Mlaliki 1:1-18

  • Zinthu zonse nʼzachabechabe (1-11)

    • Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale (4)

    • Zinthu zamʼchilengedwe zimachitika mobwerezabwereza (5-7)

    • Palibe chatsopano padziko lapansi pano (9)

  • Nzeru za anthu nʼzoperewera (12-18)

    • Kuthamangitsa mphepo (14)

1  Mawu a wosonkhanitsa anthu,+ mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu.+   Wosonkhanitsa anthu wanena kuti: “Nʼzachabechabe!Nʼzachabechabe! Zinthu zonse nʼzachabechabe!”+   Kodi munthu amapeza chiyani pa ntchito yake yonse yovutaImene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano?*+   Mʼbadwo umapita ndipo mʼbadwo wina umabwera,Koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.+   Dzuwa limatuluka* ndipo dzuwa limalowa,Kenako limathamanga* kupita kumalo amene limatulukira kuti likatulukenso.+   Mphepo imapita kumʼmwera ndipo imazungulira mpaka kukafika kumpoto.Imangozungulira mobwerezabwereza. Mphepoyo imapitiriza kuzungulira.   Mitsinje yonse* imakathira mʼnyanja koma nyanjayo sidzaza.+ Imabwerera kumalo kumene ikuchokera kuti ikayambirenso kuyenda.+   Zinthu zonse nʼzotopetsa.Palibe aliyense amene angazifotokoze. Diso silikhuta ndi kuona,Ndipo khutu silidzaza chifukwa cha kumva.   Zimene zinalipo nʼzimene zidzakhaleponso,Ndipo zimene zinachitidwa nʼzimene zidzachitidwenso.Palibe chatsopano padziko lapansi pano.+ 10  Kodi chilipo chimene munthu anganene kuti, “Wachiona ichi, nʼchatsopanotu chimenechi?” Ayi, chakhalapo kuyambira kalekale.Chinalipo kale ife tisanabadwe. 11  Palibe amene amakumbukira anthu akale.Ndipo palibe amene adzakumbukire amene anabwera pambuyo pa anthu akalewo.Iwowanso sadzakumbukiridwa ndi amene adzabwere pambuyo pawo.+ 12  Ine wosonkhanitsa anthu, ndine mfumu ya Isiraeli ku Yerusalemu.+ 13  Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndiphunzire ndi kufufuza mwanzeru+ zonse zimene zachitidwa padziko lapansi.+ Ndinafufuza ntchito yotopetsa kwambiri imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azigwira. 14  Ndinaona ntchito zonse zimene zinachitidwa padziko lapansi pano,Ndipo ndinapeza kuti zonse ndi zachabechabe, zili ngati kuthamangitsa mphepo.+ 15  Chinthu chokhota sichingawongoledwe,Ndipo chimene palibe sichingawerengedwe nʼkomwe. 16  Choncho ndinanena mumtima mwanga kuti: “Ine ndapeza nzeru zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu+ ine ndisanakhalepo. Ndipo mtima wanga wamvetsa zinthu zambiri chifukwa cha nzeru ndi kudziwa zinthu.”+ 17  Ndinayesetsa ndi mtima wonse kuti ndidziwe nzeru, ndidziwe misala* komanso kuti ndidziwe uchitsiru.+ Koma zimenezinso zili ngati kuthamangitsa mphepo. 18  Chifukwa nzeru zikachuluka, zokhumudwitsa zimachulukanso,Choncho amene amadziwa zinthu zambiri amakhalanso ndi zopweteka zambiri.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “pansi pa dzuwa.”
Kapena kuti, “limawala.”
Kapena kuti, “limabwerera mwawefuwefu.”
Kapena kuti, “Mitsinje imene imayenda nthawi yamvula yokha.”
Kapena kuti, “uchitsiru wopitirira muyezo.”