Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Deuteronomo

Machaputala

Mitu

  • 1

    • Kuchoka paphiri la Horebe (1-8)

    • Anasankha atsogoleri komanso oweruza (9-18)

    • Anthu sanamvere ku Kadesi-barinea (19-46)

      • Aisiraeli anakana kulowa mʼdziko (26-33)

      • Analephera kugonjetsa Akanani (41-46)

  • 2

    • Anayenda mʼchipululu kwa zaka 38 (1-23)

    • Anagonjetsa Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni (24-37)

  • 3

    • Anagonjetsa Mfumu Ogi ya ku Basana (1-7)

    • Malire a dziko kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano (8-20)

    • Yoswa anauzidwa kuti asachite mantha (21, 22)

    • Mose sadzalowa mʼdziko (23-29)

  • 4

    • Anawalimbikitsa kuti akhale omvera (1-14)

      • Musaiwale zimene Mulungu anachita (9)

    • Yehova amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha (15-31)

    • Palibe Mulungu wina kupatulapo Yehova (32-40)

    • Mizinda yothawirako kumʼmawa kwa Yorodano (41-43)

    • Anawapatsa Chilamulo (44-49)

  • 5

    • Yehova anachita pangano ku Horebe (1-5)

    • Anabwereza kuwauza Malamulo Khumi (6-22)

    • Anthu anachita mantha paphiri la Sinai (23-33)

  • 6

    • Muzikonda Yehova ndi mtima wanu wonse (1-9)

      • “Tamverani Aisiraeli inu” (4)

      • Makolo aziphunzitsa ana (6, 7)

    • Musaiwale Yehova (10-15)

    • Musamamuyese Yehova (16-19)

    • Mudzafotokozere mʼbadwo wotsatira (20-25)

  • 7

    • Mitundu 7 yoyenera kuwonongedwa (1-6)

    • Chifukwa chimene anasankhira Aisiraeli (7-11)

    • Kumvera kumabweretsa madalitso (12-26)

  • 8

    • Anawauzanso madalitso amene Yehova adzawapatse (1-9)

      • “Munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha” (3)

    • Musaiwale Yehova (10-20)

  • 9

    • Chifukwa chake Aisiraeli anapatsidwa dziko (1-6)

    • Aisiraeli anakwiyitsa Yehova maulendo 4 (7-29)

      • Mwana wa ngʼombe wagolide (7-14)

      • Mose anachonderera Yehova (15-21, 25-29)

      • Anamukwiyitsanso maulendo ena atatu (22)

  • 10

    • Anapanganso miyala yosema iwiri (1-11)

    • Zimene Yehova amafuna (12-22)

      • Muziopa komanso kukonda Yehova (12)

  • 11

    • Mwaona mphamvu za Yehova (1-7)

    • Dziko Lolonjezedwa (8-12)

    • Madalitso amene adzapeze chifukwa chomvera (13-17)

    • Muzisunga mawu a Mulungu mʼmitima yanu (18-25)

    • “Dalitso ndi temberero” (26-32)

  • 12

    • Muzilambira pamalo amene Mulungu anasankha (1-14)

    • Analoledwa kudya nyama koma osati magazi (15-28)

    • Musagwidwe mʼmisampha ya milungu ina (29-32)

  • 13

    • Zoyenera kuchita ndi ampatuko (1-18)

  • 14

    • Zinthu zosayenera kuchita polira maliro (1, 2)

    • Zakudya zodetsedwa komanso zosadetsedwa (3-21)

    • Chakhumi choperekedwa kwa Yehova (22-29)

  • 15

    • Ankakhululukira angongole chaka cha 7 chilichonse (1-6)

    • Kuthandiza osauka (7-11)

    • Akapolo ankamasulidwa chaka cha 7 chilichonse (12-18)

      • Kuboola khutu la kapolo (16, 17)

    • Nyama zoyamba kubadwa zinali zopatulika (19-23)

  • 16

    • Pasika; Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa (1-8)

    • Chikondwerero cha Masabata (9-12)

    • Chikondwerero cha Misasa (13-17)

    • Kusankha oweruza (18-20)

    • Zinthu zosayenera kuzilambira (21, 22)

  • 17

    • Nsembe zizikhala zopanda chilema (1)

    • Zoyenera kuchita ndi ampatuko (2-7)

    • Milandu yovuta kuweruza (8-13)

    • Malangizo oti mafumu azidzatsatira (14-20)

      • Mfumu izikopera buku la Chilamulo (18)

