Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Hoseya

Machaputala

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14

Mitu

  • 1

    • Mkazi wa Hoseya ndiponso ana amene anabereka (1-9)

      • Yezereeli (4), Lo-ruhama (6), ndi Lo-ami (9)

    • Chiyembekezo cha kubwezeretsa komanso mgwirizano (10, 11)

  • 2

    • Aisiraeli osakhulupirika analangidwa (1-13)

    • Yehova anakhalanso mwamuna wawo (14-23)

      • “Adzanditchula kuti Mwamuna wanga” (16)

  • 3

    • Hoseya anagula mkazi wake wachigololo (1-3)

    • Aisiraeli adzabwerera kwa Yehova (4, 5)

  • 4

    • Yehova anali ndi mlandu woti aimbe Aisiraeli (1-8)

      • Panalibe amene ankadziwa Mulungu mʼdzikolo (1)

    • Aisiraeli ankalambira mafano komanso kuchita chiwerewere (9-19)

      • Mtima wachiwerewere unawasocheretsa (12)

  • 5

    • Chiweruzo cha Efuraimu ndi Yuda (1-15)

  • 6

    • Anawauza kuti abwerere kwa Yehova (1-3)

    • Anthu anasonyeza chikondi chokhulupirika chosakhalitsa (4-6)

      • Chikondi chokhulupirika chimaposa nsembe (6)

    • Anthu anali ndi khalidwe lochititsa manyazi (7-11)

  • 7

    • Zoipa za Efuraimu (1-16)

      • Sangathawe ukonde wa Mulungu (12)

  • 8

    • Zotsatira za kulambira mafano (1-14)

      • Kufesa mphepo, kukolola mphepo yamkuntho (7)

      • Aisiraeli anaiwala amene anawapanga (14)

  • 9

    • Mulungu anakana Efuraimu chifukwa cha machimo ake (1-17)

      • Anadzipereka kwa mulungu wochititsa manyazi (10)

  • 10

    • Aisiraeli, omwe ndi mtengo wa mpesa wowonongeka, adzawonongedwa (1-15)

      • Kufesa ndiponso kukolola (12, 13)

  • 11

    • Mulungu anakonda Isiraeli kuyambira ali mnyamata (1-12)

      • ‘Ndinaitana mwana wanga kuti atuluke mu Iguputo’ (1)

  • 12

    • Efuraimu ayenera kubwerera kwa Yehova (1-14)

      • Yakobo analimbana ndi Mulungu (3)

      • Yakobo analira kuti apeze madalitso a Mulungu (4)

  • 13

    • Efuraimu anaiwala Yehova chifukwa cholambira mafano (1-16)

      • ‘Imfa, kodi mphamvu yako ili kuti?’ (14)

  • 14

    • Anapemphedwa kuti abwerere kwa Yehova (1-3)

      • Kutamanda Mulungu ndi pakamwa (2)

    • Aisiraeli osakhulupirika anachiritsidwa (4-9)