1-33)

      • Dipo linapezeka (24)

      • Adzakhala ndi mphamvu ngati mmene analili ali mnyamata (25)

  • 34

    • Elihu ananena kuti Mulungu amachita zinthu mwachilungamo (1-37)

      • Yobu ananena kuti Mulungu sanamuchitire zinthu mwachilungamo (5)

      • Mulungu woona sachita zoipa (10)

      • Yobu sankadziwa zinthu zina (35)

  • 35

    • Elihu anasonyeza kuti maganizo a Yobu anali olakwika (1-16)

      • Yobu ananena kuti anali wolungama kuposa Mulungu (2)

      • Mulungu ali pamwamba kwambiri, ndipo sakhudzidwa ndi tchimo (5, 6)

      • Yobu ankayenera kuyembekezera Mulungu (14)

  • 36

    • Elihu anatamanda Mulungu chifukwa cha mphamvu zake zopanda malire (1-33)

      • Anthu omvera zinthu zimawayendera bwino; anthu oipa amakanidwa (11-13)

      • ‘Kodi pali mphunzitsi winanso wofanana ndi Mulungu?’ (22)

      • Yobu ankayenera kulemekeza Mulungu (24)

      • “Mulungu ndi wamkulu kuposa mmene tikudziwira” (26)

      • Mulungu amalamulira mvula komanso mphezi (27-33)

  • 37

    • Mphamvu zamʼchilengedwe zimasonyeza kuti Mulungu ndi wamkulu (1-24)

      • Mulungu angaimitse zochita za anthu (7)

      • ‘Ganizirani ntchito zodabwitsa za Mulungu’ (14)

      • Anthu sangathe kumumvetsa Mulungu (23)

      • Munthu aliyense asamadzione kuti ndi wanzeru (24)

  • 38

    • Yehova anasonyeza kuti munthu ndi wamngʼono (1-41)

      • ‘Unali kuti pamene dziko lapansi linkalengedwa?’ (4-6)

      • Ana a Mulungu anafuula mosangalala (7)

      • Mafunso okhudza zinthu zodabwitsa zamʼchilengedwe (8-32)

      • “Malamulo amene zinthu zakuthambo zimatsatira” (33)

  • 39

    • Nyama zimene Mulungu analenga zimasonyeza kuti pali zambiri zimene anthu sakudziwa (1-30)

      • Mbuzi zamʼmapiri komanso mphoyo (1-4)

      • Bulu wamʼtchire (5-8)

      • Ngʼombe yamphongo yamʼtchire (9-12)

      • Nthiwatiwa (13-18)

      • Hatchi (19-25)

      • Kabawi komanso chiwombankhanga (26-30)

  • 40

    • Mafunso enanso ochokera kwa Yehova (1-24)

      • Yobu anavomereza kuti alibe chonena (3-5)

      • “Kodi unganene kuti ndine wopanda chilungamo?” (8)

      • Mulungu anafotokoza mphamvu za mvuu (15-24)

  • 41

    • Mulungu anafotokoza kudabwitsa kwa ngʼona (1-34)

  • 42

    • Zimene Yobu anayankha Yehova (1-6)

    • Mulungu anadzudzula anzake atatu a Yobu (7-9)

    • Yehova anabwezeretsa mmene zinthu zinaliri pa moyo wa Yobu (10-17)

      • Ana aamuna ndi aakazi a Yobu (13-15)