Pitani ku nkhani yake

Mfundo zothandiza mabanja

Pagawoli pali nkhani zosiyanasiyana zokhala ndi malangizo ochokera m’Baibulo othandiza mabanja.  a Kuti muone mndandanda wa nkhani zosiyanasiyana zothandiza mabanja, pitani pagawo lakuti Anthu Okwatirana Komanso Mabanja.

a Mayina a anthu ena omwe atchulidwa munkhanizi asinthidwa.

Banja

Muziona Moyenera Zinthu Zimene Zimakukwiyitsani

M’malo molowa kuti zinthu zimene zimakukwiyitsani zisokoneze banja lanu, muziyesetsa kuona zinthuzo moyenera.

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Woleza Mtima?

Anthu awiri opanda ungwiro akakwatirana, amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Kuleza mtima n’kofunika kwambiri kuti banja likhale lolimba.

Mungatani Kuti Banja Lanu Lizisangalala: Muzisonyezana Ulemu

Baibulo lingakuthandizeni kuti muyambe kulemekezana m’banja lanu ngakhale kuti poyamba simunkalemekezana.

Kodi Mungasonyezane Bwanji Ulemu?

Anthu okwatirana ayenera kusonyezana ulemu nthawi zonse. Koma kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza mwamuna kapena mkazi wanu?

Kodi Mungasonyeze Bwanji kuti Mumayamikira Zimene Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Amachita?

Mwamuna ndi mkazi akamayesetsa kuona zabwino zimene mnzawo amachita, nthawi zambiri chikondi chawo chimakula. N’chiyani chingakuthandizeni kuti muziyamikira mwamuna kapena mkazi wanu?

Kuti Mukhale Ndi Banja Losangalala: Muzisonyezana Chikondi

Kugwira ntchito, kupanikizika maganizo komanso zochitika za tsiku ndi tsiku zingachititse anthu okwatirana kuti azilephera kusonyezana chikondi. Kodi ndi zotheka kubwezeretsa chikondi m’banja mwanu?

Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Mumakonda Mwamuna Kapena Mkazi Wanu?

Kodi anthu okwatirana angasonyeze bwanji kuti amakondana? Werengani nkhaniyi ndi kupeza mfundo 4 zochokera m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni pa nkhaniyi.

Mungatani Kuti Mukwaniritse Lonjezo Lanu?

Kodi mumaona kuti lonjezo laukwati lili ngati goli loti simungathe kuchokamonso kapena mumaona kuti lili ngati nangula?

Zimene Mungachite Kuti Musamagwire Ntchito Pamene Simuli Kuntchito

Mfundo 5 zimene zingakuthandizeni kuti ntchito yanu isamasokoneze banja lanu.

Kodi Mungatani Kuti Musamawononge Ndalama Zambiri?

Musadikire mpaka ndalama zanu kutha musanayambe kuganizira njira yoyenera yogwiritsira ntchito ndalama. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti muzigwiritsa ntchito ndalama mosamala.

Mungatani Kuti Muzigwirizana Ndi Apongozi Anu?

Mfundo zitatu zomwe zingakuthandizeni kuti nkhani zokhudza apongozi zisasokoneze banja lanu.

Zimene Mungachite Ngati Mumaona Zinthu Mosiyana

Kodi anthu okwatirana angatani kuti athetse kusamvana popanda kukangana?

Zimene Mungachite Ngati Mumakonda Zosiyana

Kodi mumaona kuti ndinu wosiyana kwambiri ndi mwamuna kapena mkazi wanu?

Kodi Mungatani Kuti Musamasunge Chakukhosi?

Kodi kukhululuka kumatanthauza kuti mukuchepetsa vutolo kapena mukuona kuti silinachitike n’komwe?

Mungatani Kuti Musamakwiye Mopitirira Malire?

Mukamangokhalira kukwiya kapena kubisa mmene mukumvera, mukhoza kuika moyo wanu pangozi. Kodi mungachite zotani ngati mwamuna kapena mkazi wanu wakukhumudwitsani?

