Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Danieli

Machaputala

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12

Mitu

  • 1

    • Yerusalemu anazunguliridwa ndi Ababulo (1, 2)

    • Anyamata amene anatengedwa kupita ku ukapolo analandira maphunziro apadera (3-5)

    • Chikhulupiriro cha Aheberi 4 chinayesedwa (6-21)

  • 2

    • Mfumu Nebukadinezara inalota maloto ochititsa mantha (1-4)

    • Anthu anzeru analephera kumasulira maloto (5-13)

    • Danieli anapempha Mulungu kuti amuthandize (14-18)

    • Anatamanda Mulungu chifukwa anawaululira chinsinsi (19-23)

    • Danieli anauza mfumu maloto ake (24-35)

    • Kumasulira maloto (36-45)

      • Mwala umene ukuimira Ufumu, unaphwanya chifaniziro (44, 45)

    • Danieli analemekezedwa ndi mfumu (46-49)

  • 3

    • Fano lagolide la Mfumu Nebukadinezara (1-7)

      • Analamula kuti aliyense alambire fano (4-6)

    • Aheberi atatu anawaneneza kuti sakumvera (8-18)

      • “Sititumikira milungu yanu” (18)

    • Anaponyedwa mungʼanjo yamoto (19-23)

    • Anapulumutsidwa modabwitsa mungʼanjo yamoto (24-27)

    • Mfumu inalemekeza Mulungu wa Aheberi (28-30)

  • 4

    • Mfumu Nebukadinezara inavomereza kuti Mulungu ndi woyenera kukhala mfumu (1-3)

    • Maloto a mfumu okhudza mtengo (4-18)

      • Padzadutsa nthawi zokwana 7 mtengowo utagwetsedwa (16)

      • Mulungu ndi Wolamulira wa anthu (17)

    • Danieli anamasulira maloto (19-27)

    • Kukwaniritsidwa koyamba pa mfumu (28-36)

      • Mfumu inachita misala kwa nthawi 7 (32, 33)

    • Mfumu inalemekeza Mulungu wakumwamba (37)

  • 5

    • Phwando la Mfumu Belisazara (1-4)

    • Dzanja linalemba pakhoma (5-12)

    • Danieli anapemphedwa kuti amasulire zimene dzanja linalemba (13-25)

    • Kumasulira kwake: Babulo adzagwa (26-31)

  • 6

    • Nduna za Perisiya zinakonzera Danieli chiwembu (1-9)

    • Danieli anapitiriza kupemphera (10-15)

    • Danieli anaponyedwa mʼdzenje la mikango (16-24)

    • Mfumu Dariyo inalemekeza Mulungu wa Danieli (25-28)

  • 7

    • Masomphenya a zilombo 4 (1-8)

      • Nyanga yaingʼono yodzitukumula inamera (8)

    • Wamasiku Ambiri anayamba kuweruza mlandu (9-14)

      • Mwana wa munthu anapatsidwa ufumu (13, 14)

    • Danieli anauzidwa kumasulira kwake (15-28)

      • Zilombo 4 zikuimira mafumu 4 (17)

      • Oyera adzalandira ufumu (18)

      • Padzakhala nyanga kapena kuti mafumu 10 (24)

  • 8

    • Masomphenya a nkhosa yamphongo ndi mbuzi yamphongo (1-14)

      • Nyanga yaingʼono inadzikuza (9-12)

      • Mpaka nsembe za tsiku ndi tsiku zokwana 2,300, zamadzulo ndi zamʼmawa, zitadutsa (14)

    • Gabirieli anamasulira masomphenya (15-27)

      • Tanthauzo la nkhosa yamphongo ndi mbuzi yamphongo (20, 21)

      • Mfumu yooneka mochititsa mantha inayamba kulamulira (23-25)

  • 9

    • Pemphero la Danieli lolapa machimo (1-19)

      • Dziko lidzakhala bwinja kwa zaka 70 (2)

    • Gabirieli anapita kwa Danieli (20-23)

    • Ananeneratu za milungu 70 yaulosi (24-27)

      • Mesiya adzaonekera pambuyo pa milungu 69 (25)

      • Mesiya adzaphedwa (26)

      • Mzinda komanso malo oyera zidzawonongedwa (26)

  • 10

    • Mthenga wochokera kwa Mulungu anapita kwa Danieli (1-21)

      • Mikayeli anathandiza mngelo (13)

  • 11

    • Mafumu a Perisiya ndi Girisi (1-4)

    • Mfumu yakumʼmwera ndi yakumpoto (5-45)

      • Padzakhala wokhometsa msonkho (20)

      • Mtsogoleri wa pangano adzawonongedwa (22)

      • Adzalemekeza mulungu wamʼmalo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri (38)

      • Kukankhana kwa mfumu yakumʼmwera ndi mfumu yakumpoto (40)

      • Malipoti osokoneza ochokera kumʼmawa ndi kumpoto (44)

  • 12

    • “Nthawi yamapeto” mpaka mʼtsogolo (1-13)

      • Mikayeli adzaimirira (1)

      • Anthu ozindikira adzawala kwambiri (3)

      • Anthu adzadziwa zinthu zambiri zoona (4)

      • Danieli adzauka kuti alandire gawo lake (13)