Kalata Yopita kwa Aroma 15:1-33

  • Tizilandirana ngati mmene Khristu anatilandirira (1-13)

  • Paulo, mtumiki wa anthu a mitundu ina (14-21)

  • Maulendo amene Paulo ankafuna kuyenda (22-33)

15  Ife amene tili olimba tiyenera kumaganizira anthu amene ali ndi chikhulupiriro chofooka,+ osati kumangodzikondweretsa tokha.+  Aliyense wa ife aziyesetsa kukondweretsa mnzake ndipo azichita zinthu zomulimbikitsa.+  Chifukwa ngakhale Khristu sankachita zinthu zodzikondweretsa yekha,+ koma anachita zimene Malemba amanena kuti: “Chipongwe cha anthu amene amakunyozani chandigwera.”+  Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.+ Malembawa amatithandiza kupirira+ ndiponso amatilimbikitsa nʼcholinga choti tikhale ndi chiyembekezo.+  Choncho Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amene amatitonthoza, akuthandizeni nonsenu kukhala ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo,  kuti nonse pamodzi ndiponso mogwirizana,+ mulemekeze Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.  Choncho muzilandirana,+ ngati mmene Khristu anatilandirira,+ kuti ulemerero upite kwa Mulungu.  Kunena zoona, Khristu anakhala mtumiki wa anthu odulidwa+ kuti atsimikizire kuti Mulungu ndi wokhulupirika posonyeza kuti malonjezo amene Mulunguyo anapatsa makolo awo ndi otsimikizirika.+  Komanso kuti anthu a mitundu ina alemekeze Mulungu chifukwa cha chifundo chake,+ mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Nʼchifukwa chake ndidzakulemekezani pakati pa mitundu ya anthu ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+ 10  Komanso Malemba amati: “Inu anthu a mitundu ina, kondwerani pamodzi ndi anthu ake.”+ 11  Ndiponso amati: “Tamandani Yehova,* inu mitundu yonse ya anthu ndipo anthu onse amutamande.”+ 12  Komanso Yesaya anati: “Padzakhala muzu wa Jese,+ winawake amene adzatuluke kuti alamulire mitundu.+ Chiyembekezo cha anthu a mitundu ina chidzakhala pa iyeyo.”+ 13  Mulungu amene amapereka chiyembekezo akuthandizeni kukhala osangalala kwambiri komanso kukhala ndi mtendere wonse pamene mukumukhulupirira, kuti mukhale ndi chiyembekezo champhamvu mothandizidwa ndi mzimu woyera.+ 14  Abale anga, ine sindikukayikira kuti ndinu okonzeka kuchita zabwino, mukudziwa zambiri komanso mukhoza kulangizana. 15  Komabe, ndakulemberani mfundo zina mosapita mʼmbali kuti ndikukumbutseninso. Ndachita zimenezi chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wandisonyeza. 16  Anandisonyeza kukoma mtima kumeneku kuti ndigwire ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu monga wantchito wa Khristu Yesu, wotumikira anthu a mitundu ina.+ Ndikugwira ntchito yopatulikayi kuti anthu a mitundu inawa akhale ngati nsembe yovomerezeka kwa Mulungu+ imene yayeretsedwa ndi mzimu woyera. 17  Choncho ndikusangalala kukhala wotsatira wa Khristu Yesu komanso kugwira ntchito ya Mulungu. 18  Sindidzalankhula chilichonse chimene ndachita pandekha, koma zokhazo zimene Khristu wachita ndi kulankhula kudzera mwa ine kuti ndithandize anthu a mitundu ina kukhala omvera. 19  Iwo akhala omvera chifukwa cha zodabwitsa zamphamvu ndiponso zizindikiro+ zimene mzimu wa Mulungu wachita. Choncho ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu kuyambira ku Yerusalemu mpaka ku Iluriko.+ 20  Pochita zimenezi ndinatsimikiza mtima kuti ndisalengeze uthenga wabwino kumene anthu ankadziwa kale za Khristu nʼcholinga choti ndisamange pamaziko a munthu wina, 21  koma ndichite mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Amene sanauzidwepo za iye adzamuona, ndipo amene sanamve adzazindikira.”+ 22  Nʼchifukwa chakenso ndakhala ndikulephera kubwera kwa inu. 23  Koma tsopano kulibenso gawo limene sindinafikeko mʼmadera amenewa, ndipo kwa zaka zambiri* ndakhala ndikulakalaka kufika kwanuko. 24  Choncho ndili ndi chikhulupiriro kuti ndikamadzapita ku Sipaniya ndidzaonana nanu ndipo ndikadzacheza nanu kwakanthawi, mudzandiperekeza pa ulendo wangawo. 25  Koma panopa ndatsala pangʼono kupita ku Yerusalemu kukatumikira oyera.+ 26  Abale a ku Makedoniya ndi a ku Akaya apereka mosangalala mphatso kwa oyera ena a ku Yerusalemu omwe ndi osauka.+ 27  Nʼzoona kuti achita zimenezo mwa kufuna kwawo, komabe iwo anali ndi ngongole kwa oyerawo. Chifukwa ngati anthu a mitundu ina alandirako zinthu zauzimu kuchokera kwa oyerawo, ndiye kuti nawonso ayenera kutumikira oyerawo powapatsa zinthu zofunika pa moyo.+ 28  Choncho ndikakamaliza kuwapatsa zoperekazi, ndidzadzera kwanuko popita ku Sipaniya. 29  Komanso ndikudziwa kuti ndikadzafika kwanuko ndidzafika ndi madalitso ambiri ochokera kwa Khristu. 30  Choncho abale, ndikukupemphani kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu komanso chikondi cha mzimu, kuti muzilimbikira kundipempherera kwa Mulungu ndipo nanenso ndikulimbikira kupemphera.+ 31  Tilimbikire kupemphera kuti ndikapulumutsidwe+ kwa anthu osakhulupirira a ku Yudeya ndiponso kuti oyera a ku Yerusalemu akalandire bwino mphatso imene ndatenga.+ 32  Ngati Mulungu angalole, ndidzabwera kwa inu mosangalala ndipo tidzalimbikitsana. 33  Mulungu amene amapereka mtendere akhale ndi nonsenu.+ Ame.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “zingapo.”