  • 18

    • Zimene ansembe ndi Alevi ankayenera kulandira (1-8)

    • Anawaletsa kuchita zamizimu (9-14)

    • Mneneri ngati Mose (15-19)

    • Mmene tingadziwire aneneri abodza (20-22)

  • 19

    • Mlandu wa magazi komanso mizinda yothawirako (1-13)

    • Zizindikiro za malire sizinkafunika kusunthidwa (14)

    • Anthu operekera umboni mukhoti (15-21)

      • Pankafunika mboni ziwiri kapena zitatu (15)

  • 20

    • Malamulo okhudza nkhondo (1-20)

      • Anthu amene samayenera kupita kunkhondo (5-9)

  • 21

    • Ngati wopha munthu sakudziwika (1-9)

    • Kukwatira akazi ogwidwa kunkhondo (10-14)

    • Ufulu wa mwana woyamba kubadwa (15-17)

    • Mwana wosamvera (18-21)

    • Munthu wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa (22, 23)

  • 22

    • Kulemekeza ziweto za anthu ena (1-4)

    • Kuvala zovala zachimuna kapena zachikazi (5)

    • Kuchitira chifundo ziweto (6, 7)

    • Kampanda kapadenga la nyumba (8)

    • Zinthu zosayenera kuphatikizidwa (9-11)

    • Ulusi wa mʼmphepete mwa zovala (12)

    • Malamulo a milandu yokhudza kugonana (13-30)

  • 23

    • Anthu osayenera kulowa mumpingo wa Mulungu (1-8)

    • Ukhondo mumsasa (9-14)

    • Kapolo amene wathawa kwa mbuye wake (15, 16)

    • Uhule unaletsedwa (17, 18)

    • Chiwongoladzanja komanso malonjezo (19-23)

    • Zimene anthu ongodutsa ankaloledwa kudya (24, 25)

  • 24

    • Ukwati komanso kutha kwa ukwati (1-5)

    • Kulemekeza moyo (6-9)

    • Kuganizira osauka (10-18)

    • Malamulo okhudza kukunkha (19-22)

  • 25

    • Malamulo okhudza kukwapula munthu (1-3)

    • Ngʼombe imene ikupuntha mbewu musamaimange pakamwa (4)

    • Ukwati wapachilamu (5-10)

    • Kugwira malo osayenera pandewu (11, 12)

    • Muyezo woyenera woyezera kulemera komanso kuchuluka kwa zinthu (13-16)

    • Aamaleki ayenera kuwonongedwa (17-19)

  • 26

    • Kupereka zipatso zoyambirira (1-11)

    • Chakhumi chachiwiri (12-15)

    • Aisiraeli anali chuma chapadera kwa Yehova (16-19)

  • 27

    • Akalembe Chilamulo pamiyala (1-10)

    • Paphiri la Ebala ndi paphiri la Gerizimu (11-14)

    • Anatchulanso matemberero (15-26)

  • 28

    • Madalitso chifukwa chomvera (1-14)

    • Matemberero chifukwa chosamvera (15-68)

  • 29

    • Anachita pangano ndi Aisiraeli ku Mowabu (1-13)

    • Anawachenjeza kuti apewe kusamvera (14-29)

      • Zinthu zobisika, zinthu zoululidwa (29)

  • 30

    • Kubwerera kwa Yehova (1-10)

    • Malamulo a Yehova si ovuta kwambiri (11-14)

    • Kusankha moyo kapena imfa (15-20)

  • 31

    • Mose anali atatsala pangʼono kumwalira (1-8)

    • Kuwerenga Chilamulo pamaso pa anthu (9-13)

    • Yoswa anamuika kuti akhale mtsogoleri (14, 15)

    • Ananeneratu kuti Aisiraeli adzapandukira Mulungu (16-30)

      • Nyimbo yoti aphunzitse Aisiraeli (19, 22, 30)

  • 32

    • Nyimbo ya Mose (1-47)

      • Yehova ndi Thanthwe (4)

      • Aisiraeli anaiwala Thanthwe lawo (18)

      • “Kubwezera ndi kwanga” (35)

      • “Inu anthu a mitundu ina, sangalalani limodzi ndi anthu ake” (43)

    • Mose akafera mʼphiri la Nebo (48-52)

  • 33

    • Mose anadalitsa mafuko (1-29)

      • Manja a Yehova “omwe adzakhalapo mpaka kalekale” (27)

  • 34

    • Yehova anaonetsa Mose dziko (1-4)

    • Imfa ya Mose (5-12)