Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Numeri

Machaputala

Mitu

  • 1

    • Kalembera wa amuna oyenera kupita kunkhondo (1-46)

    • Alevi sankayenera kupita nawo kunkhondo (47-51)

    • Dongosolo lomangira matenti mumsasa (52-54)

  • 2

    • Msasa anaugawa mʼmagulu a mafuko atatu (1-34)

      • Gulu la mafuko atatu la Yuda linali mbali yakumʼmawa (3-9)

      • Gulu la mafuko atatu la Rubeni linali mbali yakumʼmwera (10-16)

      • Msasa wa Alevi unali pakati (17)

      • Gulu la mafuko atatu la Efuraimu linali mbali yakumadzulo (18-24)

      • Gulu la mafuko atatu la Dani linali mbali yakumpoto (25-31)

      • Chiwerengero cha amuna onse amene analembedwa (32-34)

  • 3

    • Ana aamuna a Aroni (1-4)

    • Alevi anasankhidwa kuti azitumikira (5-39)

    • Kuwombola ana oyamba kubadwa (40-51)

  • 4

    • Utumiki wa Akohati (1-20)

    • Utumiki wa Agerisoni (21-28)

    • Utumiki wa Amerari (29-33)

    • Mmene kalembera anayendera (34-49)

  • 5

    • Kuika munthu wodetsedwa kwayekha (1-4)

    • Kuulula tchimo komanso kulipira (5-10)

    • Kumwetsa madzi munthu amene akumuganizira kuti wachita chigololo (11-31)

  • 6

    • Lumbiro la Unaziri (1-21)

    • Madalitso ochokera kwa ansembe (22-27)

  • 7

    • Nsembe zimene anapereka pa mwambo wotsegulira chihema (1-89)

  • 8

    • Aroni anayatsa nyale 7 (1-4)

    • Alevi anayeretsedwa nʼkuyamba kutumikira (5-22)

    • Zaka zimene Alevi ankayenera kuyamba komanso kusiya utumiki (23-26)

  • 9

    • Anthu amene analephera kuchita Pasika ankachita mwezi wotsatira (1-14)

    • Mtambo ndi moto zinkakhala pamwamba pa chihema (15-23)

  • 10

    • Malipenga asiliva (1-10)

    • Anachoka ku Sinai (11-13)

    • Dongosolo la kayendedwe (14-28)

    • Hobabu anapemphedwa kuti alondolere njira Aisiraeli (29-34)

    • Pemphero limene Mose anapereka ponyamuka (35, 36)

  • 11

    • Mulungu anawabweretsera moto chifukwa chodandaula (1-3)

    • Anthu anayamba kulirira nyama (4-9)

    • Mose ankadziona kuti ndi wosayenerera (10-15)

    • Yehova anapereka mzimu kwa akulu 70 (16-25)

    • Eledadi ndi Medadi; Yoswa anachita nsanje chifukwa choti ankadera nkhawa Mose (26-30)

    • Anabweretsa zinziri; anthu analangidwa chifukwa cha dyera (31-35)

  • 12

    • Miriamu ndi Aroni anakangana ndi Mose (1-3)

      • Mose anali wofatsa kuposa munthu aliyense (3)

    • Yehova anaikira kumbuyo Mose (4-8)

    • Miriamu anachita khate (9-16)

  • 13

    • Anatumiza anthu 12 kuti akafufuze zokhudza dziko la Kanani (1-24)

    • Anthu 10 anabweretsa lipoti loipa (25-33)

  • 14

    • Anthu ankafuna kubwerera ku Iguputo (1-10)

      • Lipoti labwino la Yoswa ndi Kalebe (6-9)

    • Yehova anakwiya; Mose anapepesa (11-19)

    • Chilango: zaka 40 mʼchipululu (20-38)

    • Aisiraeli anagonjetsedwa ndi Aamaleki (39-45)

  • 15

    • Malamulo okhudza nsembe (1-21)

