Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Ezekieli

Machaputala

Mitu

  • 1

    • Ezekieli anaona masomphenya a Mulungu ku Babulo (1-3)

    • Masomphenya a galeta lakumwamba la Yehova (4-28)

      • Mphepo yamkuntho, mtambo ndi moto (4)

      • Angelo 4 (5-14)

      • Mawilo 4 (15-21)

      • Thambo lonyezimira ngati madzi oundana (22-24)

      • Mpando wachifumu wa Yehova (25-28)

  • 2

    • Ezekieli anamupatsa ntchito ya uneneri (1-10)

      • ‘Kaya akamvetsera kapena ayi’ (5)

      • Anamuonetsa mpukutu wa nyimbo zoimba polira (9, 10)

  • 3

    • Ezekieli anauzidwa kuti adye mpukutu umene Mulungu anamupatsa (1-15)

    • Ezekieli anaikidwa kuti akhale mlonda (16-27)

      • Kunyalanyaza kungapangitse kuti tikhale ndi mlandu wamagazi (18-21)

  • 4

    • Anasonyeza zimene adani adzachite poukira mzinda wa Yerusalemu (1-17)

      • Kunyamula zolakwa kwa masiku 390 komanso masiku 40 (4-7)

  • 5

    • Anasonyeza zimene zidzachitike Yerusalemu akamadzawonongedwa (1-17)

      • Mneneri anameta tsitsi nʼkuligawa magawo atatu (1-4)

      • Yerusalemu anachita zoipa kuposa anthu a mitundu ina (7-9)

      • Anthu opanduka adzalangidwa mʼnjira zitatu (12)

  • 6

    • Tsoka limene lidzagwere mapiri a ku Isiraeli (1-14)

      • Mafano onyansa adzachititsidwa manyazi (4-6)

      • “Inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova” (7)

  • 7

    • Mapeto afika (1-27)

      • Tsoka loti silinaonekepo (5)

      • Ndalama zidzatayidwa mʼmisewu (19)

      • Kachisi adzaipitsidwa (22)

  • 8

    • Ezekieli anapititsidwa ku Yerusalemu mʼmasomphenya (1-4)

    • Anaona zinthu zonyansa mʼkachisi (5-18)

      • Azimayi ankalilira mulungu wotchedwa Tamuzi (14)

      • Amuna ankalambira dzuwa (16)

  • 9

    • Anthu 6 opereka chilango komanso munthu amene anali ndi kachikwama konyamuliramo inki ndi zolembera (1-11)

      • Chiweruzo chinayambira pamalo opatulika (6)

  • 10

    • Anatenga moto kuchokera pakati pa mawilo (1-8)

    • Anafotokoza zokhudza akerubi komanso mawilo (9-17)

    • Ulemerero wa Yehova unachoka pakachisi (18-22)

  • 11

    • Anadzudzula akalonga oipa (1-13)

      • Mzinda anauyerekezera ndi mphika (3-12)

    • Lonjezo lakubwezeretsa (14-21)

      • Kupatsidwa “mzimu watsopano” (19)

    • Ulemerero wa Mulungu unachoka mu Yerusalemu (22, 23)

    • Ezekieli anabwerera ku Kasidi mʼmasomphenya (24, 25)

  • 12

    • Zinthu zimene Ezekieli anachita polosera kuti anthu adzatengedwa kupita ku ukapolo (1-20)

      • Katundu wopita naye ku ukapolo (1-7)

      • Mtsogoleri adzachoka kuli mdima (8-16)

      • Adzadya chakudya ali ndi nkhawa ndipo adzamwa madzi ali ndi mantha aakulu (17-20)

    • Mawu achinyengo sadzakwaniritsidwa (21-28)

      • “Palibe mawu aliwonse omwe ndalankhula amene sadzachitika pa nthawi yake” (28)

  • 13

    • Anadzudzula aneneri abodza (1-16)

      • Makoma opakidwa laimu adzagwa (10-12)

    • Anadzudzula aneneri aakazi (17-23)

  • 14

    • Olambira mafano adzalangidwa (1-11)

    • Chiweruzo cha Yerusalemu nʼchosapeweka (12-23)

      • Nowa, Danieli ndi Yobu anali olungama (14, 20)

  • 15

    • Yerusalemu ndi mtengo wa mpesa wopanda ntchito (1-8)