Ana Akakula N’kuchoka Pakhomo

Okwatirana ena amakumana ndi mavuto aakulu ana awo akakula n’kuchoka pakhomo. Kodi makolo ayenera kuchita chiyani kuti azolowerenso kukhala okha?

Zimene Mungachite Ngati Mumacheza Kwambiri ndi Munthu Amene si Mwamuna Kapena Mkazi Wanu

Mukamacheza kwambiri ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu, kodi mumaona kuti palibe vuto lina lililonse? Ngati mumaona choncho, werengani nkhaniyi kuti muone mfundo za m’Baibulo zosonyeza kuti maganizo amenewo ndi oopsa.

Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino

Kodi simukondananso ndi mwamuna kapena mkazi wanu ndipo mumangomuona ngati munthu wokhala naye nyumba imodzi basi? Mfundo 5 zimene zingathandize kuti banja lanu liziyenda bwino.

Mungatani Kuti Mupewe Kuthetsa Banja Pambuyo Pokhala Limodzi kwa Zaka Zambiri?

N’chiyani chikuchititsa kuti anthu azithetsa banja pambuyo pokhala limodzi kwa zaka zambiri? Kodi mungatani kuti zimenezi zisakuchitikireni?

Kodi Mungatani Kuti Musamachitirane Nsanje M’banja?

Banja silingayende bwino ngati mwamuna ndi mkazi wake amakayikirana. Ndiye kodi mungatani kuti musamachitirane nsanje pa zifukwa zosamveka?

Kuonera Zolaula Kungasokoneze Banja Lanu

Nkhaniyi ili malangizo amene angakuthandizeni kuti musiye chizolowezi choonera zolaula komanso kukonza ubale wanu ndi mwamuna kapena mkazi wanu.

Kodi Tiyambe Kukhala Limodzi Tisanakwatirane?

Anthu ena amaganiza kuti kuyamba kukhala limodzi kaye asanakwatirane kungawathandize kukonzekera banja. Kodi amenewa ndi maganizo abwino kapena pali njira ina yabwino?

Kulankhulana

Kodi Mungatani Kuti Zipangizo Zamakono Zisamakusokonezeni?

Zipangizo zamakono zikhoza kulimbitsa kapena kusokoneza banja lanu. Kodi zimenezi zingachitike bwanji?

Mungatani Kuti Musamakangane Pokambirana Mavuto Anu?

Amuna ndi akazi amafotokoza maganizo awo mosiyana. Kudziwa mfundoyi kungakuthandizeni kuti musamakangane.

Kodi Mungatani Kuti Muzimvetsera Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akamalankhula?

Kumvetsera mwatcheru si luso chabe koma ndi njiranso yosonyezera kuti mnzanuyo mumamukonda. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti muzimvetsera mwamuna kapena mkazi wanu akamalankhula.

Kodi Mungatani Kuti Muzilolerana M’banja?

Mfundo 4 zomwe zingakuthandizeni kuti musamangokangana koma muzipeza njira zothetsera mavuto.

Zimene Mwamuna ndi Mkazi Angachite Kuti Asamasiye Kulankhulana Akasemphana Maganizo

Kodi chimachititsa n’chiyani kuti mwamuna ndi mkazi wake asiye kulankhulana, nanga n’chiyani chingathandize kuti athetse kusamvana?

Zimene Mungachite Kuti Musamakangane

Kodi simuchedwa kukangana ndi mwamuna kapena mkazi wanu? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zimene zingathandize banja lanu.

Kodi Mungapewe Bwanji Kulankhula Mawu Achipongwe?

Kodi mungatani ngati banja lanu lasokonekera chifukwa choti inuyo ndi mkazi kapena mwamuna wanu mumakonda kulankhulana mawu achipongwe?

Kodi Mungatani Ngati Zimakuvutani Kupepesa?

Kodi ndiyenera kupepesabe ngakhale kuti wolakwa si ine?

Kodi Mungatani Kuti Muzikhululukirana?

N’chifukwa chiyani kukhululukirana sikophweka? Werengani nkhani kuti muone mmene Baibulo lingakuthandizireni.

