Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene zili mu Oweruza

Machaputala

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21

Mitu

  • 1

    • Madera omwe Yuda ndi Simiyoni anagonjetsa (1-20)

    • Ayebusi anapitiriza kukhala ku Yerusalemu (21)

    • Yosefe anagonjetsa Beteli (22-26)

    • Akanani ena anasiyidwa (27-36)

  • 2

    • Chenjezo la mngelo wa Yehova (1-5)

    • Imfa ya Yoswa (6-10)

    • Oweruza anayamba kupulumutsa Isiraeli (11-23)

  • 3

    • Yehova anayesa Aisiraeli (1-6)

    • Otiniyeli, woweruza woyamba (7-11)

    • Woweruza Ehudi anapha mfumu yonenepa Egiloni (12-30)

    • Woweruza Samagara (31)

  • 4

    • Mfumu Yabini ya ku Kanani inkapondereza Aisiraeli (1-3)

    • Mneneri wamkazi Debora ndi woweruza Baraki (4-16)

    • Yaeli anapha Sisera mkulu wa asilikali (17-24)

  • 5

    • Nyimbo imene Debora ndi Baraki anaimba atapambana (1-31)

      • Nyenyezi zinamenya nkhondo yolimbana ndi Sisera (20)

      • Mtsinje wa Kisoni unasefukira (21)

      • Okonda Yehova ali ngati dzuwa (31)

  • 6

    • Amidiyani ankapondereza Aisiraeli (1-10)

    • Mngelo anatsimikizira woweruza Gidiyoni kuti amuthandiza (11-24)

    • Gidiyoni anagwetsa guwa lansembe la Baala (25-32)

    • Mzimu wa Mulungu unathandiza Gidiyoni (33-35)

    • Kuyesa ndi ubweya wa nkhosa (36-40)

  • 7

    • Gidiyoni ndi anthu ake 300 (1-8)

    • Asilikali a Gidiyoni anagonjetsa Amidiyani (9-25)

      • “Nkhondo ya Yehova ndi ya Gidiyoni!” (20)

      • Chipwirikiti mumsasa wa Amidiyani (21, 22)

  • 8

    • Amuna a ku Efuraimu anakangana ndi Gidiyoni (1-3)

    • Mafumu a ku Midiyani anathamangitsidwa nʼkuphedwa (4-21)

    • Gidiyoni anakana ufumu (22-27)

    • Mbiri ya Gidiyoni (28-35)

  • 9

    • Abimeleki anakhala mfumu ku Sekemu (1-6)

    • Mwambi wa Yotamu (7-21)

    • Ulamuliro wankhanza wa Abimeleki (22-33)

    • Abimeleki anapha anthu ku Sekemu (34-49)

    • Mzimayi anavulaza Abimeleki ndipo anafa (50-57)

  • 10

    • Oweruza Tola ndi Yaeli (1-5)

    • Aisiraeli anasiya Mulungu kenako nʼkulapa (6-16)

    • Aamoni anaopseza Aisiraeli (17, 18)

  • 11

    • Woweruza Yefita anathamangitsidwa kenako anakhala mtsogoleri (1-11)

    • Yefita anakambirana ndi Aamoni (12-28)

    • Lonjezo la Yefita komanso mwana wake wamkazi (29-40)

      • Mwana wa Yefita sanakwatiwe (38-40)

  • 12

    • Anakangana ndi amuna a ku Efuraimu (1-7)

      • Anawayesa ndi mawu akuti “Shiboleti” (6)

    • Oweruza Ibizani, Eloni ndi Abidoni (8-15)

  • 13

    • Mngelo anapita kwa Manowa ndi mkazi wake (1-23)

    • Kubadwa kwa Samisoni (24, 25)

  • 14

    • Woweruza Samisoni ankafuna mkazi wa Chifilisiti (1-4)

    • Mzimu wa Yehova unathandiza Samisoni kupha mkango (5-9)

    • Mwambi wa Samisoni pa ukwati (10-19)

    • Mkazi wa Samisoni anaperekedwa kwa mwamuna wina (20)

  • 15

    • Samisoni anabwezera Afilisiti (1-20)

  • 16

    • Samisoni ku Gaza (1-3)

    • Samisoni ndi Delila (4-22)

    • Samisoni anabwezera nʼkufa (23-31)

  • 17

    • Mafano a Mika ndi wansembe wake (1-13)

  • 18

    • Anthu a fuko la Dani ankafufuza malo (1-31)

      • Mafano a Mika ndi wansembe wake anatengedwa (14-20)

      • Anagonjetsa Laisi nʼkusintha dzina kukhala Dani (27-29)

      • Kulambira mafano ku Dani (30, 31)

  • 19

    • Anthu a fuko la Benjamini anagwirira mkazi ku Gibeya (1-30)

  • 20

    • Nkhondo yomenyana ndi fuko la Benjamini (1-48)

  • 21

    • Fuko la Benjamini linapulumutsidwa (1-25)