      • Malamulo ofanana kwa nzika ndi alendo (15, 16)

    • Nsembe za machimo amene munthu wachita mosadziwa (22-29)

    • Chilango cha munthu amene wachimwa mwadala (30, 31)

    • Munthu amene anaphwanya Sabata anamupha (32-36)

    • Zovala zizikhala ndi ulusi mʼmphepete (37-41)

  • 16

    • Kupanduka kwa Kora, Datani ndi Abiramu (1-19)

    • Anthu opandukawo analandira chilango (20-50)

  • 17

    • Ndodo ya Aroni inachita maluwa monga chizindikiro (1-13)

  • 18

    • Ntchito za ansembe ndi Alevi (1-7)

    • Gawo limene ansembe ankalandira (8-19)

      • Pangano lamchere (19)

    • Alevi azilandira komanso kupereka chakhumi (20-32)

  • 19

    • Ngʼombe yofiira komanso madzi oyeretsera (1-22)

  • 20

    • Miriamu anamwalira ku Kadesi (1)

    • Mose anamenya thanthwe nʼkuchimwa (2-13)

    • Aedomu anakana kuti Aisiraeli adutse mʼdziko lawo (14-21)

    • Imfa ya Aroni (22-29)

  • 21

    • Mfumu ya ku Aradi inagonjetsedwa (1-3)

    • Njoka yakopa (4-9)

    • Aisiraeli anayenda mozungulira Mowabu (10-20)

    • Sihoni Mfumu ya Aamori inagonjetsedwa (21-30)

    • Ogi Mfumu ya Aamori inagonjetsedwa (31-35)

  • 22

    • Balaki analemba ganyu Balamu (1-21)

    • Bulu wa Balamu analankhula (22-41)

  • 23

    • Ndakatulo yoyamba ya Balamu (1-12)

    • Ndakatulo yachiwiri ya Balamu (13-30)

  • 24

    • Ndakatulo yachitatu ya Balamu (1-11)

    • Ndakatulo ya 4 ya Balamu (12-25)

  • 25

    • Aisiraeli anachimwa ndi akazi a Chimowabu (1-5)

    • Pinihasi sanalekerere zoipa (6-18)

  • 26

    • Kalembera wachiwiri wa mafuko a Isiraeli (1-65)

  • 27

    • Ana aakazi a Tselofekadi (1-11)

    • Yoswa anasankhidwa kuti alowe mʼmalo mwa Mose (12-23)

  • 28

    • Kaperekedwe ka nsembe zosiyanasiyana (1-31)

      • Nsembe za tsiku ndi tsiku (1-8)

      • Za tsiku la Sabata (9, 10)

      • Nsembe za mwezi ndi mwezi (11-15)

      • Za Pasika (16-25)

      • Za Chikondwerero cha Masabata (26-31)

  • 29

    • Kaperekedwe ka nsembe zosiyanasiyana (1-40)

      • Tsiku loliza lipenga (1-6)

      • Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo (7-11)

      • Chikondwerero cha Misasa (12-38)

  • 30

    • Malumbiro a amuna (1, 2)

    • Malumbiro a akazi ndi ana aakazi (3-16)

  • 31

    • Kubwezera Amidiyani (1-12)

      • Balamu anaphedwa (8)

    • Malamulo okhudza zinthu zotengedwa kunkhondo (13-54)

  • 32

    • Anayamba kukhala kumʼmawa kwa Yorodano (1-42)

  • 33

    • Malo amene Aisiraeli anaima mʼchipululu (1-49)

    • Malangizo oti akawatsatire pogonjetsa Akanani (50-56)

  • 34

    • Malire a dziko la Kanani (1-15)

    • Amuna amene anawapatsa ntchito yogawa malo (16-29)

  • 35

    • Mizinda ya Alevi (1-8)

    • Mizinda yothawirako (9-34)

  • 36

    • Lamulo lokhudza ukwati wa akazi amene akulandira cholowa (1-13)