Kulera Ana

Zimene Mungachite Kuti Mukhale Bambo Wabwino

Zimene mukuchita panopa monga mwamuna zimasonyeza kuti mudzakhala bambo wotani mwana wanu akadzabadwa.

Zimene Makolo Ayenera Kudziwa Zokhudza Kutumiza Mwana Kumalo Osamalira Ana Masana

Dzifunseni mafunso 4 kuti mudziwe ngati kutumiza mwana wanu kumalo osamalira ana kungathandize mwanayo.

Kodi Mwana Wanga Akhale ndi Foni?

Dzifunseni mafunso awa kuti mudziwe ngati inuyo ndi mwana wanu muli okonzeka.

Phunzitsani Ana Anu Kugwiritsa Ntchito Foni Mosamala

Ngakhale ana amene amadziwa bwino kugwiritsa ntchito foni amafunika kuphunzitsidwa mmene angaigwiritsire ntchito mosamala.

N’chifukwa Chiyani Kuwerenga ndi Kofunika Kwambiri kwa Ana?​—Mbali Yoyamba: Kodi Zomwe Zingawathandize Ndi Zowerenga Kapena Zoonera?

Ana ambiri amakonda kuonera mavidiyo. Kodi makolo angalimbikitse bwanji ana kuti azikonda kwambiri kuwerenga?

Mmene Mungathandizire Ana Anu kuti Asasokonezeke Ndi Nkhani Zoopsa

Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti asasokonezeke ndi nkhani zoopsa?

Kodi Mungayankhe Bwanji Mwana Wanu Atakufunsani za Imfa?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu 4 zimene mungachite pothandiza mwana wanu kudziwa zokhudza imfa komanso mmene mungamuthandizire kupirira wachibale akamwalira.

Ndingatani Ngati Mwana Wanga Akumaboweka?

Ngati mwana wanu ali pakhomo ndipo akusowa zochita, mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita.

Ubwino wa Masewera Othandiza Kuganiza

N’zothandiza kwambiri poyerekezera ndi masewera a pazipangizo zamakono kapena ochita kukonzedweratu.

Kodi Kuphunzitsa Ana Ntchito Zapakhomo N’kothandiza Bwanji?

Kodi makolo zimakuvutani kuphunzitsa ana anu ntchito zapakhomo? Ngati ndi choncho, werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene kupatsa ana ntchitozi kumawathandizira kudziwa udindo wawo komanso kukhala osangalala.

Mmene Mungathandizire Ana Anu Akamalephera Zinazake

Kulakwa si nkhani yachilendo. Muziwathandiza kuti asamabise zomwe zachitikazo komanso kuti asamadzione kuti ndi olephera.

Mungathandize Bwanji Mwana Wanu Kuti Azikhoza Bwino Kusukulu?

Werengani nkhaniyi kuti muone zimene zingakuthandizeni kudziwa vuto lomwe likuchititsa mwana wanu kuti asamakhoze bwino komanso mmene mungamuthandizire.

Kodi Ndingatani Ngati Nditamva Kuti Mwana Wanga Amavutitsidwa ndi Anzake?

Werengani nkhaniyi kuti mupeze mfundo 4 zomwe zingamuthandize kudziwa zoyenera kuchita akamavutitsidwa.

Muziyamikira Ana Anu

Kuyamikira mwana akachita khama n’kothandiza kwambiri.

Mmene Kutha Kwa Banja Kumakhudzira Ana

Ngakhale kuti anthu ena amaganiza kuti kuthetsa banja kungathandize ana, kafukufuku akusonyeza kuti zimenezi zimabweretsa mavuto ambiri kwa anawo.

Zimene Mungachite Mwana Akatsala Pang’ono Kutha Msinkhu

Mfundo 5 za m’Baibulo zomwe zingathandize makolo panthawi imene mwana wawo akukumana ndi mavuto chifukwa cha kusintha kwa thupi lake.

