Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la 1 Mafumu

Machaputala

Mitu

  • 1

    • Davide ndi Abisagi (1-4)

    • Adoniya ankafuna kukhala mfumu (5-10)

    • Zimene anachita Natani ndi Bati-seba (11-27)

    • Davide analamula kuti Solomo adzozedwe kukhala mfumu (28-40)

    • Adoniya anathawira kuguwa la nsembe (41-53)

  • 2

    • Davide analangiza Solomo (1-9)

    • Davide anamwalira; Solomo anakhala mfumu (10-12)

    • Zimene Adoniya anachita zinamuphetsa (13-25)

    • Abiyatara anathamangitsidwa; Yowabu anaphedwa (26-35)

    • Simeyi anaphedwa (36-46)

  • 3

    • Solomo anakwatira mwana wa Farao (1-3)

    • Yehova anaonekera kwa Solomo mʼmaloto (4-15)

      • Solomo anapempha nzeru (7-9)

    • Solomo anaweruza azimayi awiri (16-28)

  • 4

    • Ulamuliro wa Solomo (1-19)

    • Zinthu zinkayenda bwino mu ulamuliro wa Solomo (20-28)

      • Aliyense anali wotetezeka pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi wa mkuyu (25)

    • Nzeru za Solomo ndi miyambi yake (29-34)

  • 5

    • Mfumu Hiramu anapereka zipangizo zomangira (1-12)

    • Antchito yokakamiza a Solomo (13-18)

  • 6

    • Solomo anamanga kachisi (1-38)

      • Chipinda chamkati (19-22)

      • Akerubi (23-28)

      • Zogoba, zitseko, bwalo lamkati (29-36)

      • Anamanga kachisi zaka pafupifupi 7 (37, 38)

  • 7

    • Nyumba yachifumu ya Solomo (1-12)

    • Hiramu waluso anathandiza Solomo (13-47)

      • Zipilala ziwiri zakopa (15-22)

      • Thanki yosungira madzi (23-26)

      • Zotengera 10 zakopa (27-39)

    • Anamaliza kupanga zinthu zagolide (48-51)

  • 8

    • Anabweretsa Likasa mʼkachisi (1-13)

    • Solomo analankhula ndi anthu (14-21)

    • Pemphero la Solomo lotsegulira kachisi (22-53)

    • Solomo anadalitsa anthu (54-61)

    • Nsembe ndi chikondwerero chotsegulira kachisi (62-66)

  • 9

    • Yehova anaonekeranso kwa Solomo (1-9)

    • Mphatso zimene Solomo anapatsa Hiramu (10-14)

    • Zinthu zimene Solomo anamanga (15-28)

  • 10

    • Mfumukazi ya ku Sheba inakaona Solomo (1-13)

    • Chuma chambiri cha Solomo (14-29)

  • 11

    • Akazi a Solomo anapotoza mtima wake (1-13)

    • Anthu amene ankalimbana ndi Solomo (14-25)

    • Yerobowamu analonjezedwa mafuko (26-40)

    • Solomo anamwalira; Rehobowamu anakhala mfumu (41-43)

  • 12

    • Rehobowamu sanayankhe bwino anthu (1-15)

    • Mafuko 10 anagalukira Solomo (16-19)

    • Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli (20)

    • Rehobowamu anamuletsa kuti asakamenyane ndi Aisiraeli (21-24)

    • Yerobowamu anayamba kulambira mwana wa ngʼombe (25-33)

  • 13

    • Ulosi wonena za guwa la ku Beteli (1-10)

      • Guwa linagumuka (5)

    • Munthu wa Mulungu sanamvere (11-34)

  • 14

    • Ulosi wa Ahiya wotsutsa Yerobowamu (1-20)

    • Rehobowamu anayamba kulamulira ku Yuda (21-31)

      • Sisaki anaukira Yerusalemu (25, 26)

  • 15

    • Abiyamu, mfumu ya Yuda (1-8)

    • Asa, mfumu ya Yuda (9-24)

    • Nadabu, mfumu ya Isiraeli (25-32)

    • Basa, mfumu ya Isiraeli (33, 34)

  • 16

    • Yehova anaweruza Basa (1-7)

    • Ela, mfumu ya Isiraeli (8-14)

    • Zimiri, mfumu ya Isiraeli (15-20)

    • Omuri, mfumu ya Isiraeli (21-28)

    • Ahabu, mfumu ya Isiraeli (29-33)

    • Hiyeli anamanganso Yeriko (34)

  • 17

    • Mneneri Eliya analosera chilala (1)

    • Akhwangwala ankabweretsera Eliya chakudya (2-7)

    • Eliya anapita kwa mkazi wamasiye wa ku Zarefati (8-16)

    • Mwana wa mkazi wamasiye anamwalira nʼkuukitsidwa (17-24)

  • 18

    • Eliya anakumana ndi Obadiya ndi Ahabu (1-18)

    • Eliya ndi aneneri a Baala paphiri la Karimeli (19-40)

      • ‘Mukayikakayika mpaka liti?’ (21)

    • Chilala cha zaka zitatu ndi hafu chinatha (41-46)

  • 19

    • Eliya anathawa Yezebeli (1-8)

    • Yehova anaonekera kwa Eliya ku Horebe (9-14)

    • Eliya anadzoza Hazaeli, Yehu ndi Elisa (15-18)

    • Elisa anadzozedwa kuti alowe mʼmalo mwa Eliya (19-21)

  • 20

    • Asiriya anamenyana ndi Ahabu (1-12)

    • Ahabu anagonjetsa Asiriya (13-34)

    • Ulosi wotsutsana ndi Ahabu (35-43)

  • 21

    • Ahabu anasirira munda wa Naboti (1-4)

    • Yezebeli anakonza zoti Naboti aphedwe (5-16)

    • Uthenga wa Eliya wotsutsa Ahabu (17-26)

    • Ahabu anadzichepetsa (27-29)

  • 22

    • Yehosafati anachita mgwirizano ndi Ahabu (1-12)

    • Mikaya analosera kuti Ahabu agonjetsedwa (13-28)

      • Mzimu wabodza unapusitsa Ahabu (21, 22)

    • Ahabu anaphedwa ku Ramoti-giliyadi (29-40)

    • Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda (41-50)

    • Ahaziya mfumu ya Isiraeli (51-53)