  • 16

    • Mulungu ankakonda Yerusalemu (1-63)

      • Anamupeza ngati mwana wotayidwa patchire (1-7)

      • Mulungu anamukongoletsa nʼkupangana naye pangano la ukwati (8-14)

      • Anakhala wosakhulupirika (15-34)

      • Anapatsidwa chilango chifukwa anali mkazi wachigololo (35-43)

      • Anamuyerekezera ndi Samariya komanso Sodomu (44-58)

      • Mulungu anakumbukira pangano lake (59-63)

  • 17

    • Fanizo la ziwombankhanga ziwiri ndi mtengo wa mpesa (1-21)

    • Nsonga yanthete idzakhala mtengo waukulu wa mkungudza (22-24)

  • 18

    • Aliyense adzaimbidwa mlandu chifukwa cha machimo ake (1-32)

      • Moyo umene wachimwa ndi umene udzafe (4)

      • Mwana sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake (19, 20)

      • Sasangalala ndi imfa ya munthu woipa (23)

      • Munthu wolapa amapulumutsa moyo wake (27, 28)

  • 19

    • Nyimbo yoimba polira yokhudza atsogoleri a Isiraeli (1-14)

  • 20

    • Mbiri ya kupanduka kwa Isiraeli (1-32)

    • Aisiraeli analonjezedwa kuti adzabwerera kwawo (33-44)

    • Ulosi wokhudza mbali yakumʼmwera (45-49)

  • 21

    • Mulungu adzasolola lupanga lake lachiweruzo (1-17)

    • Mfumu ya Babulo idzaukira Yerusalemu (18-24)

    • Mtsogoleri woipa wa Isiraeli adzachotsedwa pa udindo (25-27)

      • “Vula chisoti chachifumu” (26)

      • “Mpaka atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga” (27)

    • Lupanga lidzapha mbadwa za Amoni (28-32)

  • 22

    • Yerusalemu, mzinda wa mlandu wokhetsa magazi (1-16)

    • Isiraeli ali ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo (17-22)

    • Anadzudzula atsogoleri komanso anthu a mu Isiraeli (23-31)

  • 23

    • Akazi awiri apachibale omwe ndi osakhulupirika (1-49)

      • Ohola ndi Asuri (5-10)

      • Oholiba ndi Babulo komanso Iguputo (11-35)

      • Chilango chimene akazi awiriwo analandira (36-49)

  • 24

    • Yerusalemu ali ngati mphika wadzimbiri (1-14)

    • Imfa ya mkazi wa Ezekieli inali chizindikiro (15-27)

  • 25

    • Ulosi wokhudza Amoni (1-7)

    • Ulosi wokhudza Mowabu (8-11)

    • Ulosi wokhudza Edomu (12-14)

    • Ulosi wokhudza Filisitiya (15-17)

  • 26

    • Ulosi wokhudza Turo (1-21)

      • “Malo oyanikapo makoka” (5, 14)

      • Miyala komanso dothi zinaponyedwa mʼmadzi (12)

  • 27

    • Nyimbo yoimba polira yokhudza sitima yapamadzi ya Turo imene ikumira (1-36)

  • 28

    • Ulosi wokhudza mfumu ya Turo (1-10)

      • “Ndine mulungu” (2, 9)

    • Nyimbo yoimba polira yokhudza mfumu ya Turo (11-19)

      • “Iwe unali mu Edeni” (13)

      • “Kerubi wodzozedwa amene amagwira ntchito yoteteza” (14)

      • “Unayamba kuchita zinthu zosalungama” (15)

    • Ulosi wokhudza Sidoni (20-24)

    • Isiraeli adzabwezeretsedwa mwakale (25, 26)

  • 29

    • Ulosi wokhudza Farao (1-16)

    • Babulo anapatsidwa Iguputo monga malipiro ake (17-21)

  • 30

    • Ulosi wokhudza Iguputo (1-19)

      • Ananeneratu kuti Nebukadinezara adzaukira Iguputo (10)

    • Mphamvu za Farao zidzathyoka (20-26)

  • 31

    • Kugwa kwa Iguputo, yemwe ndi mtengo wautali wa mkungudza (1-18)

  • 32

    • Nyimbo yoimba polira yokhudza Farao ndi Iguputo (1-16)

    • Iguputo adzaikidwa mʼmanda limodzi ndi anthu osadulidwa (17-32)