Kuphunzitsa Mwana Wanu Nkhani Zokhudza Kugonana

Masiku ano ana akumaona ndiponso kumva zinthu zokhudza kugonana ali aang’ono kwambiri. Kodi muyenera kudziwa zotani? Kodi mungachite chiyani kuti muziteteza ana anu?

Mmene Mungathandizire Ana Anu pa Nkhani ya Mowa

Kodi ndi liti pamene makolo angayambe kukambirana ndi ana awo zokhudza mowa ndipo angakambirane nawo bwanji?

Mmene Mungauzire Mwana Wanu za Kuipa Kosankhana Mitundu

Mukamaphunzitsa mwana wanu za kuipa kosankhana mitundu mogwirizana ndi msinkhu wake, mudzamuthandiza kuti asatengere maganizo olakwika omwe anthu ambiri ali nawo.

Phunzitsani Ana Anu Kuti Akhale Odziletsa

Kupatsa ana anu chilichonse chimene akufuna kungawalepheretse kuphunzira makhalidwe ofunika.

Mungaphunzitse Bwanji Ana Anu Kukhala Odzichepetsa?

Muziphunzitsa mwana kukhala wodzichepetsa popanda kum’pangitsa kudziona ngati wachabechabe.

Muziphunzitsa Ana Anu Kukhala ndi Mtima Woyamikira

Ngakhale ana aang’ono akhoza kuphunzira kunena kuti zikomo munthu wina akawachitira zabwino.

Mungaphunzitse Bwanji Mwana Wanu Kuti Azikumverani?

Kodi inuyo simugwirizana ndi mwana wanu ndipo nthawi zambiri mumangochita zomwe mwanayo akufuna? M’nkhaniyi muli mfundo 5 zomwe zingathandize makolo kulera bwino ana awo.

Kodi Mungatani Kuti Musamangopatsa Mwana Wanu Chilichonse Chimene Akufuna?

Mungatani ngati mwakaniza mwana wanu zinazake, iye n’kuyamba kuvuta kapena kuchonderera pofuna kudziwa ngati mwatsimikizadi?

Zimene Mungachite Mwana Akayamba Kuvuta

Kodi mungachite chiyani mwana wanu atayamba kuvuta? Baibulo lili ndi malangizo omwe angakuthandizeni kuthana ndi vuto limeneli.

Zimene Mungachite Ngati Mwana Wanu Amanama

Kodi mungatani ngati mwana wanu wanama? Nkhaniyi ikufotokoza malangizo a m’Baibulo amene angakuthandizeni kuphunzitsa mwana wanu kufunika kunena zoona.

Kulera Ana Achinyamata

Zimene Mungachite Kuti Muzimasukirana ndi Mwana Wanu

Kodi mumakhumudwa kwambiri chifukwa cholephera kulankhulana bwino ndi mwana wanu? Kodi n’chiyani chimene chimachititsa kuti muzivutika kulankhulana naye?

Ngati Mwana Wanu Wamkazi Akuvutika Maganizo

Atsikana ambiri amavutika ndi zimene zimachitika akamakula. Kodi makolo angawathandize bwanji akamavutika maganizo chifukwa cha zimenezi?

Mwana Wanu Wachinyamata Akachita Zinthu Zokuchititsani Kusiya Kumukhulupirira

Musafulumire kuganiza kuti mwana wanu wachinyamata waganiza zoti asamakumvereni. Mukhoza kumuthandiza kuti ayambirenso kuchita zinthu mokhulupirika.

Mmene Mungalangizire Ana Anu

N’chifukwa chiyani zimakhala zosavuta kuti ana azigwirizana kwambiri ndi anzawo kuposa makolo awo?

Zimene Mungachite Kuti Mwana Wanu Azikumverani

Cholinga cha chilango ndi kuphunzitsa. Mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kuti muphunzitse mwana wanu kumvera.

Khazikitsani Malamulo oti Mwana Wanu Azitsatira

Kodi mungatani ngati mwana wanu wachinyamata sasangalala ndi malamulo amene munakhazikitsa?

Phunzitsani Ana Anu Kuti Azigwiritsa Ntchito Intaneti Moyenera

Kodi mungatani kuti musamangoikira mwana wanu malamulo koma muzimuphunzitsa kuti azitha kusankha zinthu mwanzeru?

