Wolembedwa ndi Maliko 4:1-41

  • MAFANIZO OKHUDZA UFUMU (1-34)

    • Wofesa mbewu (1-9)

    • Chifukwa chake Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo (10-12)

    • Tanthauzo la fanizo la wofesa mbewu (13-20)

    • Nyale saivindikira ndi dengu (21-23)

    • Muyezo umene mukuyezera (24, 25)

    • Wofesa mbewu amene amagona (26-29)

    • Kanjere ka mpiru (30-32)

    • Anagwiritsa ntchito mafanizo (33, 34)

  • Yesu analetsa mafunde (35-41)

4  Yesu anayambanso kuphunzitsa mʼmphepete mwa nyanja ndipo chigulu cha anthu chinasonkhana pafupi ndi iye. Choncho iye anakwera ngalawa nʼkukhala mʼngalawamo chapatali pangʼono ndi anthuwo, koma gulu lonse la anthulo linakhala mʼmphepete mwa nyanjayo.+  Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri pogwiritsa ntchito mafanizo.+ Powaphunzitsapo ankawauza kuti:+  “Tamverani! Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu.+  Pamene ankafesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa msewu ndipo kunabwera mbalame nʼkuzidya.  Zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira ndipo zinamera mwamsanga chifukwa dothilo linali losazama.+  Koma dzuwa litawala kwambiri zinawauka ndipo zinafota chifukwa zinalibe mizu.  Mbewu zina zinagwera paminga ndipo mingazo zinakula nʼkulepheretsa mbewuzo kukula moti sizinabereke chipatso chilichonse.+  Koma zina zinagwera panthaka yabwino ndipo zinamera nʼkukula, moti zinayamba kubereka zipatso. Mbewu ina inabereka zipatso 30, ina 60 ndipo ina 100.”+  Kenako anawonjezera mawu akuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+ 10  Tsopano pamene anali payekha, ena amene anali naye chapafupi limodzi ndi atumwi 12 aja, anayamba kumufunsa zokhudza mafanizo aja.+ 11  Iye anawauza kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi woti mumvetse chinsinsi chopatulika+ cha Ufumu wa Mulungu. Koma amene ali kunja amauzidwa zonse pogwiritsa ntchito mafanizo+ 12  kuti kuyangʼana, aziyangʼana ndithu koma asamaone. Kumva, azimva ndithu koma asamazindikire tanthauzo lake. Komanso kuti asatembenuke nʼkukhululukidwa.”+ 13  Iye anawauzanso kuti: “Ngati simukumvetsa fanizo ili, ndiye mungamvetse bwanji mafanizo ena onse? 14  Wofesayo amafesa mawu.+ 15  Choncho mbewu zimene zimagwera mʼmbali mwa msewu ndi mawu amene afesedwa mwa anthu amene amati akangomva mawuwo, Satana amabwera+ nʼkudzachotsa mawu amene afesedwa mwa iwo.+ 16  Mofanana ndi zimenezi, mbewu zimene zafesedwa pamiyala ndi mawu amene afesedwa mwa anthu omwe amati akangomva mawuwo, amawalandira mosangalala.+ 17  Koma iwo amakhala opanda mizu ndipo amapitirizabe kwakanthawi. Ndiyeno akangoyamba kuvutitsidwa kapena kuzunzidwa chifukwa cha mawuwo, amapunthwa. 18  Ndiye palinso mbewu zina zimene zimafesedwa paminga. Amenewa ndi anthu amene amamva mawu,+ 19  koma nkhawa za moyo+ wamʼnthawi* ino, chinyengo champhamvu cha chuma+ komanso kulakalaka zinthu+ zina zonse, zimalowa mʼmitima yawo nʼkulepheretsa mawuwo kukula ndipo sabereka zipatso. 20  Pomaliza, mbewu zimene zinafesedwa panthaka yabwino ndi anthu amene amamvetsera mawu ndipo amawalandira bwino nʼkubereka zipatso wina 30, wina 60 ndipo wina 100.”+ 21  Iye anawauzanso kuti: “Nyale saivindikira ndi dengu* kapena kuiika pansi pa bedi, amatero ngati? Koma amaiika pachoikapo nyale,+ si choncho kodi? 22  Chifukwa palibe chobisika chimene sichidzaululika ndipo palibe chimene chimasungidwa mwachinsinsi kwambiri chimene sichidzaululika.+ 23  Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+ 24  Anapitiriza kuwauza kuti: “Mvetserani mosamala zimene ndikunenazi.+ Muyezo umene mukuyezera ena, nanunso adzakuyezerani womwewo. Inde, adzakuwonjezerani zochuluka. 25  Chifukwa amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka,+ koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.”+ 26  Iye anapitiriza kulankhula kuti: “Ufumu wa Mulungu uli ngati mmene munthu amamwazira mbewu panthaka. 27  Munthuyo amagona usiku nʼkumadzuka kukacha ndipo mbewuzo zimamera nʼkukula. Koma mmene zimenezi zimachitikira, mwiniwakeyo sadziwa. 28  Pangʼonopangʼono, payokha nthaka ija imabereka zipatso. Choyamba tirigu amakula, kenako amatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera mʼngalamo. 29  Koma mbewuzo zikacha, iye amazimweta ndi chikwakwa chifukwa nthawi yokolola yakwana.” 30  Iye anapitiriza kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani kapena tingaufotokoze ndi fanizo lotani? 31  Uli ngati kanjere ka mpiru,* kamene pa nthawi yofesa kamakhala kakangʼono kwambiri kuposa njere zonse zapadziko lapansi.+ 32  Koma akakafesa, kamamera nʼkukula kuposa mbewu zonse zakudimba ndipo kamapanga nthambi zikuluzikulu, moti mbalame zamumlengalenga zimatha kupeza malo okhala mumthunzi wake.” 33  Iye anawauza mawu pogwiritsa ntchito mafanizo ambiri+ ofanana ndi amenewa, malinga ndi zimene akanakwanitsa kumva. 34  Ndithudi, nthawi zonse iye ankalankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo, koma kumbali ankafotokoza zinthu zonse kwa ophunzira ake.+ 35  Tsiku limenelo madzulo, iye anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.”+ 36  Choncho atauza gulu la anthulo kuti lizipita, ophunzirawo anachoka naye pangalawa imene anakwera ija, koma analinso ndi ngalawa zina.+ 37  Kenako kunayamba chimphepo champhamvu chamkuntho, ndipo mafunde ankawomba ngalawayo moti inangotsala pangʼono kumira.+ 38  Koma Yesu anali kumbuyo kwa ngalawayo akugona, atatsamira pilo. Choncho anamudzutsa nʼkumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi sizikukukhudzani kuti tikufa?” 39  Atamva zimenezi anadzuka nʼkudzudzula mphepoyo komanso kuuza nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!”+ Atatero mphepoyo inaleka ndipo kenako panachita bata lalikulu. 40  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi? Kodi mudakali opandiratu chikhulupiriro?” 41  Koma iwo anagwidwa ndi mantha aakulu ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani kwenikweni? Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “dengu loyezera.”
“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakangʼono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita 4 ndipo kamakhala ndi nthambi.