  • 33

    • Ntchito za mlonda (1-20)

    • Nkhani yokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu (21, 22)

    • Uthenga wopita kwa anthu okhala mʼmabwinja a ku Yerusalemu (23-29)

    • Anthu atamva uthengawo, sanachite chilichonse (30-33)

      • Ezekieli ali ngati “nyimbo yachikondi” (32)

      • “Pakati pawo panali mneneri” (33)

  • 34

    • Ulosi wokhudza abusa a Isiraeli (1-10)

    • Yehova amasamalira nkhosa zake (11-31)

      • “Mtumiki wanga Davide” adzakhala mʼbusa wawo (23)

      • “Pangano la mtendere” (25)

  • 35

    • Ulosi wokhudza dera lamapiri la Seiri (1-15)

  • 36

    • Ulosi wokhudza mapiri a ku Isiraeli (1-15)

    • Isiraeli adzabwereranso mwakale (16-38)

      • ‘Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu’ (23)

      • “Ngati munda wa Edeni” (35)

  • 37

    • Masomphenya a chigwa cha mafupa ouma (1-14)

    • Ndodo ziwiri adzaziphatikiza pamodzi (15-28)

      • Mtundu umodzi wolamulidwa ndi mfumu imodzi (22)

      • Pangano la mtendere limene lidzakhalepo mpaka kalekale (26)

  • 38

    • Gogi adzaukira Isiraeli (1-16)

    • Yehova adzakwiyira Gogi (17-23)

      • ‘Mitundu ya anthu idzadziwa kuti ine ndine Yehova’ (23)

  • 39

    • Gogi ndi magulu ake a asilikali adzawonongedwa (1-10)

    • Adzaikidwa mʼmanda mʼChigwa cha Hamoni-Gogi (11-20)

    • Isiraeli adzabwereranso mwakale (21-29)

      • Mulungu anatsanulira mzimu wake pa Isiraeli (29)

  • 40

    • Ezekieli anamupititsa ku Isiraeli mʼmasomphenya (1, 2)

    • Ezekieli anaona masomphenya a kachisi (3, 4)

    • Mabwalo ndi mageti (5-47)

      • Geti lakunja lakumʼmawa (6-16)

      • Bwalo lakunja; mageti ena (17-26)

      • Bwalo lamkati ndi mageti (27-37)

      • Zipinda zochitiramo utumiki wapakachisi (38-46)

      • Guwa lansembe (47)

    • Khonde la kachisi (48, 49)

  • 41

    • Malo opatulika amʼkachisi (1-4)

    • Khoma komanso zipinda zamʼmbali (5-11)

    • Nyumba imene inali kumadzulo (12)

    • Anayeza nyumba zonse (13-15a)

    • Mkati mwa kachisi (15b-26)

  • 42

    • Nyumba imene inali ndi zipinda zodyera (1-14)

    • Anayeza mbali 4 za kachisi (15-20)

  • 43

    • Ulemerero wa Yehova unadzaza mʼkachisi (1-12)

    • Guwa lansembe (13-27)

  • 44

    • Geti lakumʼmawa linkakhala lotseka (1-3)

    • Malangizo okhudza alendo (4-9)

    • Malangizo okhudza Alevi ndi ansembe (10-31)

  • 45

    • Chopereka chopatulika komanso mzinda (1-6)

    • Malo amene mtsogoleri ankalandira (7, 8)

    • Atsogoleri azichita zinthu moona mtima (9-12)

    • Zinthu zimene anthu ankapereka komanso zimene mtsogoleri ankayenera kuchita (13-25)

  • 46

    • Nsembe zoperekedwa pazochitika zapadera (1-15)

    • Cholowa chochokera pamalo a mtsogoleri (16-18)

    • Malo amene ankawiritsirapo nsembe (19-24)

  • 47

    • Mtsinje wochokera mʼkachisi (1-12)

      • Madzi ankazama pangʼonopangʼono (2-5)

      • Madzi a mʼNyanja Yakufa anakhala abwino (8-10)

      • Madzi amʼzithaphwi sadzakhala abwino (11)

      • Mitengo ya zipatso komanso yochiritsa (12)

    • Malire a dziko (13-23)

  • 48

    • Kugawidwa kwa dziko (1-29)

    • Mageti 12 a mzinda (30-35)

      • Mzinda wotchedwa “Yehova Ali Kumeneko” (35)