Kodi Mwana Wanga Azigwiritsa Ntchito Intaneti?

Mafunso 4 omwe angakuthandizeni kusankha zoti muchite.

Kukambirana ndi Mwana Wanu Nkhani Yotumizirana Zinthu Zolaula Pafoni

Musachite kudikira kuti mpaka mwana wanu akumane ndi vuto linalake chifukwa chakuti sanagwiritse ntchito bwino foni yake. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti mukambirane ndi mwana wanu kuopsa kotumizirana zinthu zolaula.

Mmene Mungathandizire Mwana Wanu Amene Amadzivulaza Mwadala

Achinyamata ena amadzivulaza mwadala. N’chiyani chimawachititsa kuti azichita zimenezi? Kodi mungamuthandize bwanji mwana wanu ngati amadzivulaza mwadala?

Achinyamata

Kodi Mungatani Kuti Musamangotengera Zochita za Anzanu?

Munthu akhoza kuyamba kuchita zoipa chifukwa chotengera zochita za anzake. Zimene muyenera kudziwa zokhudza kutengera zochita za anzanu komanso zimene mungachite pothetsa vutoli.

Kodi Mumatani Wina Akakupatsani Malangizo pa Zomwe Mwalakwitsa?

Kodi zingatheke bwanji kuti malangizo owawa kwambiri akhale othandiza kwambiri?

Kodi Mungasonyeze Bwanji Khalidwe Labwino Mukamatumiza ndi Kulandira Mameseji pa Foni?

Kodi mukuona kuti n’kupanda ulemu kusiya kaye kucheza ndi mnzanu kuti muwerenge meseji? Kapena mukuganiza si bwino kumangopitirizabe kucheza ndi mnzanuyo osawerenga kaye meseji imene mwalandira?

Mungatani Kuti Musamagonje Mukakumana ndi Mayesero?

Mwamuna komanso mkazi weniweni amatha kupewa mayesero. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu 6 zimene zingakuthandizeni kusagonja mukamayesedwa komanso kuti musakhale ndi nkhawa chifukwa chodziwa kuti mwagonja.

Kodi Mungatani Kuti Muziugwira Mtima?

Mfundo 5 zokuthandizani kuti muziugwira mtima.

Kodi Mungatani Ngati Mumasowa Wocheza Naye

Kusowa ocheza nawo kwa nthawi yaitali kumasokoneza thanzi la munthu mofanana ndi mmene zimakhalira ndi munthu yemwe amasuta ndudu 15 pa tsiku. Kodi mungatani ngati nthawi zina mumaona kuti mumangokhala nokhanokha ndipo mukusowa wocheza naye?

Kodi Mungatani Ngati Chibwenzi Chatha?

N’chiyani chingakuthandizeni ngati chibwenzi chanu chatha?

Kodi Mukufuna Kubwereranso Kunyumba?

Kodi zinthu zakuvutani ndipo mukuona kuti mukufunikanso kubwerera kwanu? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zomwe zingakuthandizeni kuti zinthu ziyambenso kukuyenderani bwino.

Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Anzanu Apamtima?

Mfundo 4 zomwe zingakuthandizeni kuti mupeze anzanu apamtima.

Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha

Zinthu zimasintha pamoyo. Onani zimene ena achita kuti azolowere zinthu zitawasinthira.

Mungatani Ngati Muli ndi Chisoni Chifukwa cha Imfa ya Bambo Kapena Mayi Anu?

Zimakhala zothetsa nzeru kwambiri bambo kapena mayi ako akamwalira. Kodi wachinyamata amene bambo kapena mayi anamwalira, angatani ngati ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya kholo lakelo?

Kodi Mumakonda Masewera Oika Moyo Pangozi?

Achinyamata ambiri amafuna kudziwa ngati angakwanitse kuchita masewera enaake ngakhale kuti nthawi zina zingaike moyo wawo pangozi. Kodi nanunso zimenezi zimakuchitikirani?